Mawu a Mulungu amatiphunzitsa mu 1 Timoteo 5:22 kuti tisamafulumire kuyika manja pa wina aliyense, kapena kutenga nawo mbali mu machimo a ena. Tiyenera kudzisunga oyera. Kuyika manja sikuyenera kuchitika chifukwa cha kutengeka maganizo kapena chifundo, koma chiyenera kuchitika motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Choncho, tiyenera kuchita izi moganizira bwino kwambiri kuti moyo wa munthuyo udalitsidwe.
Kuyika manja kumachitika popereka madalitso, mphamvu zauzimu, kapena pochiza. M’Chikhristu, ndi chizindikiro chosonyeza kupereka Mzimu Woyera ndi kugwirizana ndi Mulungu. Timaona kuyika manja m’mavesi ambiri a m’Baibulo. Mwachitsanzo, m’Chipangano Chakale, Mose anayika manja pa Yoswa asanatsogolere Aisraeli kulowa m’dziko lolonjezedwa. M’Chipangano Chatsopano, Yesu nayenso anaika manja pochiza odwala ndi kutulutsa ziwanda.
Komabe, nthawi zonse tiyenera kukumbukira kuti mphamvu yeniyeni imachokera kwa Mulungu, ndipo kuyika manja ndi njira imodzi yokha imene tingagwiritsire ntchito kukhala chida cha Mulungu pa moyo wa wina. Choncho, n’kofunika kuti amene akuyika manja adzipereke kwa Mulungu ngati nsembe yolandirika, kuti agwiritsidwe ntchito ngati chida cholemekezeka m’manja mwake.
Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja.
Usafulumire kumsanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa uchimo wao. Iwe usunge bwino kuyera mtima kwako.
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
Dzuŵa likuloŵa, anthu onse amene anali ndi anzao odwala nthenda zosiyanasiyana, adabwera nawo kwa Yesu. Iye adasanjika manja pa wodwala aliyense, naŵachiritsa onse.
Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati, “Usaope. Woyamba ndiponso Wotsiriza ndine.
za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni.
Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo idzalandiridwa kuti ikhale yopepesera machimo ake.
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja. Umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse, tsono umlonge m'malo mwako, iwo akupenya. Iwoŵa adakaima pamaso pa Mose, pa wansembe Eleazara, pa atsogoleri, ndiponso pamaso pa mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, nati, Umpatseko udindo wako, kuti mpingo wonse wa Aisraele uzimumvera. Tsono adzapite kwa wansembe Eleazara amene adzamdziŵitse zimene Chauta akufuna, pofunsa kwa Urimu ndi Tumimu. Umotu ndi m'mene Iyeyu adzatsogolere ndi kulamula Yoswa ndi mpingo wonse wa Aisraele.” Mose adachitadi monga momwe Chauta adamlamulira. Adamtengadi Yoswa namuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara ndi pamaso pa mpingo wonse. Ndipo adamsanjika manja, nampatsa udindo monga momwe Chauta adamlangizira kudzera mwa Mose.
Anthu ena ankabwera ndi ana kuti Yesu aŵasanjike manja ndi kuŵapempherera, ophunzira ake nkumaŵazazira. Koma Yesu adati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wakumwamba ndi wa anthu otere.” Atatero adaŵasanjika manja, kenaka nkumapita.
Tsono Yoswa, mwana wa Nuni, adadzazidwa ndi nzeru, chifukwa Mose adaamsanjika manja kuti aloŵe m'malo mwake. Aisraele adamvera Yoswa, ndi kutsata malamulo onse amene Chauta adaŵapatsa kudzera mwa Mose.
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu amene mzimu wa Mulungu uli mwa iye, ndipo umsanjike manja.
Nchifukwa chake ndikukukumbutsa kuti mphatso imene Mulungu adakupatsa pamene ndidakusanjika manja, uiyatsenso ngati moto.
Adaŵaimiritsa pamaso pa atumwi, ndipo atumwiwo adapemphera naŵasanjika manja.
Bambo wake wa Publioyo anali gone, chifukwa ankadwala malungo ndi kamwazi. Paulo adaloŵa m'chipinda chake nayamba kupemphera, ndipo adamsanjika manja nkumuchiritsa.
Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu.
Motero sadathe kuchita zinthu zamphamvu kumeneko. Adangosanjika manja pa odwala oŵerengeka, nkuŵachiritsa.
ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”
Pamenepo Ananiya adanyamuka nakaloŵa m'nyumbamo. Adamsanjika manja Sauloyo nati, “Mbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene adakuwonekera pa njira imene wadzera ija, andituma. Akufuna kuti upenyenso, ndipo udzazidwe ndi Mzimu Woyera.”
Pamene Yesu ankakamba zimenezi, munthu wina wamkulu adadzamgwadira nati, “Mwana wanga wamkazi wamwalira tsopano apa. Chonde bwerani mudzamsanjike manja, kuti akhale ndi moyo.”
Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa.
“Pambuyo pake ubwere ndi ng'ombe yamphongo pakhomo pa chihema chamsonkhano. Tsono Aroni ndi ana ake asanjike manja ao pamutu pa ng'ombeyo.
Wansembe abwere ndi ng'ombeyo pa khomo la chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta. Tsono asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphe pamaso pa Chauta.
nayamba kumdandaulira kwambiri. Adati, “Pepani, mwana wanga wamkazi ali pafupi kufa. Ngati nkotheka, mukamsanjike manja kuti achire ndi kukhala ndi moyo.”
Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha, ndipo adachiradi.
Yesu adamgwira dzanja, natuluka naye kunja kwa mudzi. Adapaka malovu m'maso mwa munthuyo, namsanjika manja nkumufunsa kuti, “Kodi ukuwona kanthu?” Munthu uja adaŵeramuka nati, “Ndikuwona anthu akuyenda, koma akuwoneka ngati mitengo.” Yesu adamuikanso manja kumaso kwake. Munthu uja adayang'anitsitsa ndipo adachira, nayamba kumapenya zonse bwino lomwe.
Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.
Anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu yemwe anali gonthi ndi wolankhula movutikira. Anthuwo adapempha Yesu kuti amchiritse pomusanjika manja munthuyo. Yesu adatengera munthu uja pambali kumchotsa pa khamu la anthu. Adapisa zala m'makutu a munthuyo, nalavula malovu, nkukhudza lilime la munthu uja. Adayang'ana kumwamba, nadzuma, nkumuuza kuti, “Efata!” ndiye kuti “Tsekuka!” Pomwepo makutu a munthuyo adatsekuka, ndipo chimene chinkamanga lilime lake chidamasuka, mpaka adayamba kulankhula bwino lomwe.
Simoni uja ataona kuti Mzimu Woyera waperekedwa kwa iwo atumwi aja ataŵasanjika manja, adafuna kuŵapatsa ndalama atumwiwo. Adati, “Bwanji mutandipatsako inenso mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndikamsanjike manja, akalandire Mzimu Woyera.”
Koma Yakobe adasemphanitsa manja. Motero adasanjika dzanja lake lamanja pamutu pa Efuremu amene anali wamng'ono, dzanja lamanzere adalisanjika pamutu pa Manase amene anali wamkulu. Ndipo adadalitsa Yosefe ndi mau akuti, “Mulungu amene makolo anga Abrahamu ndi Isaki adamtumikira, Mulungu amene wanditsogolera moyo wanga wonse mpaka lero lino, aŵadalitse anaŵa!
Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja naŵapatsa ulamuliro ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa yonse ndi zochiritsira nthenda.
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.”
Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.
Stefano anali munthu amene Mulungu adamkomera mtima kwambiri namdzaza ndi mphamvu, kotero kuti ankachita zizindikiro zozizwitsa pakati pa anthu.
Ambuye ankaŵalimbikitsa, mwakuti anthu ambiri adakhulupirira natembenukira kwa Ambuye.
Zitachitika zimenezi, anthu ena onse odwala pachilumbapo adabwera, Paulo nkuŵachiritsa.
Atatero, adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino ngati linzake.
Yesu adatuluka m'chombomo, ndipo pamene adaŵaona anthu ambirimbiriwo, adaŵamvera chifundo, nayamba kuchiritsa amene ankadwala.
Yesu adaŵamvera chifundo nakhudza maso ao. Pompo iwo adayamba kupenya, kenaka nkumamutsata.
Yesu adamumvera chifundo. Adatambalitsa dzanja nkumukhudza nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!”
Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha.
Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo, namuuza kuti, “Pita ukasambe ku dziŵe la Siloamu.” (Tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, Wotumidwa.) Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya.
Atatero adamgwira dzanja lamanja, namuimiritsa. Pompo mapazi ake ndi akakolo ake adalimba.
Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
Tsono uŵadzoze monga momwe udadzozera bambo wao, kuti akhale ansembe onditumikira Ine. Kudzozedwako kudzaŵasandutsa ansembe pa mibabwo ndi mibadwo.”
Mafuta ena odzozerawo adaŵathira pamutu pa Aroni, namdzoza, ndi kumsandutsa wopatulika.
Eliya atachoka kumeneko, adakapeza Elisa akulima ndi pulawo yokokedwa ndi ng'ombe. Panali magoli khumi ndi aŵiri, mwiniwakeyo nkumakuyenda ndi goli lotsiriza. Eliya adabwera kumene kunali iyeko, namuveka mwinjiro wake.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.
Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.
Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa. Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.
Anthu akhungu ndi opunduka adadza kwa Yesu m'Nyumba ya Mulungumo, ndipo Iye adaŵachiritsa.
Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri. Tsono Iye adayankha ophunzira a Yohane aja kuti, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mwaona ndi kuzimva. Akhungu akupenya, opunduka miyendo akuyenda, akhate akuchira, agonthi akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino.
Ophunzira aja adapitadi, adanka nalalika Uthenga Wabwino ku midzi yonse, nkumachiritsa anthu ponseponse.
Muchiritse anthu odwala amene ali m'mudzimo, ndipo muŵauze kuti, ‘Tsopano ufumu wa Mulungu wakufikirani.’
Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
ndipo waona m'masomphenya munthu wina, dzina lake Ananiya, akuloŵa ndi kumsanjika manja kuti apenyenso.”
Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.
ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko.
Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda.
Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu.
Kodi Mulungu amene amakupatsani Mzimu Woyera, nachita zozizwitsa pakati panu, amachita zimenezi chifukwa mumatsata Malamulo, kapena chifukwa mudamva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino?
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa,
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Ankatulutsa mizimu yoipa yocholuka, ndiponso ankadzoza mafuta anthu odwala ambiri nkumaŵachiritsa.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!”
Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.
Petro adaŵapempha onse kuti atuluke, ndipo adagwada pansi nkumapemphera. Kenaka adatembenukira mtembo uja nati, “Tabita, dzuka!” Apo Tabita adatsekula maso, ndipo pamene adaona Petro, adakhala tsonga. Petro adamgwira dzanja namuimiritsa. Ndipo adaitana anthu a Mulungu ndi azimai amasiye aja, nampereka kwa iwo ali wamoyo.
Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza, natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala.
Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.