Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


148 Mauthenga a Mulungu Okhudza Mphatso ya Chikhulupiriro

148 Mauthenga a Mulungu Okhudza Mphatso ya Chikhulupiriro


Ahebri 11:1

Tikati kukhulupirira, ndiye kuti kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndiponso kutsimikiza kuti zinthu zimene sitikuziwona zilipo ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:17

Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:9

Mzimu Woyera yemweyo amapatsa wina mphatso ya kukhulupirira, ndipo Mzimu Woyera mmodzi yemweyo amapatsa wina mphatso ya kuchiritsa matenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:20

Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:7

Pakuti timatsata chikhulupiriro, osati zopenya ndi maso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:23

Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:6

Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:21-22

Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati mukhala ndi chikhulupiriro, osakayika, mudzachita zimene ndauchita mkuyuzi. Koma si pokhapo ai, ngakhale mutauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ zidzachitikadi. Ngati mukhala ndi chikhulupiriro, zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu mudzalandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4

Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5-6

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera. Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:8-9

Iyeyu simudamuwone, komabe mumamkonda. Ngakhale simukumuwona tsopano, mumamkhulupirira ndipo mumakondwera ndi chimwemwe chachikulu ndi chosaneneka. Pakutero mukupata mphotho ya chikhulupiriro, ndiye kuti chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 11:22-24

Yesu adaŵayankha kuti, “Muzikhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo. Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:6

Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:20-21

Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu. Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:23

Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:17

Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:17

Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:22

Pamenepo Yesu adacheuka, naona maiyo, ndipo adati, “Limbani mtima mai, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani.” Nthaŵi yomweyo mai uja adachiradi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:40

Yesu adamufunsa kuti, “Kodi sindidakuuze kuti ukakhulupirira uwona ulemerero wa Mulungu?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:14

Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:7

Ndamenya nkhondo yabwino, ndatsiriza bwino mpikisano wa liŵiro, ndasunga chikhulupiriro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:3

Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:13

Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:3

Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:3

Tiyenera kuthokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale. Nkoyeneradi kutero, chifukwa chikhulupiriro chanu chikunka chikukulirakulira kwambiri pamodzi ndi kukondana kwanu pakati pa inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:12

Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:15

Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:29

Yesu adati, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiwona? Ngwodala amene amakhulupirira ngakhale sadaone.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:10

Yesu atamva zimenezi, adachita chidwi, ndipo adauza anthu amene ankamutsata aja kuti, “Kunena zoona, ngakhale pakati pa Aisraele sindidapeze chikhulupiriro chotere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:13-14

Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:50

Yesu atamva mauwo adauza Yairo kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupira, ndipo mwanayo akhalanso bwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:2

Paja ifenso tidaumva Uthenga Wabwino, monga iwo aja. Koma iwowo sadapindule nawo mau olalikidwawo, popeza kuti adangoŵamva, koma osaŵakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:4

Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:1

Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:12

Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:5

Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:28

Apo Yesu adati, “Inu mai, chikhulupiriro chanu nchachikulu. Zichitikedi zimene mukufuna.” Pompo mwana wake wamkazi uja adachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:3

Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:16

Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:29

Yesu adaŵayankha kuti, “Chimene Mulungu afuna kuti muchite nchakuti mundikhulupirire Ineyo amene Mulungu adandituma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:21

Kudzera mwa Iye mumakhulupirira Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa, namupatsa ulemerero. Ndipo choncho chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu zili mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:30

Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:50

Koma Yesu adauza maiyo kuti, “Chikhulupiriro chanu chakupulumutsani. Pitani ndi mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:13

Onseŵa adasunga chikhulupiriro chao mpaka kufa. Sadalandire zimene Mulungu adaaŵalonjeza, koma adangoziwonera chapatali ndi kuzikondwerera. Adaavomera kuti pansi pano analidi alendo osakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:8

Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:13

Malembo akuti, “Ndidakhulupirira, nchifukwa chake ndidalankhula.” Tsono popeza kuti ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timalankhula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:1

Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:2

adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:5

Mwa Khristuyo ife tidalandira mwai wokhala atumwi, kuti tithandize anthu a mitundu yonse kumkhulupirira ndi kumumvera, kuti choncho dzina lake lilemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:6

