Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Timoteyo 3:13 - Buku Lopatulika

13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Pakuti iwo akutumikira bwino adzitengera okha mbiri yabwino, ndi kulimbika kwakukulu m'chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu.

Onani mutuwo Koperani




1 Timoteyo 3:13
17 Mawu Ofanana  

monga Mwana wa Munthu sanadze kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo wake dipo la anthu ambiri.


Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.


Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi.


Ndipo pamene anafika pamakwerero, kudatero kuti anamsenza asilikali chifukwa cha kulimbalimba kwa khamulo;


Ndipo anampenyetsetsa onse akukhala m'bwalo la akulu a milandu, naona nkhope yake ngati nkhope ya mngelo.


Ndipo mau amene anakonda unyinji wonse; ndipo anasankha Stefano, ndiye munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi Mzimu Woyera, ndi Filipo, ndi Prokoro, ndi Nikanore ndi Timoni, ndi Parmenasi, ndi Nikolasi, ndiye wopinduka wa ku Antiokeya:


Ndipo Stefano, wodzala ndi chisomo ndi mphamvu, anachita zozizwa ndi zizindikiro zazikulu mwa anthu.


Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),


ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.


koma tingakhale tidamva zowawa kale, ndipo anatichitira chipongwe, monga mudziwa, ku Filipi, tinalimbika pakamwa mwa Mulungu wathu kulankhula ndi inu Uthenga Wabwino wa Mulungu m'kutsutsana kwambiri.


Izi ndikulembera ndi kuyembekeza kudza kwa iwe posachedwa, koma ngati ndichedwa,


Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'chisomo cha mwa Khristu Yesu.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa