Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda. Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.
Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda.
Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa.
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.”
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Pajatu mau aakulu amene ndidakupatsani ndi omwewo amene inenso ndidalandira. Mauwo ndi akuti Khristu adafera machimo athu, monga Malembo anenera. Nanga pamenepo ifenso timakhaliranji m'zoopsa nthaŵi zonse? Abale anga, imfa ndimayenda nayo tsiku ndi tsiku. Ndikunenetsa zimenezi chifukwa ndimakunyadirani mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Nanga pamene ndidalimbana ndi zilombo ku Efeso, ndidapindulapo chiyani, ngati ndinkatsata maganizo a anthu chabe? Ndiyetu ngati akufa sauka, tizingochita monga amanenera kuti, “Tiyeni tizidya ndi kumwa, pakuti maŵa tikufa.” Musadzinyenge. “Paja kuyanjana ndi anthu ochimwa kumaononga khalidwe.” Mudzidzimuke mumtima mwanu, ndipo muleke kuchimwa. Ena mwa inu sadziŵa Mulungu konse. Ndikukuuzani zimenezi kuti muchite manyazi. Koma kapena wina nkufunsa kuti, “Kodi akufa adzauka bwanji? Kodi adzakhala ndi thupi lotani?” Ati kupusa ati! Mbeu imene umafesa, siingamere ndi kukhala moyo itapanda kufa. Ndipo chimene ufesa, si mmera umene udzatuluka ai, koma ndi njere chabe, kaya ndi ya tirigu, kapena ya mtundu wina uliwonse. Koma Mulungu amaisandutsa mmera monga momwe Iye akufunira, mbeu iliyonse mmera wakutiwakuti. Mnofu sukhala wa mtundu umodzi. Pali mnofu wina wa anthu, wina wa nyama, wina wa mbalame, ndi wina wa nsomba. Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera.
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Chifukwa chakuti Yesu Khristu adachita zimene Mulungu adaafuna kuti achite, ife tidayeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene Iye adapereka kamodzi kokhako.
Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m'kuwoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Khristuyo adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga?
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.
Yesu ameneyu sali ngati akulu a ansembe ena aja. Palibe chifukwa chakuti tsiku ndi tsiku azipereka nsembe poyamba chifukwa cha machimo ake, kenaka chifukwa cha machimo a anthu. Zimenezi adachitiratu kamodzi kokha, pakudzipereka yekha ngati nsembe.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.”
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Mulungu adachita zimene Malamulo a Mose sadathe kuzichita, chifukwa khalidwe la anthu lopendekera ku zoipa lidaŵafooketsa. Iye adatsutsa uchimo m'khalidwe lopendekera ku zoipalo, pakutuma Mwana wakewake, ali ndi thupi longa la ife anthu ochimwa, kuti m'thupilo adzagonjetse uchimowo. Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake. Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angaŵaimbe mlandu anthu amene Mulungu adaŵasankha? Mulungu mwiniwake amaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo. Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”
Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
Anali wofooka pamene adapachikidwa pa mtanda, komabe tsopano ali moyo mwa mphamvu ya Mulungu. Ifenso ndife ofooka mwa Iye, koma tidzakhala amoyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, pogwira ntchito yathu pakati panu.
Pa nthaŵi imene Mulungu adaikonzeratu, pamene ife tikusoŵabe pogwira, Khristu adatifera anthu ochimwafe.
Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Ndipo Ine, akadzandipachika, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” (Adaanena mau ameneŵa kuti aŵadziŵitse za m'mene analikudzafera.)
Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse. Ali munthu choncho adadzichepetsa, adakhala womvera mpaka imfa, imfa yake yapamtanda.
Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.
Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake. Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.
Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.
Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu. Iyeyo adadzipereka kuti akhale momboli wa anthu onse. Umenewu unali umboni umene udaperekedwa pa nthaŵi yake.
Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Pambuyo pake adauza onse amene anali pamenepo kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake tsiku ndi tsiku nkumanditsata.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Chimodzimodzi inunso, abale anga. Mudachita ngati kufa ndi kulekana ndi Malamulo popeza kuti ndinu ziwalo za thupi la Khristu. Motero tsopano ndinu a wina wake, ndiye kuti a Iye amene adauka kwa akufa kuti tibalire Mulungu zipatso.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma ife timalalika Khristu amene adapachikidwa pa mtanda. Kwa Ayuda mau ameneŵa ndi okhumudwitsa, pamene kwa anthu a mitundu ina mauŵa ndi opusa.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti,
Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati. za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni. Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
Ndidaperekera msana wanga kwa ondimenya, ndiponso masaya anga kwa ondimwetula ndevu. Sindidaŵabisire nkhope ondinyoza ndi ondithira malovu.
Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa.
Iwo adatifera kuti tikakhale ndi moyo pamodzi naye, ngakhale pamene tili amoyo kapena titafa kale.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
Adapachikanso pa mitanda zigaŵenga ziŵiri, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere.
Nthaŵi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu m'thupi mwathu, kuti moyo wake uwonekenso m'thupi mwathu. Pakuti nthaŵi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake uwonekenso m'matupi athu amene amafa.
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake. Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.
Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo.
Tiyeni tsono, tigwiritse chikhulupiriro chimene timavomereza. Pakuti tili naye Mkulu wa ansembe wopambana, amene adapita mpaka kukafika kumwamba kwenikweni kwa Mulungu. Iyeyu ndi Yesu, Mwana wa Mulungu. Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye. Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima. Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu. Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.
Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu.
M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi.
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Chauta akuti, “Mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake. Adzakwezedwa ndi kulemekezedwa, ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri. Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu. Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, Mafumu omwe adzasoŵa naye chonena, popeza kuti zinthu zosaŵauzapo chiyambire adzaziwona, ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa.”
Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa. Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,
Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu. Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.
Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola. Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu. Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo. Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen. Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu. Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu. Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake. Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo. Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani? Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?” Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino. Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.
Iye atasenza mtanda wake, adatuluka naye mu mzinda kupita ku malo otchedwa “Malo a Chibade cha Mutu” (pa Chiyuda amati “Gologota.”)
Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu. Aboola manja anga ndi mapazi anga. Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang'anitsitsa akukondwera poona kuti ndikuvutika. Agaŵana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere.
Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.
Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Pakuti chimene Atate anga afuna nchakuti munthu aliyense amene aona Mwanayo namkhulupirira, akhale ndi moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu.
Sindiisandutsa yopandapake mphatso yaulere ya Mulungu. Pakuti ngati munthu atha kusanduka wolungama pamaso pa Mulungu pakutsata Malamulo, ndiye kuti Khristu adafa pachabe.
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita.
Mwala umene amisiri omanga nyumba adaukana, womwewo wasanduka mwala wapangodya. Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu.
Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupulumutsa.
Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu.
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.