Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.
Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu.
Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa.
Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo.
Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.
Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira.
Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima, ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi.
Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena.
Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa.
Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo.
Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu.
“ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto.
Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu.
Masiku amenewo kudafika aneneri ena ku Antiokeya ochokera ku Yerusalemu. Mmodzi mwa iwo, dzina lake Agabu, adaimirira, ndipo ndi mphamvu za Mzimu Woyera adalosa kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lapansi. Njalayo idabweradi pa nthaŵi ya Klaudio.
Mu mpingo wa ku Antiokeya munali alaliki ndi aphunzitsi aŵa: Barnabasi, Simeoni (wotchedwa Wakuda), Lusio wa ku Kirene, Manaene (amene adaaleredwa pamodzi ndi bwanamkubwa Herode), ndiponso Saulo.
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
Tsono Chauta adatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga. Ndipo adandiwuza kuti, “Tamvera, ndikuika mau anga m'kamwa mwako.
Ngati mneneri walota maloto, afotokoze maloto akewo. Koma amene ali ndi mau anga, alalike mau angawo moona. Kodi mungu ungafanane ndi tirigu?” Akuterotu Chauta.
“Patapita nthaŵi, tsiku lidzafika pamene ndidzatsitsa mzimu wanga pa mtundu uliwonse wa anthu. Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosa. Nkhalamba zanu zidzalota maloto, ndipo achinyamata anu adzaona zinthu m'masomphenya.
Koma ine Chauta wandidzaza ndi mphamvu, wandidzaza ndi mzimu wake. Wandidzaza ndi kulungama ndi kulimba mtima, kuti ndidzudzule a banja la Yakobe chifukwa cha zolakwa zao, kuti ndiwonetse Aisraele zoipa zao.
Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi.
Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri.
Koma ngati mneneri alosa za mtendere, zimene walosazo zikachitikadi, pamenepo zidzadziŵika kuti Chauta adamtumadi.”
Chauta adati, “Imvani mau anga. Pakakhala mneneri pakati panupa, Ine Chauta ndimadziwonetsa kwa munthuyo m'masomphenya, ndimalankhula naye m'maloto.
Nthaŵi imeneyo Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.”
Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adadziŵa kuti Chauta adamsankha Samuele kuti akhale mneneri.
Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.”
Chauta Wamphamvuzonse akuuza anthu kuti, “Musamvere zimene akunena aneneri, iwowo amakuloserani zonyenga. Zimene amakuuzani kuti akuziwona m'masomphenya ndi maganizo ao chabe, si zolankhula Chauta ai.
Amauza oona zobisika kuti, ‘Musaonenso.’ Amauza aneneri kuti, ‘Musatiloserenso zoona. Mutiwuze zotikomera, mutilosere zam'mutu chabe.
Koma Mikaya adati, “Pali Chauta wamoyo, zimene Chautayo andiwuze, ndizo ndidzalankhule.”
Kodi mau anga ndi malamulo anga amene ndidauza atumiki anga aneneri, suja adamveka kwa makolo anu? Choncho iwo adalapa ndi kunena kuti, ‘Chauta Wamphamvuzonse watichitadi zomwe adaatsimikiza kuti adzatichita, potsata makhalidwe athu ndi ntchito zathu zoipa.’ ”
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.
Koma Mulungu adaaneneratu mwa aneneri onse kuti Wodzozedwa wake wolonjezedwa uja adzamva zoŵaŵa, ndipo zidachitikadi momwemo.
Monsemo Chauta adatuma amithenga ndi aneneri ake ku Israele ndi ku Yuda, okalalika kuti, “Musinthe makhalidwe anu auchimo ndipo mumvere Malamulo anga amene ndidaŵapereka kwa makolo anu, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”
Koma Chauta adandiyankha kuti, “Zakuti aneneriwo amalosa m'dzina langa, ili ndi bodza. Ine sindidaŵasankhe, sindidaŵatume kapena kulankhula nawo. Iwo amakuloserani zinthu zonama zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amaombeza zabodza, zimene amalankhula ndi zonyenga zopeka iwo eni ake.
Ine Ambuye Chauta ndikunena kuti, Tsoka kwa aneneri opusa amene amachita kupeka zolosa zao, chonsecho sadaone chilichonse chochokera kwa Ine.
Chauta adati, “Aneneri ameneŵa sindidaŵatume ndine, komabe ankathamanga uku ndi uku ndi mithenga yao. Sindidalankhule nawo, komabe ankalosa.
“Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe?
Munthu wolandira nthumwi ya Mulungu chifukwa choti ndi nthumwi, adzalandira mphotho ya nthumwi ya Mulungu. Wolandira munthu wolungama chifukwa choti ngwolungama, adzalandira mphotho ya munthu wolungama.
Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi.
Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.”
Tsono Eliya adauza anthu aja kuti, “Ine ndatsala ndekha mwa aneneri a Chauta, koma aneneri a Baala alipo 450 pamodzi.
Pamene a m'gulu la aneneri amene ankakhala ku Yeriko adaona Elisayo akuwoloka, adati, “Mphamvu ndi nzeru za Eliya zaloŵa mwa Elisa.” Tsono adabwera kudzakumana naye, namgwadira Elisayo, nkuŵeramitsa mitu yao pansi.
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”
Chauta adachita kukanditenga, kundileketsa ntchito yoŵeta nkhosa, nandiwuza kuti, ‘Pita, ukalalikire anthu anga, Aisraele.’
Yona adaloŵa mumzindamo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Adayamba kulalika kuti, “Pakapita masiku makumi anai, Ninive aonongeka!”
Apo adandiwuza kuti, “Alalikire mafupa ameneŵa, uŵauze mafupa oumawo kuti amve mau a Ine Chauta.
Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
“Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Inu masiku ano mukumva mau a aneneri amene ankalankhula pa nthaŵi yoyala maziko a Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse. Choncho limbani mtima, kuti Nyumbayi imangidwenso.
Ndidalankhula ndi aneneri. Ndine amene ndidaŵaonetsa zinthu zambiri ngati kutulo. Ndidalankhula m'mafanizo kudzera mwa iwo.
Ndidzakantha aneneri onama amene amati adaona zakutizakuti ngati kutulo, amenenso kulosa kwao nkwabodza. Sadzakhala nao m'bwalo la aphungu la anthu anga. Sadzalembedwa m'kaundula wa nzika za Israele, ndipo sadzaloŵa m'dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Ambuye Chauta.
Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”
Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa. Pamenepo mzimu wa Chauta ukuloŵa mwamphamvu, ndipo nawenso uyamba kulosa nao, usinthika ndi kukhala munthu wina.
Yehu mwana wa Nimisi ukamdzoze kuti akhale mfumu ya ku Israele. Ndipo Elisa, mwana wa Safati wa ku Abele-Mehola, ukamdzoze kuti akhale mneneri woloŵa m'malo mwako.