Pakuti pamene tili mwa Khristu Yesu, kuumbalidwa kapena kusaumbalidwa kulibe kanthu, chachikulu nchakuti munthu akhale ndi chikhulupiriro chogwira ntchito mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:2

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:36

Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:16

Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:28

Paja timaona kuti munthu amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, osati pakutsata Malamulo ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:2

Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:24

Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3-4

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu. Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:2

Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:45

Ndinu odala chifukwa mudakhulupirira kuti zimene Ambuye adakuuzani, zidzachitadi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:14

Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:31

Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:12

Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:12

Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:10

Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26

Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:2

“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:12

Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:33-34

Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa, ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:4

Mau a Chauta ndi olungama, zochita zake zonse amazichita mokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1-2

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:42

Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:36

Koma Yesu sadasamale zimene anthuwo ankanena. Adauza mkulu uja kuti, “Musaope ai, inu mungokhulupirira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:13

Choncho pakali pano zilipo zinthu zitatuzi: chikhulupiriro, chiyembekezo ndi chikondi. Koma mwa zonsezi chopambana ndi chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 7:9

Dziko la Efuremu limagonera pa likulu lake Samariya, ndipo Samariya amagonera pa mfumu yake Peka. Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu, ndithu simudzalimba konse.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:18

Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18-19

Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:5

Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:9

Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-4

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake. Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:25-27

“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame? Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:4

Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:32

“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:5

Koma munthu atangokhulupirira, m'malo mwa kudalira ntchito zake, Mulungu amene amaŵaona kuti ngosapalamula anthu ochimwa, munthu ameneyo pakukhulupirira, Mulungu adzamuwona kuti ngwolungama pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:1-8

Yesu adaŵaphera fanizo pofuna kuŵaphunzitsa kuti azipemphera nthaŵi zonse, osataya mtima. Adati, “Anthu aŵiri adaapita ku Nyumba ya Mulungu kukapemphera. Wina anali Mfarisi, wina anali wokhometsa msonkho. Mfarisiyo adaimirira nayamba kupemphera motere mumtima mwake: ‘Mulungu, ndikukuyamikani kuti ine sindili monga anthu ena onse ai. Iwowo ndi anthu akuba, osalungama ndi adama. Sindilinso monga wokhometsa msonkho uyu ai. Ine ndimasala zakudya kaŵiri pa mlungu, ndipo ndimapereka chachikhumi pa zonse zimene ndimapata.’ Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ” Yesu popitiriza mau adati, “Kunena zoona, wokhometsa msonkhoyu adabwerera kwao ali wolungama pamaso pa Mulungu, osati Mfarisi uja ai. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo wodzichepetsa, adzamkuza.” Anthu ena ankabwera ndi ana omwe kwa Yesu kuti aŵakhudze. Ophunzira ake poona zimenezi, ankaŵazazira. Koma Yesu adaŵaitana nati, “Alekeni anaŵa azibwera kwa Ine, musaŵaletse. Paja Ufumu wa Mulungu ndi wa anthu otere. Ndithu ndikunenetsa kuti amene salandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, ameneyo sadzaloŵamo.” Mkulu wina adafunsa Yesu kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?” Yesu adamuyankha kuti, “Ukunditchuliranji wabwino? Wabwinotu ndi mmodzi yekha, Mulungu basi. Adati, “M'mudzi mwina mudaali woweruza wina amene sankaopa Mulungu kapena kulabadako za munthu. Malamulo ukuŵadziŵa: Usachite chigololo, usaphe, usabe, usachite umboni wonama, lemekeza atate ako ndi amai ako.” Munthu uja adati, “Zonsezi ndakhala ndikuzitsata kuyambira ndili mwana.” Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri. Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.” Anthu amene adamva zimenezi adafunsa kuti, “Tsono nanga angathe kupulumuka ndani?” Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.” Pamenepo Petro adati, “Ifetu paja tidasiya zonse kuti tizikutsatani.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wosiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena makolo, kapena ana chifukwa cha Ufumu wa Mulungu, M'mudzi momwemo mudaalinso mai wamasiye. Iyeyu ankabwera kwa woweruza uja kudzampempha kuti, ‘Mundiweruzireko mlandu umene uli pakati pa ine ndi mdani wanga.’ ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.” Yesu adatengera ophunzira ake pambali, naŵauza kuti, “Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu, ndipo zonse zidzachitika zimene aneneri adalemba zokhudza Mwana wa Munthu. Akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamnyazitsa, ndi kumthira malovu. Akamkwapula, nkumupha, koma mkucha wake Iye adzauka.” Ophunzira aja sadamvetse konse zimenezi. Tanthauzo la mau ameneŵa linali lobisika kwa iwo, nchifukwa chake sadamvetsetse zimene Yesu ankanenazo. Pamene Yesu ankayandikira ku Yeriko, munthu wina wakhungu adaakhala pamphepete pa mseu akupemphapempha kwa anthu. Atamva anthu ambirimbiri akupita mumseumo, adafunsa kuti, “Kodi kuli chiyani?” Adamuyankha kuti, “Kukupita Yesu wa ku Nazarete.” Apo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!” Anthu amene anali patsogolo adamzazira, adati, “Khala chete!” Koma iye adafuulirafuulira kuti, “Inu Mwana wa Davide, chitireni chifundo!” Kwa nthaŵi yaitali woweruza uja ankakana, koma pambuyo pake adaganiza kuti, ‘Ngakhale sindiwopa Mulungu kapena kusamala munthu, Yesu adaima nalamula kuti abwere naye kwa Iye. Atafika pafupi, Yesu adamufunsa kuti, “Kodi ukufuna kuti ndikuchitire chiyani?” Iye adati, “Ambuye, ndikufuna kuti ndizipenyanso.” Yesu adamuuza kuti, “Penya. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” Nthaŵi yomweyo adapenyanso nayamba kutsata Yesu, akuthokoza Mulungu. Anthu onse aja ataona zimenezi, adatamanda Mulungu. komabe chifukwa mai wamasiyeyu akundivuta, ndimuweruzira mlandu wake, kuwopa kuti angandilemetse nako kubwerabwera kwake.’ ” Tsono Ambuye adati, “Mwamvatu mau a woweruza wosalungama uja. Nanga Mulungu, angaleke kuŵaweruzira mlandu wao osankhidwa ake, amene amamdandaulira usana ndi usiku? Kodi adzangoŵalekerera? Iyai, kunena zoona adzaŵaweruzira mlandu wao msanga. Komabe Mwana wa Munthu pobwera, kodi adzapezadi chikhulupiriro pansi pano?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:20-21

Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:4

Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:12

Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:7

Ena amatamira magaleta ankhondo, ena amadalira akavalo, koma ife timatamira dzina la Chauta, Mulungu wathu, timamutama Iyeyo mopemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:29-31

Yesu adati, “Chabwino, bwera.” Tsono Petro adatuluka m'chombo nayamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu. Pajatu Herode kale adaatuma asilikali ake kuti akagwire Yohane, akammange ndi kumponya m'ndende. Adaachita zimenezi chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo, mbale wake. Koma ataona m'mene ikuwombera mphepo, adachita mantha, nkuyamba kumira. Tsono adafuula kuti, “Ambuye, pulumutseni!” Pompo Yesu adatambalitsa dzanja nkumugwira nati, “Iwe wa chikhulupiriro chochepawe, unakayikiranji?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:24

Inde, Mulungu adatipulumutsa, koma tikuyembekezabe chipulumutsocho. Koma tsono tikamaona ndi maso zimene tikuziyembekezazi, apo si chiyembekezonso ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:5

Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:37

Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:5

Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5

Inu Ambuye, ndinu amene ndimakukhulupirirani, Inu Chauta, ndinu amene ndimakudalirani kuyambira ubwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:13

Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:22

Ngati mukhala ndi chikhulupiriro, zonse zimene mungapemphe kwa Mulungu mudzalandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:3

Paja Malembo akuti bwanji? Akuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, ndipo pakukhulupirirapo, Mulungu adamuwona kuti ngwolungama.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:6

Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:8

Yesani ndipo mudzaona kuti Chauta ndi wabwino. Ngwodala munthu wothaŵira kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:4

Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25

Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:22

Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:8

Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:25

Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:8

Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:15

Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:26

Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:4

Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:5-6

Atumwi adapempha Ambuye kuti, “Mutiwonjezere chikhulupiriro.” Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:11

Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:46

Ine ndine kuŵala, ndipo ndidadza pansi pano, kuti munthu aliyense wokhulupirira Ine, asamayende mu mdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:22

Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa