Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


100 Mau a m'Baibulo Okhudza Gehena

100 Mau a m'Baibulo Okhudza Gehena

Ndikufuna ndikufotokozereni za malo amene akufa amapita, osiyana ndi chilango chomaliza cha oipa. Ngakhale kuti mawuwa achokera ku nkhani zakale zachikunja, tanthauzo lake lenileni lachokera ku mawu achihebri akuti Sheol. Mawuwa amapezeka nthawi makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu m’Malemba Achihebri, ndipo ngakhale kuti m’ma Baibulo ena amawamasulira kuti gehena, manda, kapena dzenje, Baibulo la Chichewa limagwiritsa ntchito mawu akuti Sheol. Mofanana ndi momwe mawu akuti Hades amagwiritsidwira ntchito m’Malemba Achigiriki.

Chofunika kwambiri apa ndichakuti Yesu anauza Petro kuti zipata za Hades sizidzalimbana ndi mpingo. Izi zikutanthauza kuti Yesu wapatsa mpingo mphamvu zoposa mphamvu zonse za mdani kuti tilengeze moyo pamene mdani walengeza imfa. Choncho, tifunika nthawi zonse kuima m’malo mwa anthu, kulankhula Mawu a Mulungu, ndikupemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi.




Machitidwe a Atumwi 2:27

ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku Malo a anthu akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18

Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:31

Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:15

Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:23

Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:18

Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:13

Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:22

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti aliyense wopsera mtima mbale wake adzayenera kuzengedwa ku bwalo lamilandu. Aliyense wonena mnzake kuti, ‘Wopandapake iwe,’ adzayenera kuzengedwera ku Bwalo Lapamwamba. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru,’ adzayenera kukaponyedwa ku moto wa Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:23

Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:8

Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:28

Musamaŵaopa amene amapha thupi, koma mzimu sangathe kuupha. Makamaka muziwopa amene angathe kuwononga thupi ndi mzimu womwe m'Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:13-14

Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:33

“Njoka inu, ana a mamba, mudzachipeŵa bwanji chilango cha ku Gehena?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:24

Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:26

Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:28

Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:19

Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:27

Munthu aliyense amafa kamodzi kokha, pambuyo pake nkumaweruzidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:27

Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:6

Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:19

Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:6

Nchifukwa chake Uthenga Wabwino udalalikidwa ndi kwa amene adafa omwe, kuti ngakhale adaweruzidwa m'thupi monga anthu, komabe mu mzimu akhale ndi moyo monga Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:11

“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, siidzamkhudza imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:14

Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma anthu amantha, osakhulupirika, okonda zonyansa, opha anzao, ochita zadama, ochita zaufiti, opembedza mafano, ndi anthu onse onama, malo ao ndi m'nyanja yodzaza ndi moto ndi miyala ya sulufure woyaka. Imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 14:9

“Kumanda kwatekeseka kuti kukulandire podzafika iwe mfumu ya ku Babiloni. Mandawo adzutsa mizimu ya anthu akufa kuti ikulonjere iwe, adzutsa mizimu ya onse amene adaali atsogoleri pa dziko lapansi. Akuŵaimiritsa pa mipando yao yaufumu onse amene adaali mafumu a mitundu ya anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 14:15

Koma watsitsidwa m'manda, pansi penipeni pa dzenje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:24

“Akamachoka, adzaona mitembo ya anthu amene adandipandukira. Mphutsi zimene zidzaŵadya sizidzafa, ndipo moto umene udzaŵatentha sudzazima. Anthu a mitundu yonse poŵaona adzanyansidwa nawo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 32:21

M'kati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana kuti, ‘Kani anthu osaumbalidwa aja, ophedwa pa nkhondo, afika kunsi kuno. Si aŵa agona apaŵa!’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 32:27

Sadaikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene adatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zao zomwe zankhondo. Malupanga ao adaŵaika ku mitu yao, ndipo zishango zao adaphimbira mafupa ao. Kale anthu amphamvu ameneŵa ankaopsa m'dziko la anthu amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:12

Koma chonsecho amene akadayenera kukhala mu Ufumuwo, adzaŵaponya kunja, ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano chifukwa cha zoŵaŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:13

Apo mfumuyo idauza anyamata ake kuti, ‘Mmangeni manja ndi miyendo, mukamponye kunja ku mdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:51

Choncho adzamlanga koopsa, ndipo adzamtaya ku malo a anthu achiphamaso. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:30

Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:5

Koma ndikuchenjezeni: amene muyenera kumuwopa ndi Mulungu. Iye atalanda moyo wa munthu, ali nazonso mphamvu za kumponya m'Gehena. Ndithu ndi ameneyo amene muzimuwopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 13:28

Apo mudzayamba kulira ndi kukukuta mano, pamene mudzaona Abrahamu ndi Isaki ndi Yakobe ndi aneneri onse mu Ufumu wa Mulungu, inuyo mukuponyedwa kunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19

“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:18

Mkwiyo wa Mulungu ukuwoneka kuchokera Kumwamba. Amakwiyira anthu chifukwa cha kusalungama kwao konse ndi kusamchitira ulemu. Kusalungama kwaoko kumaŵalepheretsa kudziŵa zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:8

Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:9

Masautso ndi zoŵaŵa zidzaŵagwera onse ochita zoipa, poyamba Ayuda, kenaka anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:9

Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:11

Utsi wa moto woŵazunzawo umakwera kumwamba mpaka muyaya. Anthu amene adapembedza chilombo chija ndi fano lake, ndiponso amene adalembedwa chizindikiro cha dzina lake chija, sapeza mpumulo usana kapena usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:15

Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:17

Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:15

Inu Mulungu, mulole kuti imfa iŵagwere adani anga, atsikire ku manda akadali moyo, pakuti zoipa zili tho m'mitima ndi m'nyumba zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:13

Paja chikondi chanu chosasinthika kwa ine nchachikulu, Mwandipulumutsa ku malo akuya a anthu akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:24

Njira yopita ku moyo imakamufikitsa ku ntchito zangwiro, kuti alewe malo a anthu akufa kunsiko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:20

Manda sakhuta, nawonso maso a munthu sakhuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:14

Nchifukwa chake kumanda sikukhuta, kwangoti kukamwa yasa kuti kulandire aliyense. Anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka, adzagweramo ali wowowo, m'kuledzera kwaoko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:15

Inu mumanena kuti “Ife tidachita chipangano ndi imfa, ndipo manda satiwopsa ai. Chiwonongeko chikamadzafika, sichidzatikhudza konse. Inu mumakhulupirira mabodza ngati kothaŵira, ndipo mumadalira kunama kuti kukhale kopulumukira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:33

Malo otenthera zinthu ndi okonza kale, adakonzera mfumu ya ku Asiriya. Malowo ndi ozama ndi aakulu, odzaza ndi moto ndi nkhuni. Tsono mpweya wa Chauta, wonga ngati mtsinje wa sulufure, udzakoleza motowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:55

Ndidatama dzina lanu mopemba, Inu Chauta, ndili m'dzenje lozamalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:30

“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 33:11

Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 13:14

Kodi ngati ndidzaŵapulumutsa kwa akufa? Kodi ngati ndidzaŵaombola ku imfa? Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti? Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti? Anthu ameneŵa sindidzaŵachitiranso chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 1:5

Zonsezi zikuchitika chifukwa cha zoipa za zidzukulu za Yakobe, chifukwa cha machimo a banja la Israele. Ndani adachimwitsa Aisraele? Si a ku Samariya kodi? Ndani adalakwitsa Ayuda? Si a ku Yerusalemu kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 3:14

Ndi mivi yanu mudalasa mtsogoleri wa ankhondo ake, amene adaabwera ngati kamvulumvulu kuti atibalalitse. Ankakondwerera ngati kuti akudzaononga osauka mwachinsinsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:42

nadzaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:50

nkumaŵaponya m'ng'anjo ya moto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:41

“Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:25

Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:36

Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:24

Nchifukwa chake ndakuuzani kuti mudzafera m'machimo anu. Pakuti ngati simukhulupirira kuti Ine ndine Ndilipo, mudzaferadi m'machimo anu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:9

Kani simudziŵa kuti anthu osalungama sadzaulaŵa Ufumu wa Mulungu? Musadzinyenge: anthu adama, opembedza mafano, achigololo, ochimwa ndi amuna anzao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:22

Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:5

Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:6

Chifukwa cha zinthu zotere Mulungu amaŵakwiyira anthu osamumvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:29

Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:12

Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:15-17

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:5

Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:16

Koma popeza kuti ndinu ofunda chabe, osati otentha kapena ozizira, ndidzakusanzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:20

Koma anthu oipa amatha. Adani a Chauta amafota ngati maluŵa, amazimirira ngati utsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:14

Ayenera kupita ku dziko la akufa ngati nkhosa, ndipo imfa idzakhala mbusa wao. Anthu olungama adzaŵapambana. Adzatsika kulunjika ku manda, matupi ao adzaola, kwao kudzakhala kumanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:18

Koma mwamunayo sadziŵa kuti kumeneko kuli imfa, kuti alendo ake aloŵa kale m'manda ozama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:7

Munthu wabwino anzake adzamkumbukira ngati dalitso, pamene woipa, mbiri yake idzatha ngati chinthu choola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 9:10

Ntchito iliyonse imene ukuti uigwire, uigwire ndi mphamvu zako zonse. Pajatu kumanda kumene ukupitako kulibe ntchito, kulibe malingaliro, kulibe nzeru, ndiponso kulibe luntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:21

Palibe mtendere kwa oipa,” akutero Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:34

Sikudzamvekanso mau achisangalalo ndi achimwemwe ku mizinda ya ku Yuda ndi ku miseu ya mu Yerusalemu. Sikudzamvekanso mau achikondwerero, a mkwati wamwamuna ndi wamkazi. Ndithudi dzikolo lidzasanduka chipululu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 2:22

Monga momwe mumaitanira ku chikondwerero, ndi m'mene mwandiitanira zoopsa kuchokera mbali zonse. Inu Chauta, pa tsiku la mkwiyo wanu, palibe amene adathaŵako kapena kupulumuka. Onse amene ndidaŵabala ndi kuŵalera, adani anga adaŵaononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 31:17

Mitundu imene inkakhala mumthunzi mwake chifukwa cha kumvana nawo, nayonso idapezana nawo kumandako, pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 32:11

“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni idzakufika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:30

Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:31

Kenaka mizimuyo idapempha Yesu kuti asailamule kuti ikaloŵe ku chiphompho chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:32

Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:12

Motero adzalangidwa onse amene sadakhulupirire choona, koma adakondwerera kusalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:31

Kugwa m'manja mwa Mulungu wamoyo ndi chinthu choopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:20

Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, dzina lanu ndi lolemekezeka ndi loopsa, palibe chofanana ndi chiyero chanu. Lero ndikulapa machimo anga ndipo ndikupempha chikhululukiro, ndikudziwa kuti kukhalapo kwanu kokha kunganditsuke kuti ndikhale wopanda kuipa ndi mantha. Mundipatse kukhala mwana wanu wakhama ndi wodalirika pa nkhani ya chipulumutso changa, kuti moyo wanga ukhale wonunkhira bwino pamaso panu ndipo mapazi anga atsogoleredwe ndi mawu anu. Ambuye Yesu, lero ndikudzitukumula pamaso panu, ndikuvomereza tchimo langa, chonde, Ambuye ndikupemphani kuti mundibwezeretse, mundisinthe ndi kuchiritsa mabala omwe ulendo wandipatsa, musalole kuti moyo wanga uzunzidwe kwamuyaya ku Hade. Ndithandizeni kukuyembekezerani tsiku lililonse Yesu ndi lingaliro lakuti munabwera dzulo ndipo mudzabweranso mawa, musalole Ambuye kuti zonyansa, kuipitsidwa, kapena kudzikuza zindichotse maso anga kwa inu. Mawu anu akuti: "Pakuti simudzasiya moyo wanga ku Hade, Kapena kulola kuti Woyera wanu aone chivundi." M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa