Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 12:8 - Buku Lopatulika

8 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndi Alevi ndiwo Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya, Yuda, ndi Mataniya; iye ndi abale ake amatsogolera mayamiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Alevi anali aŵa: Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya ndi Yuda. Panalinso Mataniya, amene ankayang'anira za maimbidwe a nyimbo zachiyamiko, pamodzi ndi anzakewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Alevi anali Yesuwa, Binuyi, Kadimieli, Serebiya, Yuda, ndiponso Mataniya, amene pamodzi ndi abale ake ankatsogolera nyimbo za mayamiko.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 12:8
12 Mawu Ofanana  

Ndipo awa ndi oimba, akulu a nyumba za makolo a Alevi, okhala m'zipinda, omasuka ku ntchito zina; pakuti anali nayo ntchito yao usana ndi usiku.


Alevi: ana a Yesuwa, ndi Kadimiyele, ndiwo a ana a Hodaviya, makumi asanu ndi awiri mphambu anai.


Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.


ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.


Ndipo woyang'anira wa Alevi mu Yerusalemu ndiye Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika; mwa ana a Asafu oimbira ena anayang'anira ntchito ya m'nyumba ya Mulungu.


Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.


Salu, Amoki, Hilikiya, Yedaya. Awa ndi akulu a ansembe ndi abale ao m'masiku a Yesuwa.


Ndi Bakibukiya ndi Uni, abale ao, anawayang'anira maulonda.


A Levi: ana a Yesuwa, a Kadimiyele, a ana a Hodeva, makumi asanu ndi awiri kudza anai.


ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Salimai,


Pamenepo anaimirira pa chiunda cha Alevi Yesuwa, ndi Bani, Kadimiyele, Sebaniya, Buni, Serebiya, Bani, ndi Kenani, nafuula ndi mau aakulu kwa Yehova Mulungu wao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa