Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 12:46 - Buku Lopatulika

46 Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Pa nthaŵi ya Davide ndi Asafu, panali mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo, ndiponso panali nyimbo zotamanda ndi zothokoza Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Pakuti kalekale, pa nthawi ya Davide ndi Asafu, panali atsogoleri a anthu oyimba nyimbo za matamando ndi nyimbo zoyamika Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:46
7 Mawu Ofanana  

Ndipo awa ndi oimba, akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.


Hezekiya mfumu ndi akalonga nauzanso Alevi aimbire Yehova zomlemekeza ndi mau a Davide ndi a Asafu mlauli. Ndipo anaimbira zomlemekeza mokondwera, nawerama mitu yao, nalambira.


ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.


Tidati, Tidzaimba bwanji nyimbo ya Yehova m'dziko lachilendo?


Indedi Mulungu achitira Israele zabwino, iwo a mtima wa mbee.


Mulungu musakhale chete; musakhale duu, osanena kanthu, Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa