Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 11:17 - Buku Lopatulika

17 ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mataniyo, mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, amene anali mtsogoleri pa mapemphero achiyamiko m'Nyumba ya Mulungu, ndiponso Bakibukiya, amene anali wachiŵiri pakati pa abale ake. Panalinso Abida, mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu ndiye anali wotsogolera pa mapemphero achiyamiko. Panalinso Bakibukiya amene anali wachiwiri pakati pa abale ake. Kuwonjezera apo panalinso Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 11:17
15 Mawu Ofanana  

Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.


Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israele.


ndi pamodzi nao Hemani, ndi Yedutuni, ndi osankhika otsalawo, otchulidwa maina, kuyamika Yehova; pakuti chifundo chake nchosatha;


ndi Bakibakara, Heresi, ndi Galali, ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu;


Zakuri, Serebiya, Sebaniya,


ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu;


Alevi onse m'mzinda wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai.


Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.


Mataniya, ndi Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni, Akubu, ndiwo odikira akulonda pa nyumba za chuma zili kuzipata.


Pamenepo ndinakwera nao akulu a Yuda pa lingali, ndinaikanso oyamikira magulu awiri akulu oyenda molongosoka; lina loyenda ku dzanja lamanja palinga kunka ku Chipata cha Kudzala;


Pakuti m'masiku a Davide ndi Asafu kalelo kunali mkulu wa oimbira, ndi wa nyimbo zolemekeza ndi zoyamikira Mulungu.


Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa