2 Mbiri 7:6 - Buku Lopatulika6 Naimirira ansembe mu udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Naimirira ansembe m'udikiro wao; ndi Alevi omwe ndi zoimbira za Yehova, adazipanga Davide mfumu kuyamika nazo Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire, polemekeza Davide mwa utumiki wao; ndi ansembe anaomba malipenga pamaso pao, nakhala chilili Israele yense. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Ansembe adaimirira m'malo mwao, pamene Alevi ankatamanda Chauta poimba nyimbo zothokoza Chauta ndi zipangizo zimene Davide adapanga, pakuti chikondi cha Mulungu chimakhala mpaka muyaya. Anthu onseŵa ankatero nthaŵi zonse Davide akamapereka matamando kudzera mwa iwo. Poyang'anana ndi iwowo panali ansembe oliza malipenga. Ndipo Aisraele onse adaakhala chilili. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira. Onani mutuwo |
Ndipo kunali, pakuchita limodzi amalipenga ndi oimba, kumveketsa mau amodzi akulemekeza ndi kuyamika Yehova, ndi pakukweza mau ao pamodzi ndi malipenga, ndi nsanje, ndi zoimbira zina, ndi kulemekeza Yehova, ndi kuti, Pakuti Iye ndiye wabwino, pakuti chifundo chake chikhala chikhalire; pamenepo mtambo unadzaza nyumbayi, ndiyo nyumba ya Yehova;