Mzimu Woyera amapatsa munthu wina mphatso ya kulankhula zanzeru, ndipo Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kulankhula mau olangiza anthu.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.
Ndikufuna kuti zimenezi ziŵalimbitse mtima, ndipo azilunzana pamodzi m'chikondi, azikhala odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu. Motero adzatha kudziŵa mozama chinsinsi cha Mulungu chonena za Khristu. Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti, “Usagwire chakuti”, “Usakhudze chakuti”? Malamulo ameneŵa ndi zophunzitsa zimenezi ndi za anthu chabe, ndipo zimangokhudza zinthu zimene zimatha, anthu akamazigwiritsa ntchito. Kwinaku mauwo amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamula anthu zambiri pa za kupembedza, za kudzichepetsa ndi za kuzunza thupi lao. Komabe malamulowo alibe phindu, ndipo sathandiza konse kugonjetsa khalidwe longosangalatsa thupi. Mwa Iyeyu mudzapeza chuma chonse chobisika, ndiye kuti nzeru ndi luntha.
Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza.
“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
Mulungu adapatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka, nzeru zake zinali zopanda malire. Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa, anali alembi. Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri. Motero nzeru za Solomoni zidapambaniratu nzeru za anthu onse akuvuma, ndiponso za anthu onse a ku Ejipito.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.
Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.
Komabe pakati pa anthu okhwima m'chikhulupiriro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha. Nzeru zimene timalankhula, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi, zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero.
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse. Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu.
Choncho adauza munthu kuti, ‘Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zimenezo, kuthaŵa zoipa ndiye luntha limenelo.’ ” Yobe
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe. Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
“Koma nzeru zingapezeke kuti? Luntha lingapezeke kuti? Anthu sadziŵa kufunika kwake kwa nzeruzo, ndipo sizipezeka pa dziko lino lapansi.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.
Ndimakonda malamulo anu kwambiri, ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse. Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Mulungu ndiye adakulunzanitsani ndi Khristu Yesu, ndipo adamsandutsa kuti akhale nzeru yathu. Chifukwa cha Yesu, timapezeka olungama pamaso pa Mulungu. Ndi Yesuyo amene amatisandutsa anthu akeake a Mulungu, ndiye amatipulumutsa.
Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu. Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza.
Ndinkati ayambe ndi akuluakulu aja kulankhula, chifukwa amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru. Koma mzimu wa Mphambe ndiwo umaloŵa mwa anthu ndi kuŵapatsa nzeru.
Iyeyu ndampatsa mzimu wanga, kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru, ndipo akudziŵa bwino ntchito zonse zaluso monga izi:
Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziŵa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?”
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu. Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo. Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo. Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo. Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu. Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa.
Mwanayo ankakula, nasanduka wamphamvu nkukhalanso wa nzeru zabasi. Ndipo Mulungu ankamudalitsa.
zimene Mulungu adatipatsa mochuluka. Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale.
Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.
Chauta akunena kuti, “Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake, munthu wamphamvu asanyadire mphamvu zake, ndipo munthu wolemera asanyadire chuma chake. Koma ngati wina afuna kunyadira, anyadire ichi chakuti amamvetsa za Ine, ndipo amandidziŵa. Amadziŵa kuti Ine ndine Chauta wokonda chifundo, chilungamo, ndi ungwiro pa dziko lapansi. Ndithudi, pazimenezi ndipo pali mtima wanga.”
koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi.
Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru, koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere. Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Nchifukwa chake Nzeru ya Mulungu idati, ‘Ndidzaŵatumizira aneneri ndi atumwi, koma anthu adzapha ena mwa iwo, nkuzunza ena.’
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.
Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Chiweruzo cha Chauta nchoona, ncholungama nthaŵi zonse.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni: