Malooto ndi chinthu chofunika kwambiri pa umoyo wathu. M’Baibulo muli nkhani zambiri zokhudza maloto ndi tanthauzo lake laulosi. Kuyambira maloto a Yosefe m’Chipangano Chakale mpaka masomphenya a atumwi m’Chipangano Chatsopano, mawu a Mulungu amatiwonetsa kuti maloto akhoza kukhala njira imene Mulungu amalankhulirana ndi anthu ake.
Nthawi zambiri, maloto amatipatsa chidziwitso chozama. Mulungu angagwiritse ntchito maloto kuti atiuze chifuniro chake, kutitsogolera, komanso kutichenjeza. Komabe, ngakhale kuti Mulungu angalankhule nafe kudzera m’maloto, tiyenera kuzindikira bwino uthenga wake.
Baibulo limatiphunzitsa kukhala anzeru ndi kufunafuna chitsogozo cha Mzimu Woyera kuti timvetse bwino maloto athu. Choncho, kumbukira kuti maloto ndi ofunika pa moyo wathu ndi kuyenda kwathu ndi Mulungu.
Monga okhulupirira, tiyenera kukhala okonzeka kumva Mulungu akulankhula nafe kudzera m’maloto. Monga Yosefe ndi atumwi, tiyenera kufunafuna nzeru kuti timvetse bwino uthenga umene timalandira m’maloto athu, ndipo koposa zonse, kudalira chitsogozo cha Mzimu Woyera.
Chidziwitso chimenechi chitithandize kufunafuna Mulungu, kulakalaka ubwenzi wozama ndi Iye, ndi kuyenda momvera chifuniro chake.
“Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika pamene ndidzatsitsa mzimu wanga pa mtundu uliwonse wa anthu. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa. Nkhalamba zanu zidzalota maloto, ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya.
Akulingalira zimenezi, mngelo wa Ambuye adamuwonekera m'maloto, namuuza kuti, “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kumtenga Maria, mkazi wakoyu. Pathupi ali napopa padachitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
“Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika pamene ndidzatsitsa mzimu wanga pa mtundu uliwonse wa anthu. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa. Nkhalamba zanu zidzalota maloto, ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya. Masiku amenewo, ndidzatsitsa mzimu wanga ngakhale pa akapolo ndi pa adzakazi omwe.
Onsewo adayankha kuti, “Aŵirife tonse talota maloto usiku wapitawu, ndipo pano palibe ndi mmodzi yemwe wotha kutimasulira malotowo.” Apo Yosefe adaŵauza kuti, “Ndi Mulungu yekhatu amene amapatsa nzeru zomasulira maloto. Tandiwuzani maloto anuwo.”
“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto. Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu.
Chauta adati, “Imvani mau anga. Pakakhala mneneri pakati panupa, Ine Chauta ndimadziwonetsa kwa munthuyo m'masomphenya, ndimalankhula naye m'maloto.
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.
Tsiku lina Yosefe adalota maloto, nafotokozera abale ake malotowo. Zitatero, adadana naye kopambana kale. Iye adaŵauza kuti “Mverani maloto omwe ndalota. Tonsefe tinali m'munda, ndipo tinalikumanga mitolo yatirigu. Tilikumanga chomwecho, mtolo wanga unaimirira. Tsono mitolo yanu inauzungulira mtolo wangawo ndi kumauŵeramira.”
Labani Mwaramu uja adalota maloto usiku womwewo. Mulungu adadza namuuza kuti, “Usamuwopseze Yakobe mwa njira iliyonse.”
Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo. Chauta adaimirira pambali pake namuuza kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa Abrahamu ndi wa Isaki. Dziko ukugonapoli ndidzakupatsa iwe pamodzi ndi zidzukulu zako. Zidzukulu zakozo zidzachuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. Zidzabalalikira ku mbali zonse: kuzambwe, kuvuma, kumpoto ndi kumwera. Ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadalitsidwa kudzera mwa iwe ndi zidzukulu zako. Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
Mwina mneneri kapena womasulira maloto adzaoneka pakati panupo, namanena kuti adzachita chizindikiro kapena chozizwitsa,
Tsiku lina dzuŵa litapendeka, nthaŵi ili ngati 3 koloko, adaona zinthu m'masomphenya. Adaona bwino ndithu mngelo wa Mulungu akubwera kwa iye nkunena kuti, “Kornelio!”
Tsono atafika pafupi, Gideoni adamva munthu akufotokozera mnzake maloto ake. Ankati, “Ine ndalota maloto. Ndinangoona mtanda wa buledi wabarele ukugubuduzika kutsikira ku zithando za Amidiyani ndipo unafika mpaka ku chithando china nuchigunda, kotero kuti chinagwa ndipo nkuphwasukaphwasuka.”
Buku lino likufotokoza zimene Yesu Khristu adaulula. Mulungu adampatsa zimenezi kuti aonetse atumiki a Mulunguyo zomwe zikuyenera kudzachitika posachedwa. Khristu pofuna kudziŵitsa zinthuzo mtumiki wake Yohane, adachita kutuma mngelo wake kwa iye.
Pambuyo pake mngelo uja adandiwuza kuti, “Mau aŵa ndi oona ndiponso oyenera kuŵakhulupirira. Ndipo Ambuye Mulungu amene amalankhulitsa aneneri, adatuma mngelo wao kuti aonetse atumiki ao zimene zidzachitike posachedwa.”
Gideoni atamva kufotokoza kwa malotowo pamodzi ndi kumasulira kwake, adagwada pansi nathokoza Mulungu, ndipo adabwerera ku zithando za Aisraele naŵauza kuti, “Dzukani, Chauta wapereka Amidiyani m'manja mwanu.”
Adapempha nzeru kwa Chauta, koma sadamuyankhe ngakhale podzera m'maloto, kapena mwa Urimu kapena mwa aneneri.
Aneneri ameneŵa amakhulupirira kuti anthu anga adzandiiŵala akamamva zamalotozo, monga momwe makolo ao adaiŵalira dzina langa pomapembedza Baala.
Ku Gibiyoniko Chauta adamuwonekera Solomoni m'maloto usiku, namuuza kuti, “Upemphe chilichonse chimene ufuna kuti ndikupatse.”
Ndikuŵakana aneneri amene amalota zabodza, namasimbira anthu anga ndi kumaŵasokeza ndi mabodza aowo. Sindidaŵatume ndine kapena kuŵalamula, ndipo sathandiza anthu mpang'ono pomwe,” akuterotu Chauta.
Ngati mneneri walota maloto, afotokoze maloto akewo. Koma amene ali ndi mau anga, alalike mau angawo moona. Kodi mungu ungafanane ndi tirigu?” Akuterotu Chauta.
Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo. M'maloto, m'masomphenya usiku, pamene anthu ali m'tulo tofa nato, pamene akungosinza chabe pa bedi, pamenepo amaŵatsekula makutu anthuwo, naŵaopsa ndi machenjezo.
Pamenepo ndidadzuka nkudzati maso mwalamwala, ndipo ndidaona kuti ai ndidaatipha tulo.
Pambuyo pake mngelo amene ankalankhula nane uja adabweranso nandidzutsa monga momwe amadzutsira munthu amene ali m'tulo. Pakali pano anthuwo ndi okhumudwa kuwona kuti ntchito sikufulumira. Koma akadzamuwona Zerubabele atatenga mwala wotsiriza uja m'manja mwake, pamenepo adzakondwa. “Nyale zisanu ndi ziŵiri ndi maso a Chauta amene akunka nayang'anayang'ana pa dziko lonse lapansi.” Tsono ndidamufunsa munthuyo kuti, “Nanga mitengo iŵiri ya olivi ili kumanja ndi kumanzere kwa choikaponyalecho ikutanthauza chiyani?” Ndidamufunsanso kuti, “Pambali pa mipopi iŵiri yagolide yodzera mafutayo pali nthambi ziŵiri za mtengo wa olivi, zimenezi zikutanthauza chiyani?” Iye adati, “Monga iwe zimenezi sukuzidziŵa?” Ine ndidayankha kuti, “Inde, mbuye wanga, sindikuzidziŵa.” Tsono iye adati, “Ameneŵa ndi anthu aŵiri odzozedwa aja, amene amatumikira Chauta, Ambuye a dziko lonse lapansi.” Adandifunsa kuti, “Ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona choikaponyale, chonse chagolide, ndi mbale pamwamba pake. Chili ndi nyale zisanu ndi ziŵiri, iliyonse ili ndi ziboo zisanu ndi ziŵiri zoloŵetsamo zingwe zoyatsira.
Mulungu adaŵachenjeza m'maloto kuti asadzerekonso kwa Herode kuja. Motero adadzera njira ina pobwerera kwao.
Ndipo adalota akuwona makwerero ochoka pansi mpaka kukafika kumwamba. Angelo a Mulungu ankatsika ndi kumakwera pa makwererowo. Chauta adaimirira pambali pake namuuza kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wa Abrahamu ndi wa Isaki. Dziko ukugonapoli ndidzakupatsa iwe pamodzi ndi zidzukulu zako.
Atapita akatswiri a nyenyezi aja, mngelo wa Ambuye adaonekera Yosefe m'maloto. Adamuuza kuti, “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mai wake, uthaŵire ku Ejipito. Ukakhale kumeneko mpaka ndidzakuuze, popeza kuti Herode azidzafunafuna mwanayu kuti amuphe.”
Tsiku lachisanu la mwezi wachinai, chaka cha 30, ndidaakhala pamodzi ndi akapolo a ku Yuda pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Tsono Kumwamba kudatsekuka, ndipo ndidaona maonekedwe a Mulungu m'masomphenya.
Mnyamata uja Samuele ankatumikira Chauta, ndipo Eli ankamuyang'anira. Masiku amenewo mau a Chauta sankamveka kaŵirikaŵiri, ndipo kuwona zinthu m'masomphenya sikunkachitikanso kaŵirikaŵiri.
Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.”
Tsono ku Damasikoko kunali wophunzira wina, dzina lake Ananiya. Iyeyu adaaona m'masomphenya Ambuye akumuitana kuti, “Ananiya!” Iye adati, “Ee, Ambuye.” Apo Ambuye adamuuza kuti, “Nyamuka, upite ku mseu wa mumzindamu umene amati, ‘Njira Yolunjika.’ Ndipo ku nyumba ya Yudasi ukafune munthu wina wa ku Tariso, dzina lake Saulo. Panopa akupemphera, ndipo waona m'masomphenya munthu wina, dzina lake Ananiya, akuloŵa ndi kumsanjika manja kuti apenyenso.”
Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo. Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’ Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.” Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti, “Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo, ulembepo kuti, ‘Ya Ayuda ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ina, ulembepo kuti, ‘Ya Aefuremu, ndiye kuti fuko la Yosefe, ndi Aisraele ogwirizana nawo.’ Tsono utenge ndodo ziŵirizo ndi kuzilumikiza kuti zikhale ngati ndodo imodzi. Anthu akwanu akakufunsa tanthauzo lake la zimenezi, uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndili pafupi kutenga ndodo ya Yosefe, imene ili m'manja mwa Efuremu, pamodzi ndi Aisraele ogwirizana nawo, ndiilumikiza ndi ndodo ya Yuda kuti zikhale ndodo imodzi. Ndipo zidzakhaladi imodzi m'manja mwanga. Chauta adandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo analitu ochuluka kwambiri m'chigwa chonsecho, ndipo anali ochita kuti gwaa kuuma kwake. Ndodo zimene ukulembapozo zikadzakhala m'manja mwako, pamaso pa anthu onse, pamenepo udzaŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndidzaŵaitana Aisraele kuchokera ku malo ao aukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mphepo zinai ndi kuŵabwezera ku dziko lao. Ndidzaŵasandutsa mtundu umodzi m'dzikomo, ku mapiri a Israele, ndipo adzakhala ndi mfumu imodzi yokha. Sadzakhalanso mitundu iŵiri ya anthu kapena kugaŵikana maufumu aŵiri. Sadzadziipitsanso ndi mafano ao ndi zinthu zina zonyansa, kapena ndi zochimwa zao zina zilizonse. Ndidzaŵapulumutsa ku machimo ao onse, ndipo ndidzaŵayeretsa. Motero iwowo adzakhala anthu anga, ndipo Ineyo ndidzakhala Mulungu wao. “Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yao, motero onsewo adzakhala ndi mbusa mmodzi. Adzatsata malamulo anga, adzamvera mosamala malangizo anga. Adzakhala m'dziko limene ndidapatsa mtumiki wanga Yakobe, kumene ankakhala makolo anu. Iwowo, pamodzi ndi ana ao ndi zidzukulu zao, adzakhala kumeneko mpaka muyaya. Ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri wao mpaka muyaya. Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya. Nyumba yanga idzakhala pakati pao. Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Apo anthu a mitundu ina adzadziŵa kuti Ine Chauta Aisraele ndimaŵasandutsa oyera, chifukwa chakuti Nyumba yanga ili pakati pao mpaka muyaya.” Tsono adandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa ameneŵa angathe kukhalanso ndi moyo?” Ine ndidati, “Ambuye Chauta, ndi Inuyo amene mukudziŵa zimenezi.”
Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.
Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.
Makamu ndi makamu a anthu ali m'Chigwa cha Chiweruzo. Ndithu tsiku la Chauta layandikira m'Chigwa cha Chiweruzo.
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona pakhomo potsekuka Kumwamba. Ndipo ndidamva wina akulankhula nane ndi liwu lomwe ndidaamva poyamba lija, limene linkamveka ngati kulira kwa lipenga. Adandiwuza kuti, “Bwera Kumwamba kuno, ndidzakuwonetse zimene ziyenera kuchitika bwino lino.” Pamene zikuchitika zimenezi, Akuluakulu 24 aja amadzigwetsa pamaso pa wokhala pa mpando wachifumuyo, ndi kumpembedza wokhala ndi moyo wamuyayayo. Ndipo amaponya pansi zisoti zao zaufumu patsogolo pa mpando wachifumuwo ndi kunena kuti, “Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.” Nthaŵi yomweyo ndidagwidwa ndi Mzimu Woyera. Kumwambako ndidaona mpando wachifumu, wina atakhalapo pampandopo.
Kwa inu zinthu zilizonse zoziwona m'masomphenya zakhala zobisika ngati mau a m'buku lomatirira. Buku limenelo atapatsa wina wodziŵa kuŵerenga kuti aŵerenge, iye adzati, “Sindingathe, chifukwa choti nlomatidwa.”
Zitatha izi, Chauta adaonekera Abramu m'masomphenya namuuza kuti, “Usachite mantha Abramu, Ine ndili ngati chishango chako chokutchinjiriza. Mphotho yako idzakhala yaikulu.”
“Usiku wathawu ndinaona zinthu m'masomphenya. Ndinaona munthu atakwera pa kavalo wofiira. Munthuyo anaima pa timitengo tazitsamba m'chigwa. Kumbuyo kwake kunalinso akavalo, ena ofiira, ena odera, ena oyera.
Tsono Mulungu adamuwonekera usiku m'maloto nati, “Ufatu iwe chifukwa mkazi watengayu ndi wokwatiwa.”
Patapita zaka ziŵiri, Farao adaalota kuti waimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo. Paja inu mfumu mudaatipsera mtima antchitofe. Ndipo ine ndi wophika buledi tonse mudaatitsekera m'ndende, m'nyumba ya mkulu wa alonda. Tsono usiku wina, aŵirife tidaalota maloto. Aliyense mwa ife anali atalota maloto ake, a tanthauzo lakelake. M'nyumba momwemo munali mnyamata wina Wachihebri, mtumiki wa mkulu wa alonda a m'ndende muja. Iyeyo adammasulira bwino aliyense mwa ife tanthauzo la maloto akewo. Ndipo zidachitikadi monga momwe adaatimasulira. Ine ndidabwerera pa ntchito yanga, koma wophika buledi uja adampachika pa mtengo.” Tsono Farao adaitanitsa Yosefe, ndipo adamtulutsa msanga kundendeko. Iyeyo atameta bwino ndi kusintha zovala, adapita kwa Farao kuja. Farao adauza Yosefe kuti, “Ine ndidalota maloto, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akutha kumasula malotowo. Tsono adandiwuza kuti iwe ukamva maloto, ati umadziŵa kumasula kwake.” Yosefe adayankha kuti, “Sindine ai, koma Mulungu ndiye amene adzatha kuimasulira mfumu maloto ameneŵa.” Apo Farao adati, “Ine ndidaalota ntaimirira pamphepete pa mtsinje wa Nailo. Nthaŵi yomweyo ndidangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zitatuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Kenaka padatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi za maonekedwe oipa kwambiri. Ng'ombe zimenezo zinali zoonda kwambiri kupambana ng'ombe zoonda zonse za m'dziko lonse la Ejipito. Nthaŵi yomweyo adangoona ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepa bwino zikutuluka mumtsinjemo, nkuyamba kudya msipu wam'mabango. Ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Koma zitadya zinzakezo, palibe ndi mmodzi yemwe akadazindikira, popeza kuti ng'ombe zoondazo sizidasinthike konse kaonekedwe kake, koma zidangokhala zoonda ndithu monga kale. Tsono ndidadzuka. Nditagonanso ndidalota ntaona ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zakucha ndi zokhwima bwino zitabala pa mphesi imodzi. Pomwepo padaphukanso ngala zina zatirigu zisanu ndi ziŵiri zofwapa, zopserera ndi mphepo yakuvuma. Ngala zofwapazo zidameza zinzake zokhwima zija. Tsono ndidafotokozera amatsenga maloto ameneŵa, koma palibe ndi mmodzi yemwe amene adatha kundimasulira.” Apo Yosefe adauza Farao kuti, “Maloto onse aŵiriŵa ali ndi tanthauzo limodzi lokha. Mulungu wakuuziranitu zimene adzachite. Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zonenepazo ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Ndipo ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zokhwimazo nazonso ndi zaka zisanu ndi ziŵiri. Kumasula kwake nkumodzi. Ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zoonda zimene zidabwera pambuyo zija, ndiponso ngala zatirigu zisanu ndi ziŵiri zopserera ndi mphepo yakuvuma zija, ndi zaka zisanu ndi ziŵiri za njala. Tsono monga momwe ndanenera, ndiye kuti Mulungu wakuuziranitu zomwe adzachite. Padzakhala zaka zisanu ndi ziŵiri za dzinthu dzambiri m'dziko lonse la Ejipito. Kenaka mumtsinje momwemo mudatulukanso ng'ombe zina zisanu ndi ziŵiri zoonda ndi zofooka, zimene zidaima pa mtunda pafupi ndi ng'ombe zina zija. Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko. Zaka zonse zija za dzinthu dzambiri sizidzakumbukikanso, chifukwa njala imene idzabwereyo idzakhala yoopsa. Poti inu Farao mwalota kaŵiri maloto okhaokhaŵa, zikuwonetsa kuti Mulungu ndiye amene wakonza zimenezi, ndipo azichitadi posachedwa. Tsopano inu mfumu sankhulani munthu wodziŵa zinthu ndi wanzeru, mumpatse ulamuliro pa dziko lonse la Ejipito. Musankhenso anthu akuluakulu m'dziko lonse lino, ndipo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse za zokolola, azichiika padera pa zaka zisanu ndi ziŵiri za chakudya chochuluka. Asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zadzinthu zimene zikubwerazi. Azichita zonsezi ndi ulamuliro wanu, ndipo aziika tirigu padera m'mizinda yonse ndi kumsunga bwino. Chakudya chimenecho chidzakhala chakudya cha nthaŵi ya njala ya zaka zisanu ndi ziŵiri imene idzabwere ndithu mu Ejipito muno, kuti choncho anthu a ku Ejipito asadzafe ndi njala.” Farao pamodzi ndi nduna zake adavomereza zonse zimene adaanena Yosefe. Tsono Farao adafunsa nduna zakezo kuti, “Kodi tingampeze kuti munthu wina woposa uyu amene ali ndi mzimu wa Mulungu?” Motero Farao adauza Yosefe kuti, “Popeza kuti Mulungu wakuwonetsa zonsezi, palibenso wina aliyense wodziŵa zinthu ndi wanzeru kupambana iweyo. Tsono ng'ombe zoondazo zidadya zinzake zonenepa zija. Pamenepo Farao adadzuka.
Mngelo wa Chauta adamuwonekera ngati malaŵi a moto umene unkayaka m'chitsamba. Mose atapenya, adaona kuti chitsamba chili moto laŵilaŵi, koma osapsa.
Tsono atafika pafupi, Gideoni adamva munthu akufotokozera mnzake maloto ake. Ankati, “Ine ndalota maloto. Ndinangoona mtanda wa buledi wabarele ukugubuduzika kutsikira ku zithando za Amidiyani ndipo unafika mpaka ku chithando china nuchigunda, kotero kuti chinagwa ndipo nkuphwasukaphwasuka.” Ndipo mnzake uja adayankha kuti, “Zimenezi si kanthu kena koma nkhondo ya Gideoni, mwana wa Yoasi, munthu wa ku Israele. Mulungu wapereka Midiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse m'manja mwake.” Gideoni atamva kufotokoza kwa malotowo pamodzi ndi kumasulira kwake, adagwada pansi nathokoza Mulungu, ndipo adabwerera ku zithando za Aisraele naŵauza kuti, “Dzukani, Chauta wapereka Amidiyani m'manja mwanu.”
Ndiyenera kunyada, tsono kunyada kwake nkopanda phindu. Komabe ndimati ndikambe za zimene Ambuye adandiwonetsa m'masomphenya, ndiponso za zimene adandiwululira. Tsono ndimakondwera pamene ndili wofooka, pamene anthu andinyoza, namandizunza, ndiponso pamene ndimva zoŵaŵa ndi kusautsidwa chifukwa cha Khristu. Pakuti pamene ndili wofooka, mpamene ndili ndi mphamvu. Ndasanduka wopusa, koma ndinu mwandichititsa zimenezi. Ndinu mukadayenera kundichitira umboni. Pakuti ngakhale sindili kanthu, atumwi anu apamwamba aja sandipambana pa kanthu kalikonse. Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu. Kodi nchiyani chimene ndidachitira mipingo ina, inu osakuchitirani, kupatula chokhachi chakuti sindidakhale ngati katundu wokulemetsani? Ndikhululukireni kulakwa kwangaku. Aka nkachitatu tsopano kukonzeka kuti ndibwere kwanuko, ndipo sindidzakhala ngati katundu wokulemetsani. Sindikufuna zinthu zanu, koma ndikufuna inuyo. Pakuti si udindo wa ana kusungira makolo ao chuma, koma ndi udindo wa makolo kusungira ana ao chuma. Kunena za ine, ndidzakondwa kupereka zanga zonse, ndi kutaya ngakhale moyo wanga womwe chifukwa cha inu. Ine ndikamakukondani kwambiri chotere, kodi ndiye kuti inuyo muzingondikonda pang'ono? Momwemo tsono, mudzandivomereza kuti ine sindidakhale ngati katundu wokulemetsani. Koma kapena wina adzati popeza kuti ndine wochenjera, ndidakuchenjeretsani. Kodi kapena ndidakuchenjererani mwa aliyense amene ndidamtuma kwa inu? Ndidapempha Tito kuti apite, kenaka ndidatuma mbale wathu wina pamodzi naye. Kodi Titoyo adakuchenjererani? Kodi suja iye ndi ine tinkachita zonse ndi mtima umodzi? Suja tinkatsata njira imodzimodzi? Kapena mwakhala mukuganiza kuti tikuyesa kudziteteza pamaso panu. Iyai, koma pokhala pamaso pa Mulungu, timalankhula mwa Khristu, ndipo pa zonsezi, okondedwa anga, timangofuna kukulimbitsani mtima. Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi. Ndikuwopa kuti ndikadzabwera kwanuko, mwina nkudzakupezani muli osiyana ndi m'mene ndikadafunira. Ndikuwopa kuti mwina inunso nkudzandipeza ine wosiyana ndi m'mene mukadafunira. Ndikuwopanso kuti mwina ine nkudzapeza kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusinjirirana, ugogodi, kudzitukumula, ndiponso chisokonezo. Ndikuwopa kuti ndikadzabweranso kwanuko, mwina Mulungu wanga nkudzandinyazitsa pamaso panu, ineyo nkudzalira misozi chifukwa cha ambiri amene adachimwa kale, ndipo sadalape zonyansa zao, dama lao, ndi mayendedwe ao oipa. Ndikudziŵa kuti munthuyo adaatengedwa mwadzidzidzi kupita ku Paradizo. Sindikudziŵa ngati zimenezi zidaachitika ali m'thupi, kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi. Kumeneko munthuyo adamva zinthu zosasimbika, zinthu zimene munthu sangazilankhule.
Tsono mngelo wa Ambuye adaonekera Zakariya. Mngeloyo adaaimirira ku dzanja lamanja la guwa lofukizirapo lubani.
Tsiku lina usiku Ambuye adaonekera Paulo m'masomphenya namuuza kuti, “Usaope, koma upitirire kulalika, osakhala chete ai,
Adadzipereka kwa Mulungu pa nthaŵi ya Zekariya amene ankamphunzitsa Uziyayo kuti azilemekeza Mulungu. Ndipo nthaŵi zonse pamene ankadzipereka kwa Chauta, Mulungu ankamupezetsa bwino.
Ndidaonanso zinthu m'masomphenya: ndidaona munthu atatenga chingwe choyesera m'manja mwake. “Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta. Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu. Iyeyo adzamtenganso Yuda kuti akhale chuma chake m'dziko lopatulika, ndipo Yerusalemu adzakhala mzinda wake wapamtima. Anthu nonsenu, ingokhalani chete pamaso pa Chauta, chifukwa wadzambatuka ndi kutuluka ku malo ake oyera. Ndidamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti?” Iye adandiyankha kuti, “Ndikukayesa mzinda wa Yerusalemu kuti ndidziŵe kutalika kwa muufupi mwake ndi m'litali mwake.”
Pambuyo pake kudaoneka chizindikiro chachikulu kuthambo: mai atavala dzuŵa, mapazi ake ataponda pa mwezi, pamutu pake pali chisoti chaufumu cha nyenyezi khumi ndi ziŵiri.
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Aneneri asakunyengeni, ngakhale oombeza amene ali pakati panu, ndipo musamvere maloto ao. Ndithu amakuloserani zabodza m'dzina langa, Ine sindidaŵatume,’ ” akutero Chauta.
Adatambalitsa chinthu chonga dzanja nandigwira tsumba. Pomwepo mzimu wa Mulungu udandikweza mu mlengalenga. Ndipo ngati ndikuwona Mulungu kutulo, udapita nane ku Yerusalemu, nundiika pa khoma loloŵera ku chipata cham'kati choyang'ana kumpoto. Kumeneko kunali fano loputa mkwiyo wa Mulungu. Ulemerero wa Mulungu wa Israele udaoneka kumeneko, monga momwe ndidaaonera kale m'masomphenya m'chigwa muja.
Koma Stefano, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adayang'ana kumwamba naona ulemerero wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono adati, “Onani! Ndikuwona Kumwamba kotsekuka, ndipo Mwana wa Munthu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.”
“Koma za tsiku lake kapena nthaŵi yake, palibe amene amadziŵa. Angelo omwe akumwamba sadziŵa. Ngakhale Ineyo Mwanane sindidziŵa; amadziŵa ndi Atate okha basi.
Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima, uŵagonthetse makutu, ndipo uŵatseke m'maso, kuti angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mitima yao, kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.” Pamenepo ndidafunsa kuti, “Zimenezo ndi mpaka liti, Inu Ambuye?” Iwo adati: “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja, mpaka nyumba zitasoŵa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu. Ine anthuŵa ndidzaŵasamutsira kutali, ndipo dziko lidzakhala thengo. Tsono ngakhale chigawo chachikhumi cha anthu chitsaleko m'dzikomo, nachonso chidzayatsidwa moto. Koma monga mitengo ya muŵanga ndi ya thundu imasiya chitsa akaidula, chonchonso mbeu yoyera ija idzatsalira ngati chitsa chotsala m'dziko.” Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: aŵiri ophimbira kumaso, aŵiri ophimbira mapazi, aŵiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.” Chifukwa cha kufuulako maziko a zitseko ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m'Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha.
Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu udandinyamula nukandifikitsa kwa akapolo ku dziko la Babiloni. Zonsezi zidachitika m'masomphenya, monga momwe Mzimu wa Mulungu udaandiwonetsera. Kenaka zinthu zimene ndinkaziwonazo zidayamba kuzimirira.
Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike.
Choyamba mumvetse izi: pa masiku otsiriza kudzafika anthu olalata, otsata zilakolako zao zoipa. Azidzalalata nkumanena kuti, “Kodi suja Ambuye adalonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nkale adamwalira makolo athu, koma zonse zili monga momwe Mulungu adazilengera poyamba paja.”
Pambuyo pake ndidaona Mwanawankhosa uja akumatula chimodzi mwa zimatiro zisanu ndi ziŵiri zija. Ndipo ndidamva chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chikunena ndi liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” Mizimuyo idafuula mokweza mau kuti, “Ambuye, Inu ndinu Mfumu yathu yoyera ndi yoona. Mudzaŵalekerera mpaka liti osaŵaimba mlandu ndi kuŵalanga anthu aja okhala pansi pano amene adatipha?” Apo aliyense adapatsidwa mkanjo woyera, ndipo adamva mau akuti, “Bapumulani pang'ono mpaka chitakwanira chiŵerengero chathunthu cha atumiki anzanu ndi abale anu, amene nawonso ayenera kuphedwa monga inu nomwe.” Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho. Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake. Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri. Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo. Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?” Nditayang'ana, ndidaona kavalo woyera. Wokwerapo wake anali ndi uta, ndipo adaapatsidwa chisoti chaufumu. Adatulukira ngati wogonjetsa kuchokera kumwamba, kuti akagonjetsenso ena pa dziko lapansi.
Mngelo wachitatu adaliza lipenga lake. Atatero chinyenyezi choyaka ngati muuni chidagwa kuchokera kuthambo. Chidagwera pa chimodzi mwa zigawo zitatu za mitsinje, ndi pa akasupe.
