Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


138 Mau a m'Baibulo Okhudza Mdima

138 Mau a m'Baibulo Okhudza Mdima

Ukaiganizira za dziko la mdima, mungaliwone ngati malo amdima, oipa, komanso osokoneza. Baibulo limatiphunzitsa kuti dziko la mdima likuimira chilichonse chotsutsana ndi kuunika kwa Mulungu, malamulo ake, komanso dongosolo lake labwino pa miyoyo yathu.

Muyenera kudziwa kuti pali gulu lankhondo la Satana lomwe likuyendayenda nthawi zonse, cholinga chake chokha ndikutsutsana ndi chifuniro cha Mulungu, kubweretsa chiwonongeko kwa anthu. Aefeso 6:12 amatiuza kuti “sitikumenyana ndi anthu, koma ndi olamulira, ndi akuluakulu, ndi mafumu a dziko la mdima lino, ndi mizimu yoipa m’malo akumwamba.”

Vesi limeneli limatithandiza kumvetsa kuti kumbuyo kwa mphamvu zomwe zimalimbikitsa zoipa padziko lapansi, pali zenizeni zauzimu zomwe tiyenera kukumana nazo kudzera mu mphamvu ya Mulungu.

Komanso, 1 Petro 2:9 amatikumbutsa kuti monga ana a Mulungu, tinaitanidwa “kuchokera mu mdima kulowa mu kuunika kwake kodabwitsa.” Izi zimationetsa kuti, ngakhale tidali mumdima, tsopano tili mu ufumu wa kuunika kwa Mulungu.

Choncho, ili ndi pempho loti tikhale omvera Mulungu, Mawu ake, ndikuwonetsa ulemerero wake pakati pa dziko lodzaza ndi chisokonezo ndi kutayika mtima. N’zoona kuti mdima waukulu waphimba dziko lapansi, kuipa ndi uchimo zikuchulukirachulukira, koma n’zoonaninso kuti ana a Mulungu ndife amene tiyenera kukhala kuunika m’dziko lomwe likufunikira kuwunikiridwa kwathu.

Sitingaleke kupemphera, kulira, ndikupempherera mpaka titaona Ufumu wa Khristu utakutidwa padziko lapansi, ndipo ntchito yathu ndikuchotsa mdima wonse m’dzina la Yesu.




Yohane 8:12

Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:2

Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 10:21-23

Pambuyo pake Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti pagwe mdima wandiweyani pa dziko lonse la Ejipito.” Mose adakweza dzanja lake kumwamba, ndipo pa masiku atatu, mudagwa mdima wandiweyani m'dziko lonse. Aejipitowo sankathanso kuwonana, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adachoka pakhomo pake masiku atatu onsewo. Koma Aisraele okha ankakhala koŵala ndithu kuja ankakhalaku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:5

Kuŵalako kukuunikabe mu mdima, ndipo mdima sudathe kugonjetsa kuŵalako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:28

Ndithu, Inu mumayatsa nyale ya moyo wanga. Chauta, Mulungu wanga, amandiwunikira mu mdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:1-2

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Mulungu adautcha mtundawo Dziko, madzi adaŵasonkhanitsa aja adaŵatcha Nyanja. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Tsono adati, “Panthaka pamere zomera zobala njere, ndiponso mitengo yobala zipatso zanjere malinga ndi mtundu wake,” ndipo zidachitikadi. Motero panthaka padamera zomera za mitundu yonse, zipatso zokhala ndi njere ndi mitengo yobeleka zipatso za njere, malingana ndi mitundu yao. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachitatu. Pambuyo pake Mulungu adati, “Kuthambo kukhale miyuni kuti izilekanitsa usana ndi usiku, ndiponso kuti ikhale zizindikiro za nyengo, masiku ndi zaka. Miyuni imeneyi ikhale ku thambo ndi kumaunikira dziko lapansi,” ndipo zidachitikadi. Motero Mulungu adalenga miyuni iŵiri yaikulu: dzuŵa loŵala masana, ndi mwezi woŵala usiku. Adalenganso nyenyezi. Mulungu adaika miyuniyo ku thambo, kuti iziwunikira dziko lapansi, kuti iziŵala usana ndi usiku, kulekanitsa kuyera ndi mdima. Mulungu adaona kuti zinali zabwino. Ndipo kudali madzulo ndiponso m'maŵa, tsiku lachinai. Dziko lapansilo linali lopanda maonekedwe enieni ndiponso losakonzeka. Mdima unali utaphimba nyanja yaikulu ponseponse, ndipo Mzimu wa Mulungu unkayendayenda pamwamba pa madziwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:8

Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 88:6

Inu mwandiika pansi penipeni pa dzenje m'malo akuya a mdima wandiweyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:2

Anthu amene ankayenda mumdima aona kuŵala kwakukulu. Amene ankakhala m'dziko la mdima wandiweyani, kuŵala kwaŵaonekera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:6

Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:7

Udzaŵatsekula maso anthu akhungu, udzamasula akaidi m'ndende, udzatulutsa m'ndende anthu okhala mu mdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:14

Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:5

Uthenga umene tidamva kwa Iye, ndipo timaulalika kwa inu, ndi wakuti Mulungu ndiye kuŵala, ndipo mwa Iye mulibe mdima konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:2

Mdima udzaphimba dziko lapansi, mdima wandiweyani udzagwa pa anthu a mitundu ina. Koma iwe, Chauta adzakuŵalira, ulemerero wake udzaoneka pa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:16

Anthu okhala mu mdima aona kuŵala kwakukulu. Anthu okhala m'dziko la mdima wabii wa imfa, kuŵala kwaŵaonekera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13-14

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:23

Koma ngati maso ako sali bwino, m'thupi mwako monse mumakhala mdima. Tsono ngati kuŵala kumene kuli mwa iwe kusanduka mdima, mdima wakewo ndi wochita kuti goo!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11-12

Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:12

Koma chonsecho amene akadayenera kukhala mu Ufumuwo, adzaŵaponya kunja, ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano chifukwa cha zoŵaŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:3

Nchifukwa chake zonse zimene mwalankhula pa mdima, zidzamveka poyera, ndipo zonse zimene mwanong'oneza anthu m'kati mwa nyumba, adzazilengeza pa bwalo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:19

Mlandu wake ndi uwu wakuti ngakhale kuŵala kudadza pansi pano, anthu adakonda mdima, osati kuŵalako, chifukwa zochita zao zinali zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:13

Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:12

Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:30

Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:9

Munthu akamati ali m'kuŵala, komabe nkumadana ndi mnzake, akali mu mdima ameneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 15:33

Nthaŵi itakwana 12 koloko masana, padaagwa mdima pa dziko lonse mpaka pa 3 koloko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:79

Kuŵala kwake kudzaunikira onse okhala mu mdima wabii ngati wa imfa, kudzatitsogolera pa njira ya mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:53

Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu, inuyo osandigwira. Koma ino ndi nthaŵi yanu ndiponso ya mphamvu za mdima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:11

Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:19

Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:14

Iwowo amakumana ndi mdima ngakhale masana, amayambasa masanasana ngati usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 82:5

Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru, amangoyenda m'chimbulimbuli. Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:9

Anthu akuti, “Chifukwa cha zonsezo chilungamo chatikhalira kutali, ndipo kukhala aungwiro nkosatheka. Timafunafuna kuŵala, koma timangopeza mdima. Timayembekeza kuti kudzakhala mbee, koma kuli bii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:35-36

Apo Yesu adaŵauza kuti, “Kuŵala kukhalabe pakati panu, koma kanthaŵi pang'ono chabe. Yendani pamene kuŵalako kuli pakati panu, kuti mdima ungakugwereni. Munthu woyenda mu mdima saona kumene akupita. Nthaŵi ino pamene kuŵala kuli pakati panu, mukhulupirire kuŵalako, kuti mukhale anthu oyenda m'kuŵala.” Yesu atanena zimenezi, adachokapo nakabisala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 13:16

Mlemekezeni Chauta, Mulungu wanu, asanagwetse mdima, mapazi anu asanakhumudwe m'chisisira cham'mapiri, asanasandutse kuŵala, kumene mukukufuna, kuti kukhale mdima wandiweyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 26:18

Ndikukutuma kuti anthu ameneŵa uŵatsekule maso, kuti atembenuke kuchoka mu mdima wa machimo nkuloŵa m'kuŵala, ndiponso kuchoka m'mphamvu ya Satana nkutsata Mulungu. Ndifuna kuti akhulupirire Ine, kuti machimo ao akhululukidwe, ndipo alandire nao madalitso pamodzi ndi anthu amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale akeake.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:5

Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:10

Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:9

Kwa Inu kuli kasupe wamoyodi, m'kuŵala kwanu ifenso timaona kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:12

ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 50:10

Ndani mwa inu amaopa Chauta, ndi kumvera mau a mtumiki wake? Aliyense woyenda mu mdima, wopanda chomuunikira, akhulupirire dzina la Chauta, ndipo adalire Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 32:8

Ndidzazimitsa zoŵala zonse zamumlengalenga, ndipo dziko lako ndidzalichititsa mdima. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:20

Kodi suja tsiku la Chauta ndi mdima wokhawokha osati kuŵala, kodi suja lili ngati usiku wabii wopanda mpoti mbee pomwe!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 3:6

Ndiye Chauta akuti, “Nchifukwa chake simudzaonanso zinthu m'masomphenya, simudzalosanso konse. Inu aneneri, kwakuderani, mdima wakugwerani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:6

Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:8

Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Zimene lamuloli likunena, zidachitikadi mwa Yesu, ndipo zikuchitikanso mwa inu. Pajatu mdima ulikutha, ndipo kuŵala kwenikweni kwayamba kale kuti ngwee.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:30

Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:20

Tsoka kwa amene zoipa amaziyesa zabwino ndipo zabwino amaziyesa zoipa, amene mdima amauyesa kuŵala, ndipo kuŵala amakuyesa mdima, amene zoŵaŵa amaziyesa zozuna, ndipo zozuna amaziyesa zoŵaŵa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:15

Adati, “Ambuye mchitireni chifundo mwana wanga. Ali ndi khunyu ndipo amavutika koopsa. Kaŵirikaŵiri amagwa pa moto mwinanso m'madzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:4

Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera, Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba. Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:6

Njira yao ikhale yamdima ndi yoterera, pamene mngelo wa Chauta akuŵalondola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:12-14

Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 44:19

Komabe Inuyo mwatitswanya ndi kutisiya pakati pa nkhandwe ku chipululu, kumene kuli mdima wandiweyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:10

Ena adakhala mu mdima ali ndi chisoni, anali am'ndende ozunzika m'maunyolo achitsulo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:13

amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 30:18

Ku Tehafinehesi kudzachita mdima, pamene ndidzathyole mphamvu za Ejipito kumeneko. Motero kunyada kwake kudzatha. Mitambo idzamuphimba, ndipo okhala m'midzi yake adzatengedwa ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21-22

Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima. Iwo amadziyesa anzeru, koma chikhalirecho ndi opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 143:3

Mdani wandilondola, wavimviniza moyo wanga m'dothi, wandikhazika mu mdima, ngati anthu amene adafa kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:23

Pokhala ndi chikhulupiriro, atabadwa Mose, makolo ake adamubisa miyezi itatu, poona kuti mwana waoyo anali wokongola. Sadaope konse lamulo lamphamvu la mfumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:19

Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 29:15

Tsoka kwa amene amabisira Chauta maganizo ao, amene amachita ntchito zao mu mdima, namaganiza kuti palibe amene akuŵaona ndi kudziŵa zimene akuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 88:12

Kodi zodabwitsa zanu zimadziŵika mu mdima? Ndani angadziŵe za chithandizo chanu chopulumutsa m'dziko la anthu oiŵalika?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:19

Njira ya munthu waulesi ndi yoŵirira ndi minga, koma njira ya munthu wolungama imakhala ngati mseu wosalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:14

Chauta adaŵatulutsa anthuwo mu mdima ndi m'chisoni muja, ndipo adadula maunyolo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:5

Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:4-5

Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala. Paja nonsenu zanu zonse ndi zam'kuŵala, ndiye kuti zausana. Ife zathu si zausiku kapena zamumdima ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:17

Aphunzitsi onyengaŵa ali ngati akasupe opanda madzi, ngati nkhungu yokankhidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu adaŵasungira mdima wakuda wabii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:14

Alekeni, ndi atsogoleri akhungu ameneŵa. Tsono ngati wakhungu atsogolera wakhungu mnzake, onse aŵiri adzagwa m'dzenje.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:39

Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Kodi wakhungu nkutsogolera wakhungu mnzake? Nanga onse aŵiri sadzagwa m'dzenje kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:20

Mumapanga mdima nukhala usiku, ndipo nyama zam'nkhalango zimatuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:6-7

Tikanena kuti timayanjana naye, pamene tikuyendabe mu mdima, tikunama, ndipo zochita zathu nzosagwirizana ndi zoona. Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10-11

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana. Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:17

Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzadziŵika nkuwonekera poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:11

Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:17

Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:6-7

Nthambo yasiliva idzamasuka, mbale yagolide idzasweka, mtsuko udzaphwanyika ku kasupe, ndipo mkombero udzathyoka ku chitsime. Pamenepo thupi lidzabwerera ku dothi monga m'mene lidaaliri, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene adaupereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:20-21

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona. Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:21

Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:1-2

Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu. Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite. Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala. Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu. Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa. Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere. Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu. Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye. Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:42

nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:1

Iwe Yerusalemu dzuka, ŵala, kuŵala kwako kwayamba. Ulemerero wa Chauta wakuŵalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:2

Amadzinyenga m'maganizo mwake, kotero kuti tchimo lake sangathe kulizindikira ndi kudana nalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:4

Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:14

Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:15-16

Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse. Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:4

Ngakhale nthaŵi ya mdima, munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala, chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:35-39

Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:24

Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:1-3

Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:20

nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:16

Munthu wabwino amagwa kasanunkaŵiri, koma amadzukirira ndithu, m'menemo anthu oipa tsoka limaŵagwera chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:41

Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:14

Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:6

Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse, sadzaiŵalika mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:11-12

Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-25

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:12-13

Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:20

Mau a munthu wochita zabwino, ali ngati siliva wabwino kwambiri, koma maganizo a anthu oipa ngachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Tsono muzigonjera Mulungu. Satana muzilimbana naye, ndipo adzakuthaŵani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:18

Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, dzina lanu likhale lolemekezeka nthawi zonse. Inu muli ndi moyo ndipo mukulamulira, mwabvala uleleme ndi mphamvu. Ndinu wapamwamba, wolamulira, wamphamvuzonse, wokwezeka komanso woopsa. Mtima wanga umakulambirani ndipo umalemekeza kukhalapo kwanu. Ndimavomereza kuti ndinu Mulungu ndipo palibe wina koma inu. Ife si kanthu popanda inu, ndinu zonse zomwe tikufuna. Chifukwa cha ichi ndikukweza pemphero langa kwa inu, Yesu ndikufuna thandizo lanu. Dziko lino likuipiraipira tsiku ndi tsiku ndipo likutsutsana ndi malamulo anu chifukwa cha mphamvu ya mdima yomwe ikugwira anthu. Ndikukupemphani nthawi ino kuti mundikweze kukhala kuwala pakati pa mdimawu. Ndifuna kunyamula mau anu kulikonse ndipo kulengeza ufulu kwa ogwidwa. Ndikupempheraninso mpingo wanu, mutikweze kukhala kuwala kuti maso a omwe ali mumdima awale. Mutiuze ngati zida zolimba m'manja mwanu kuti titsutse mapulani a mdani, chifukwa tikudziwa bwino lomwe kuti mau anu m'buku la Aefeso amati nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi olamulira, ndi akulu, ndi mafumu a dziko la mdima lino, ndi mizimu yoipa m'malo akumwamba. Ambuye Yesu, tikulengeza kuti m'dzina lanu ndife opwindula ndipo tidzawona kuwala kukuwala m'miyoyo yambiri kubweretsa chipulumutso ndi ufulu mumtima mwawo. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa