Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.
Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu?
koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,
Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu.
Mzimu Woyera akunena momveka kuti pa masiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chao. Adzamvera mizimu yonyenga ndi zophunzitsa zochokera kwa mizimu yoipa.
Abale, ndifuna kuti muzindikire bwino za mphatso za Mzimu Woyera. Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo. Amene amachititsa anthu zonsezi ndi Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Amagaŵira munthu aliyense monga momwe Iye afuna kumgaŵira.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Anthu otereŵa si atumwi oona, koma antchito onyenga, amene amadzizimbaitsa, naoneka ngati atumwi a Khristu. Zimenezitu si zododometsa ai, pakuti Satana yemwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati mngelo wounikira anthu. Motero si chodabwitsa ngati atumiki ake omwe amadzizimbaitsa, naoneka ngati otumikira chilungamo. Potsiriza adzalandira molingana ndi zimene ankachita.
Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira.
Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziŵa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?”
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Nthaŵi ina pamene tinkapita ku malo opemphererako, tidakumana ndi kapolo wachitsikana amene adaagwidwa ndi mzimu woipa womunenetsa zakutsogolo. Ankapindulitsa mbuye wake kwambiri ndi kulosa kwakeko. Iyeyo adayamba kutitsatira Paulo ndi ife, akufuula kuti, “Anthu aŵa ndi atumiki a Mulungu Wopambanazonse, akukulalikirani njira ya chipulumutso.” Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi.
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndikudziŵa kuti mwakhala mukugwira ntchito kolimba, ndipo kuti muli ndi kupirira kosatepatepa. Ndikudziŵanso kuti anthu ochimwa simungaŵalekerere. Anthu amene amadzitcha atumwi, pamene sali atumwi konse, mwaŵayesa, ndipo mwaŵapeza kuti ngonama.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.
Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta. Ndipo kuwopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva.
Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena.
Komabe panali aneneri ena onama ngakhale pakati pa Aisraele omwe. Momwemonso pakati pa inu padzaoneka aphunzitsi onama. Iwowo adzaloŵetsa mwachinsinsi zophunzitsa zonama ndi zoononga, ngakhale kukana kumene Mbuye wao amene adaŵaombola, ndipo motero adzadziitanira chiwonongeko mwamsanga.
Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako?
Koma aliyense, kaya ndife kaya ndi mngelo wochokera Kumwamba, akakulalikirani uthenga wabwino wosiyana ndi uja tidakulalikiraniwu, ameneyo akhale wotembereredwa.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuuzeni za iwo aja amene amafuna kukusokeretsani. Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Munthu wolemera amadziyesa wanzeru, koma munthu wosauka amene ali womvetsa zinthu, amamtulukira.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
“Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’ Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.”
Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera angathe kuzindikira khalidwe la zonse, ndipo palibe wina amene angathe kutsutsapo ai.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho. Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto.
Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena.
Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe.
“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa. Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa,
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu.
Yesu adati, “Chenjerani kuti anthu angakusokezeni. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine.’ Azidzatinso, ‘Nthaŵi yayandikira.’ Amenewo musadzaŵatsate.
Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
“Musamapatsa agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zamtengowapatali, kuwopa kuti zingazipondereze, kenaka nkukutembenukirani ndi kukukadzulani.