Masalimo 7:17 - Buku Lopatulika17 Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Ndidzayamika Yehova monga mwa chilungamo chake; ndipo ndidzaimbira Yehova Wam'mwambamwamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Ine ndidzathokoza Chauta chifukwa cha kulungama kwake, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta, Wopambanazonse uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake; ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.