Mulungu, m’chifundo Chake chopanda malire, anandipatsa moyo kuti ndikhale paubwenzi wolimba ndi Iye. Mawu a Mulungu amandiphunzitsa kuti moyo ndi mpweya wa Mulungu ndipo ndi mbali ya umunthu wanga, ndipo ndi chizindikiro choyamba cha munthu wamoyo.
M’buku la Genesis 2:7 limati, “Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’mphuno mwake; ndipo munthuyo anakhala wamoyo.” Choncho, ine ndikuyitanidwa kukhala pamaso pa Mulungu kuti ndidzaze ndi mtendere ndi chimwemwe.
Moyo wanga unachokera ku mphamvu ya Mzimu wa Mulungu (Genesis 2:7). Moyo ndi wauzimu chifukwa unachokera kwa Mulungu, komanso ndi wachibadwidwe chifukwa umaonekera m’thupi langa. Ndikofunika kuti ndisunge moyo wanga wolumikizana ndi Mzimu wa Mulungu, wopanda chodetsa chilichonse.
Ndiyenera kukhala m’chiyero kuti tsiku lina ndikadzasiya dziko lapansi, moyo wanga udzakhala ndi moyo wosatha Kumwamba pamodzi ndi Ambuye Yesu. Mulungu safuna kuti moyo wanga utaike. Ndiyenera kuyenda m’zipatso za Mzimu, osati kukhutiritsa zilakolako za thupi langa, kuti ndikapeze chipulumutso ndikakhale Kumwamba pamodzi ndi Khristu.
Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake?
dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.
Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Tulutseni m'ndende kuti ndizitamanda dzina lanu. Anthu anu adzandizungulira, chifukwa Inu mwandichitira zabwino zambiri.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika.
Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
Ndidzatsitsimutsa anthu ofooka, ndipo anthu anjala ndidzaŵadyetsa chakudya nadzakhuta.”
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Bwerani, Inu Chauta, mudzandilanditse. Mundipulumutse chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Mau a Chauta ndi aŵa, “Imani pa mphambano, ndipo mupenye. Mufunse kumene kuli njira zakale ndi kumene kuli njira yabwino. Tsono mutsate njira yabwinoyo, ndipo mudzakhala pa mtendere. Koma inuyo mudati, ‘Sitidzaitsata.’
Moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa mwana ndi wanga, wa bambo ndi wanganso. Munthu amene wachimwa, ndiye amene adzafe.
Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?
Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga. Kunyoza kwa adani anga kumandipweteka ngati bala lofa nalo la m'thupi mwanga, akamandifunsa nthaŵi zonse kuti, “Mulungu wako ali kuti?” Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Mulungu, Mulungu wamoyo. Kodi ndidzafika liti pamaso pa Mulungu?
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Tsono Chauta adatenga dothi pa nthaka, ndipo adaumba munthu ndi dothilo. Adamuuzira mpweya wopatsa moyo m'mphuno zake, ndipo munthuyo adakhala wamoyo.
Munthu wochimwa ndiye amene adzafe, osati wina. Mwana sadzafera machimo a bambo wake, ndipo bambo sadzafera machimo a mwana wake. Munthu wabwino adzakolola zipatso za ubwino wake. Munthu woipa adzakolola zipatso za kuipa kwake.
Komabe ndi Chauta yemwe amene adaafuna kuti amuzunze, ndipo adamsautsadi. Iye adapereka moyo wake kuti ukhale nsembe yokhululukira machimo. Choncho adzaona zidzukulu zake, adzakhala ndi moyo wautali, ndipo chifuniro cha Chauta chidzachitika mwa iye.
Zitatha izi, Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu. Ndipo ndidaona kunsi kwa guwa lansembe mizimu ya anthu amene adaphedwa chifukwa cha kulalika mau a Mulungu, ndiponso chifukwa chochitira mauwo umboni wamphamvu.
Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza.
Pamenepo thupi lidzabwerera ku dothi monga m'mene lidaaliri, ndipo mzimu udzabwerera kwa Mulungu amene adaupereka.
Koma Mulungu adamuuza kuti, ‘Wopusawe! Usiku womwe uno akulanda moyo wako. Nanga zonse zimene wadzisungirazi zidzakhala za yani?’ ”
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Mtima wanga wonse umalakalaka Inu usiku, mzimu wanga m'kati mwa ine umakufunafunani. Pamene muweruza dziko lapansi, anthu onse okhalamo amaphunzira chilungamo.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Pambuyo pake ndidaona mipando yachifumu, ndipo okhala pamipandopo adapatsidwa mphamvu zoweruzira milandu. Ndidaonanso mizimu ya anthu amene adaŵadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mau a Mulungu. Iwowo sadapembedze nao chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo adakana kulembedwa chizindikiro chija pa mphumi kapena pa dzanja. Adakhalanso ndi moyo nkumalamulira pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi.
Thupi limene timakhalamo pansi pano lili ngati msasa chabe. Koma tikudziŵa kuti msasawu ukadzapasuka, tidzakhala ndi nyumba ina imene Mulungu adatikonzera Kumwamba. Nyumbayo ndi yosamangidwa ndi manja a anthu, ndipo ndi yamuyaya.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Kwa inetu moyo ndi Khristu amene, ndipo nayonso imfa ili ndi phindu. Koma ngati kukhalabe moyo kungandipatse mwai woti ndigwire ntchito yoonetsa zipatso, sindidziŵa kaya ndingasankhe chiti. Ndagwira njakata. Kwinaku ndikulakalaka kuti ndisiye moyo uno ndikakhale pamodzi ndi Khristu, pakuti chimenechi ndiye chondikomera koposa.