“Pa nthaŵi imeneyo za Ufumu wakumwamba zidzafanafana ndi zimene zidaachitikira anamwali khumi. Iwowo adaatenga nyale zao nkumakachingamira mkwati. Pamene ankakagula, mkwati adafika. Amene anali okonzekeratu aja adaloŵa naye pamodzi m'nyumba yaphwando; pambuyo pake adatseka chitseko. “Kenaka m'mbuyomwalendo anamwali ena aja nawonso adabwera nati, ‘Bwana, Bwana, titsekulireni!’ Koma mkwatiyo adati, ‘Pepani, sindikukudziŵani!’ ” Pomaliza Yesu adati, “Ndiyetu inu, muzikhala maso, poti simudziŵa tsiku lake kapena nthaŵi yake.”
Lirani kwamphamvu pakuti tsiku la Chauta layandikira. Likubwera ndi chiwonongeko chochokera kwa Mphambe.
Tsono mngelo uja adanditenga chamumzimu kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndidaona mkazi atakhala pa chilombo chofiira. Pathupi ponse chilombocho chidaalembedwa maina onyozera Mulungu. Chinali ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.
Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona mtambo woyera. Pamtambopo padaakhala wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chisoti chaufumu chagolide, m'manjamu ali ndi chikwakwa chakuthwa. Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.” Pamenepo wokhala pamtambo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula dzinthu dzonse dza pa dziko lapansi.
Chauta adandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nthambi ya mtowo.” Chauta adati, “Waona bwino. Ineyo ndikuwonetsetsa kuti zichitikedi zimene ndidanena.”
Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu. Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya. Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo. Adagwira Chinjoka chija, ndiye kuti njoka yakale ija yotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana, nachimanga zaka chikwi chimodzi. Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono.
Dzombelo linkaoneka ngati akavalo okonzekera nkhondo. Pamitu pake panali ngati zisoti zaufumu zagolide, nkhope zake ngati za anthu. Tsitsi lake linali litalilitali ngati la azimai, mano ake ngati a mkango.
Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.
Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”
Pa masiku akudzaŵa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.
Lizani lipenga ku Ziyoni. Fuulani mochenjeza pa phiri langa loyera. Onse okhala m'dziko anjenjemere, pakuti tsiku la Chauta likufika, layandikira. Dziko lapansi likugwedezeka pamene iwo akuyandikira. Mlengalenga ukunjenjemera. Dzuŵa ndi mwezi zikuchita mdima, ndipo nyenyezi zikuleka kuŵala. Chauta akumveketsa liwu lake kutsogolo kwa gulu lake lankhondo. Gulu lake lankhondolo ndi lalikulu kwambiri. Wochitadi zimene Chauta akulamula, ngwamphamvu. Tsiku la Chauta ndi lalikulu ndi loopsa. Ndani angathe kupirira tsikulo? Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka. Mwina mwake adzasintha mtima ndi kuleka, ndipo adzatisiyira madalitso. Madalitsowo adzakhala a chopereka cha chakudya ndi chakumwa zopereka kwa Chauta, Mulungu wanu. Lizani lipenga ku Ziyoni. Lengezani mwambo wa kusala zakudya. Muitanitse msonkhano waukulu. Sonkhanitsani anthu pamodzi, muŵauze kuti adziyeretse. Sonkhanitsani akuluakulu, sonkhanitsani ana, sonkhanitsani ndi oyamwa omwe. Lamulani kuti nawonso akwati achoke m'chipinda mwao, abwere. Ansembe, amene ali atumiki a Chauta, azilira pakati pa guwa lansembe ndi khonde. Azinena kuti, “Inu Chauta, achitireni chifundo anthu anu. Musalole kuti ena aŵanyoze anthu anu osankhidwa. Anthu achikunja asaŵaseke pomafunsana kuti, ‘Ha, ali kuti Mulungu waoyo?’ ” Apo chikondi cha Chauta chidayaka ngati moto chifukwa cha dziko lake, ndipo adaŵachitira chifundo anthu ake. Chauta adaŵayankha anthu ake kuti, “Ndikutumizirani tirigu, vinyo ndi mafuta, ndipo mudzakhuta ndithu. Sindidzalolanso kuti akunja akunyozeni. Ndi tsiku lamdima ndi lachisoni, tsiku lamitambo ndi la mdima wandiweyani. Gulu la ankhondo amphamvu ochuluka langoti bii ngati mdima wokuta mapiri. Gulu lotere silinaonekepo nkale lonse, ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
Zitatha izi, ndidaona mngelo wina akutsika kuchokera Kumwamba. Anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo pa dziko lonse lapansi padayera chifukwa cha kuŵala kwake. Iwo adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka, iwe Babiloni, mzinda wotchuka, mzinda wamphamvu! Pa ora limodzi lokha chilango chako chakugwera.” Anthu amalonda a pa dziko lapansi adzalira ndi kumva naye chisoni kwambiri, pakuti palibenso wogula malonda ao. Palibenso wogula malonda ao a golide, siliva, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu; nsalu zoyera, zofiirira, zasilika ndi zamlangali; mitengo yamitundumitundu yonunkhira; zinthu zamitundumitundu zopangidwa ndi mnyanga wanjovu, ndiponso ndi mitengo yamtengowapatali; zinthu zopangidwa ndi mkuŵa, chitsulo ndi mwala wokongola; zokometsera chakudya zamitundumitundu, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta, ufa wosalala ndi tirigu, ng'ombe ndi nkhosa, akavalo ndi ngolo, akapolo ndi akaidi. Amalondawo adzamuuza kuti, “Zokoma zimene mtima wako unkalakalaka, zakuthera. Zachuma ndi zamakaka zako zonse zakutayikira, sudzazipezanso konse.” Anthu ogulitsa zimenezi, amene adalemerera pa iye, adzaima patali chifukwa cha kuwopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kumva chisoni kwambiri, ndipo adzanena kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu. Unkavala nsalu zoyera, zofiirira ndi zamlangali. Unkadzikongoletsa ndi golide, ndiponso ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. Koma pa ora limodzi lokha chuma chonsechi chaonongeka.” Onse oyendetsa zombo, onse oyenda pa nyanja, antchito apazombo, ndi onse oyendetsa malonda ao pa nyanja, adaima patali. Poona utsi uli phaphapha, mzindawo ulikupsa, adafuula kuti, “Ndi mzinda uti udalinganapo ndi mzinda wotchukawu?” Adadzithira fumbi kumutu, akulira ndi kumva chisoni kwambiri. Ankafuula kuti, “Uli ndi tsoka, uli ndi tsoka mzinda wotchukawu, mzinda umene anthu onse okhala ndi zombo zapanyanja adalemera nacho chuma chake. Koma pa ora limodzi lokha wasanduka bwinja.” Adafuula mokweza mau ndi kunena kuti, “Wagwa, wagwa Babiloni wotchuka uja! Wasanduka malo okhalamo mizimu yoipa, malo othaŵiramo mizimu yonse yonyansa, malo othaŵiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodedwa.
Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona namtindi wa angelo zikwizikwi pozungulira mpando wachifumu uja, Zamoyo zinai zija ndi Akuluakulu aja.
Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.”
Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro.
“Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.”
Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu.
Mkwiyo wa Chauta sudzachoka mpaka utatsiriza kuchita zonse zimene mtima wa Chautayo ukufuna. Mudzamvetsa zimenezi masiku akubwerawo.”
Aneneriwo amalankhula zonama, ndipo amalosa zabodza. Amanena kuti, ‘Akuterotu Chauta,’ pamene Chauta sadaŵatume konse. Komabe amayembekeza kuti zimene anenazo zidzachitika. Koma Ine ndikuti, Zimene inu aneneri mukuti mudaziwona m'masomphenya nzabodza. Ndipo kulosa kwanuko nkwabodza. Mumanena kuti ‘Akuterotu Chauta,’ ngakhale Ine sindidalankhule konse.”
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina wamphamvu akutsika kuchokera Kumwamba. Adaavala mtambo, ndipo pozungulira mutu wake panali utawaleza. Nkhope yake inali ngati dzuŵa, miyendo yake ngati mizati yamoto. Ndidalandira kampukutuko m'manja mwa mngelo uja, ndipo ndidadyadi. M'kamwamu kankazuna ngati uchi, koma nditakameza, m'mimbamu munkaŵaŵa. Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.” M'manja mwake anali ndi kampukutu kofutukula. Ndi mwendo wa ku dzanja lamanja adaaponda pa nyanja, ndi wakumanzere adaaponda pa mtunda.
Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku. Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino, ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse. Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu. Iye amene akukuitanani ngwokhulupirika, ndipo adzakuchitirani zimenezi. Abale, muzitipempherera. Abale onse muŵapatseko moni mwachikondi. M'dzina la Ambuye ndikukulamulani kuti kalatayi muŵaŵerengere abale onse. Ambuye athu Yesu Khristu akukomereni mtima. Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba. Koma inu abale, simuli m'chimbulimbuli kuti tsikulo nkukudzidzimutsani ngati mbala.
Pomaliza Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chiŵiri. Pamenepo onse Kumwamba adangoti chete pa hafu la ora.
Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho.
Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?”
“Nchifukwa chake, mfumu Agripa, sindidakane kumvera zimene Mulungu adandiwonetsa m'masomphenyazo.
Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.
“Tsono anthu a pa banja la Davide ndi anthu onse a ku Yerusalemu ndidzaŵadzaza ndi mtima wachifundo ndi wakupemphera. Motero adzati atamuyang'ana amene adambaya, adzamlira kwabasi monga muja amamlirira mwana akakhala mmodzi yekha. Adzamliradi kwambiri monga muja amamlirira mwana wachisambamu.
Mvetsetsani! Akubwera pa mitambo! Aliyense adzamuwona, amene adamubaya aja nawonso adzamuwona. Ndipo anthu a mitundu yonse pansi pano adzalira chifukwa cha Iye. Nzoonadi zimenezi. Ndithudi!
Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
Munthu Woipitsitsa uja adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzachita zamphamvu zosiyanasiyana, ndiponso zizindikiro ndi zozizwitsa zonyenga.
Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira.