Mayeso ndi nthawi imene timakopeka kuchita zinthu zosakondweretsa Mulungu (zoyipa) ndi lonjezo loti tidzapeza chisangalalo kapena phindu. Tonsefe, zaka zathu zilibe kanthu, tidzayesedwa pa moyo wathu wonse, koma ndi bwino kukumbukira kuti mayeso si uchimo. Mayeso ndi mwayi wochita zinthu zosakondweretsa Mulungu, kutanthauza kudzikondweretsa tokha, kapena kusankha kusadzikondweretsa tokha ndi kukondweretsa Mulungu ponena AYI ku mayeso.
Zinthu zambiri padziko lapansi, ngakhale anthu, zidzagwiritsidwa ntchito kutikopa kuchimwa, kuti titsatire Satana m'malo motsatira Mulungu. Gawo la moyo uno ndikuphunzira kugonjetsa mayeso ndi kusankha chabwino pa choipa. Kuyambira kugwa kwa Adamu ndi Eva, anthu akhala akulolera zilakolako za dziko lapansi ndi kugonjera zilako lako za thupi. Monga ana a Mulungu, tiyenera kuphunzira kugwiritsa ntchito ufulu wathu wosankha kuti tigonjetse mayeso ndi kusankha kutsatira Yesu Khristu mwa kufuna kwathu.
Munthu wothawa mayeso si wamantha, ndi wolimba mtima pamaso pa Mulungu! (Yakobo 1:12)
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo.
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.
Tsono popeza kuti iye yemwe adazunzikapo ndi kuyesedwapo, ndiye kuti angathe kuŵathandiza anthu amene amayesedwa.
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo.
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo.
Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.
Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Zitatha izi, Mzimu Woyera adatsogolera Yesu kupita ku chipululu kuti Satana akamuyese.
Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
Pamenepo Satana adamsiya, angelo nkubwera kumadzamutumikira Yesuyo.
Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Musamakanane, koma pokhapokha mutavomerezana kutero pa kanthaŵi kuti mudzipereke ku mapemphero. Pambuyo pake mukhalenso pamodzi, kuwopa kuti Satana angakuyeseni chifukwa cha kulephera kudzigwira.
Sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna.
Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja.
Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.
Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.
Ndiye kuti pamene anthu osamala za Mulungu akuyesedwa, Iye amadziŵa kuŵapulumutsa kwake. Koma amadziŵanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo.
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Musatengeke mtima ndi njira za mkazi ameneyo, musasokere potsata njira zakezo.
Paja iye uja adagwetsa amuna ambiri, anthu amene adaŵaphetsa ngosaŵerengeka.
Nyumba yake ndi njira yakumanda, yotsikira ku dziko la anthu akufa.
Koma anthu ofuna kulemera, amagwa m'mayeso, amagwidwa mu msampha wa zilakolako zambiri zopusa ndi zoononga. Zilakolakozo zimamiza anthu m'chitayiko choopsa.
Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.
Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe.
Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,
ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.
Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Nchifukwa chake, pamene sindidathenso kupirira, ndidatuma Timoteo kuti adzaone m'mene chiliri chikhulupiriro chanu. Pakuti ndinkaopa kuti kapena Satana, Wonyenga uja, adakunyengani, ndipo kuti ntchito zathu zonse pakati panupo zidangopita pachabe.
Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa.
Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira.
Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo.
Thaŵani dama. Tchimo lina lililonse limene munthu amachita, siliipitsa thupi lake, koma munthu wadama amachimwira thupi lake lomwe.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe?
Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Ali ndi tsoka anthu apansipano chifukwa cha zochimwitsa. Zochimwitsazo sizingalephere kuwoneka, koma ali ndi tsoka munthu wobweretsa zochimwitsayo.
“Tsono ngati dzanja lako kapena phazi lako likuchimwitsa, lidule ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli woduka dzanja kapena phazi, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wosatha uli ndi manja onse kapena mapazi onse aŵiri.
Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole ndi kulitaya. Ndi bwino kuti ukaloŵe ku moyo uli ndi diso limodzi lokha, kupambana kuti ukaponyedwe ku moto wa Gehena uli ndi maso aŵiri.”
Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena.
“Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”
Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao.
Njoka ndi kuchenjera kwake idanyenga Heva. Ndikuwopa kuti maganizo anu angaipitsidwe chimodzimodzi, ndipo mungaleke kudzipereka kwa Khristu ndi mtima wonse.
Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.
Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa?
Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera?
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Paja mkazi wadama ali ndi pakamwa pokoma ngati uchi, mau ake ndi osalala koposa mafuta.
Koma kotsiriza kwake ngwoŵaŵa ngati chivumulo, ngwolasa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.
Mapazi ake ndi oloza ku imfa, poyenda amaloŵera njira yakumanda.
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Mbeu zogwera pa nthaka yapathanthwe zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangokhulupirira kanthaŵi pang'ono chabe, mwakuti pa nthaŵi ya kuyesedwa, amabwerera m'mbuyo.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.