Mulungu wapatsa mphatso ana ake, ndipo Mzimu Woyera amagawa mphatso zimenezi monga mmene Iye akufunira. Monga mmene lemba la 1 Akorinto 12:11 limatiuza, "Mzimu yemweyo amagwira ntchito mwa onse, akugaŵira aliyense payekha monga mmene Iye akufunira."
Mphatso zauzimu ndi zipangizo zapadera zimene Mulungu amapatsa ana ake kuti amange mpingo wake ndi anthu ake, malinga ndi zosowa za kuwonetsa mphamvu yake. Tiyenera kugwiritsa ntchito mphatso zimenezi kuti tidalitsane wina ndi mnzake ndipo motero timange mpingo wamphamvu wolemekeza Mulungu.
Mphatso imene Mzimu Woyera waika mwa iwe ndi chizindikiro cha chikondi cha Atate wakumwamba. Choncho, usayibise kapena kuilola kuti itaike, uyisamalire ngati chuma chamtengo wapatali ndipo uthokoze Mulungu nthawi zonse kuti uzitha kuyigwiritsa ntchito potumikira ena, podziwa kuti si ya phindu lako, koma ya phindu la iwo akuzungulira iwe.
Mulungu wakutuma kuti ukhale yankho la mapemphero awo. Kumbukira nthawi zonse kuti mphatso sizichoka, kutanthauza kuti Ambuye sadzachotsa chimene wakupatsa. Choncho, khalani woyang'anira bwino wa chimene Mulungu wakupatsa ndipo usaiwale kumupatsa ulemerero nthawi zonse, chifukwa ndiwe chotengera m'manja mwake.
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni.
Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi.
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.
Nchifukwa chake palibe mphatso yauzimu imene yakupereŵerani, pamene mukudikira kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi. Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima. M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.” Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira. Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala? Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima, ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi. Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo. Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha. Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena. Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa. Koma Mulungu akaulula kanthu kwa munthu wina amene ali pomwepo, amene akulankhulayo akhale chete. Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa. Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo. Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu, akazi akhale chete m'misonkhano ya mpingo, pakuti iwo saloledwa kulankhula. Monga Malamulo a Mose anenera, akazi azikhala omvera. Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna ao kunyumba. Pajatu nchamanyazi kuti mkazi alankhule mu msonkhano wa mpingo. Monga nkuti mau a Mulungu adachokera kwa inu? Kaya kapena adafika kwa inu nokha? Ngati wina akuyesa kuti akulankhula mau ochokera kwa Mulungu, kapena kuti akuuzidwa mau ndi Mzimu Woyera, avomereze kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo lochokera kwa Ambuye. Ngati munthuyo savomereza zimenezi, Mulungunso samuvomereza iyeyo. Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo.
Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.
Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu.
Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo,
Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.
Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:
Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.
Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa? Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.” Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira?
Ngakhale nditakhala ndi mphatso ya uneneri, ngakhale nditamadziŵa zobisika zonse, ndi kumamvetsa zinthu zonse, ngakhale nditakhala ndi chikhulupiriro chachikulu chakuti ndingathe kusuntha mapiri, koma ngati ndilibe chikondi, sindili kanthu konse.
Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo.
Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto.
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.
Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati,
Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.” Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa.
Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo.
Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.
Mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandisandutsa wolalika Uthenga Wabwino umenewu, ndipo pakutero adaonetsapo mphamvu yake.
Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko.
Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.
Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.
Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.
Komabe aliyense wa ife adalandira mphatso yakeyake yaulere, molingana ndi m'mene Khristu amaperekera mphatso zake.
Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera. Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku. Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.