Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


160 Mauthenga a Mulungu Okhudza Kusakhwima Mwauzimu

160 Mauthenga a Mulungu Okhudza Kusakhwima Mwauzimu

Ufulu wanga wauzimu unayamba pamene ndinalandira Khristu ngati Mpulumutsi wanga. Koma imeneyo ndiye kungoyamba chabe. Ulendowu uyenera kupitirira ndi kukula mwa makhalidwe ofanana ndi a Khristu. Njira imeneyi si onse okhulupirira amatsatira njira yachibadwa yokhwima. Ambiri amakhalabe Akristu osakhwima kapena a m'thupi, zomwe zimakhudza khalidwe lawo, kuwonetsa machimo ambiri ndi kusowa nzeru m'machitidwe awo.

Kukhwima kwauzimu sikubwera tsiku limodzi. Kumafunika chikhulupiriro ndi chipiriro. Munthu akhoza kukhala ndi zaka zambiri akuzindikira Khristu, koma osakulitsa ubale wake naye. Koma sizikuyenera kukhala choncho.

Aheberi 5:11-14 imati: “Pakuti pokhala ndi nthawi yayitali, muyenera kukhala aphunzitsi, koma mufunikira wina kuti akuphunzitseni kuyambira pachiyambi mfundo zoyamba za mawu a Mulungu; ndipo mwakhala ofooka, ofunika mkaka, osati chakudya chotafuna. Pakuti yense wakudya mkaka sadziwa mawu a chilungamo; pakuti ndi khanda. Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu akuluakulu, amene pogwiritsira ntchito, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choipa.”

Ndikofunika kuunika ubale wathu ndi Mulungu ndikukonza zolakwa zathu kuti tipitirire patsogolo. Sitingathe kukhala ndi makhalidwe ndi zochita zomwezo za zaka zapitazo. Tiyenera kuyenda mokwanira ndi Yesu, kumuyika Iye pakati pa miyoyo yathu. Pokhapokha tingayende molimba mtima ndipo palibe chomwe chingatichitikire chomwe chingatisokoneze pa cholinga chathu chamuyaya mwa Mulungu.




Miyambo 9:6

Leka kupulukira kwako, kuti ukhale ndi moyo, uziyenda m'njira ya nzeru.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1

Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:20

Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1-3

Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu. Popeza kuti Mulungu adachita kundituma, ndidakhazika maziko monga mmsiri waluso, ndipo wina akumanga pa mazikowo. Koma aliyense azichenjera pomanga. Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu. Pa mazikoŵa munthu angathe kumangapo ndi golide, siliva, miyala yamtengowapali, mitengo, udzu kapena mapesi. Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho. Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto. Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene. Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.” Ndidakumwetsani mkaka, osakupatsani chakudya cholimba, chifukwa simukadatha kuchidya. Ngakhalenso tsopano simungathe kuchidya, Penanso Malembo akuti, “Ambuye amaŵadziŵa maganizo a anthu anzeru kuti ndi achabe.” Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu: Paulo, Apolo ndi Kefa, dziko lapansi, moyo ndi imfa, zimene zilipo ndi zimene zilikudza. Koma ngakhale zonsezi nzanu, inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu. popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:3

popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:2

Ndidakumwetsani mkaka, osakupatsani chakudya cholimba, chifukwa simukadatha kuchidya. Ngakhalenso tsopano simungathe kuchidya,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:2

Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14

Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12-14

Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba. Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo. Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12

Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:22

“Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 10:2

Mtima wao ndi wonyenga. Tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo ao. Chauta adzagumula maguwa ao ansembe, ndipo adzaononga miyala yao yoimiritsa yachipembedzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:6

Koma wopemphayo apemphe mokhulupirira, ndi mosakayika konse. Paja munthu wokayikakayika ali ngati mafunde apanyanja, amene amavunduka ndi kuŵinduka ndi mphepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:14

Maso ao ndi adama, osafuna kuleka kuchimwa. Amanyengerera anthu a mtima wosakhazikika. Ali ndi mtima wozoloŵera kuumirira chuma. Anthu otembereredwa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:26-27

Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:1-3

Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mloŵachuma akali wamng'ono sasiyana ndi kapolo, ngakhale iyeyo ndi mwini chuma chonsecho. Mumasunga masiku, miyezi, nyengo ndi zaka. Ndikuwopa kuti mwinatu ntchito zanga zonse pakati panu ndidazigwira pachabe. Ndikukupemphani abale, musanduke ngati ine, pakuti inenso ndidasanduka ngati inu nomwe. Simudandilakwire konse. Monga mukudziŵa, pamene ndidayamba kukulalikirani Uthenga Wabwino, ndinkadwala. Ngakhale matendawo anali ngati mayeso kwa inu, komabe simudandinyoze kapena kunyansidwa nane. Kwenikweni mudandilandira ngati mngelo wa Mulungu, kapenanso ngati Khristu Yesu mwini. Nanga chimwemwe chanu chija chili kuti tsopano? Ndikukuchitirani umboni kuti nthaŵi imene ija, kukadatheka, mukadakolowola maso anu nkundipatsa ineyo. Monga ndasanduka mdani wanu popeza kuti ndakuuzani zoona? Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo. Kwabwino nkumachita changu pa chinthu chabwino masiku onse, osati pokhapokha pamene ndili pamodzi nanu. Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu. Mwanayo ayenera kumvera omulera ndiponso akapitao oyang'anira chuma chake, mpaka nthaŵi imene bambo wake adakhazikitsa. Ndikadakonda nditakhala nanu tsopano. Apo kapena ndikadasintha mau anga, chifukwa mwandithetsa nzeru. Inu ofuna kukhala akapolo a Malamulo, tandiwuzani. Kodi simukumvetsa zimene Malamulowo akunena? Paja Malembo akuti, Abrahamu anali ndi ana aamuna aŵiri: wina mai wake anali kapolo, winayo mai wake anali mfulu. Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu. Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo. Hagarayo akufanizira phiri la Sinai la m'dziko la Arabiya, lofanizira Yerusalemu walero, amene ali m'ukapolo pamodzi ndi anthu ake onse. Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mai wathu. Paja Malembo akuti, “Sangalala iwe chumba chosabala ana, imba nthungululu, fuula mokondwera, iwe amene sunamvepo zoŵaŵa za kubala. Ana a mkazi wosiyidwa ndi ochuluka koposa ana a mkazi amene ali naye mwamuna.” Tsono inu abale, ndinu ana a Mulungu chifukwa cha lonjezo lake, monga Isaki. Nthaŵi imeneyo mwana uja amene adaabadwa monga momwe amabadwira ana onseyu, ankasautsa mwana winayo wobadwa mwa mphamvu za Mzimu Woyera, ndipo mpaka tsopano zili chimodzimodzi. Chimodzimodzinso ifeyo, pamene tinali ana, tinali akapolo a miyambo yapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:3

ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:18

Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:11

Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15

Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:15

Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:1

Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:6-7

Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-27

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1-3

Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano. Tikufunitsitsa kuti aliyense mwa inu apitirire kuwonetsa changu chomwechi mpaka potsiriza, kuti chiyembekezo chanu chifike pake penipeni. Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza. Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo. Ndiye Mulungu adati, “Ndithudi ndidzakudalitsa kwakukulu, ndipo ndidzachulukitsa kwambiri zidzukulu zako.” Nchifukwa chake Abrahamu adaayembekeza molimbikira, nalandira zimene Mulungu adaamlonjeza. Anthu amalumbira m'dzina la wina amene akuŵaposa, ndipo lumbiro lotere lotsimikizira mau, limathetsa kutsutsana konse pakati pao. Mulungu pofuna kuŵatsimikizira anthu odzalandira zimene adaalonjeza, kuti Iye sangasinthe maganizo, adatsimikiza lonjezo lakelo pakulumbira. Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu. Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati. za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni. Yesu adatitsogolera kale nkuloŵamo chifukwa cha ife. Iye adasanduka mkulu wa ansembe onse wamuyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki. Mulungu akalola, tidzaterodi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7-8

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:13-14

Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja. Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:15-17

Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21

koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:1

Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:32

Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:20-21

Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti alibe mizu yozama, amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo munthuyo amabwerera m'mbuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:10

Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:7

Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:5-6

Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-8

Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10-11

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:15

Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:14

Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:39

Ifetu sindife anthu oti nkumabwerera m'mbuyo ndi kutayika ai, ndife anthu okhulupirira, kuti tipulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:29

Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:1-2

Tsono tinene chiyani? Kodi tinganene kuti tizingokhalabe mu uchimo kuti kukoma mtima kwa Mulungu kuchuluke? Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu. Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu. Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo. Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu. Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si Malamulo, koma kukoma mtima kwa Mulungu? Iyai, mpang'ono pomwe. Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake. Tiyamike Mulungu! Inu kale munali akapolo a uchimo, koma tsopano mukumvera ndi mtima wonse zoona za chiphunzitso chimene mudalandira. Mudamasulidwa ku uchimo, ndipo tsopano mwasanduka atumiki a Mulungu ochita zachilungamo. Ndikukupherani fanizo la ukapololi kuti mungalephere kumvetsa bwino zimenezi. Kale munkadzipereka kuti mukhale akapolo a zonyansa ndi zosalongosoka zonkirankira. Chonchonso tsopano mudzipereke kuti musanduke atumiki a Mulungu ochita zachilungamo, kuti mukhale oyera mtima. Iyai, mpang'ono pomwe. Tidachita ngati kufa nkulekana ndi uchimo. Nanga tingakhalebe mu uchimowo bwanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1-3

Nchifukwa chake tayani choipa chonse, kunyenga konse, chiphamaso, kaduka ndi masinjiriro onse. Kale simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake. Kale simudaalandira chifundo, koma tsopano mwachilandira. Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu. Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere. Chifukwa cha Ambuye, muzimvera akulu onse olandira ulamuliro. Ngati ndi mfumu yaikulu koposa ija, imvereni chifukwa ili ndi ulamuliro pa mafumu ena onse. Ngati ndi nduna, zimvereni chifukwa zidachita kutumidwa ndi mfumu kuti zizilanga ochita zoipa ndi kuyamikira ochita zabwino. Paja Mulungu amafuna kuti ndi zochita zanu zabwino muthetse kulankhula kosadziŵa kwa anthu opusa. Inde muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa. Koma khalani ngati atumiki a Mulungu. Muzilemekeza anthu onse. Muzikonda akhristu anzanu. Khalani anthu oopa Mulungu. Mfumu yaikulu koposa ija muziipatsa ulemu. Inu antchito, muzimvera ndi ulemu wonse anthu okulembani ntchito, osati okhawo amene ali abwino ndi ofatsa ai, koma ndi ovuta omwe. Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera. Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso, Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu. Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake. Iye sadachitepo tchimo lililonse, ndipo sadanene bodza lililonse. Pamene anthu ankamuchita chipongwe, Iye sadabwezere chipongwe. Pamene ankazunzika, Iye sadaopseze, koma adapereka zonse kwa Mulungu amene amaweruza molungama. Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake. Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani. popeza kuti mwachilaŵadi chifundo cha Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:21

Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:11-12

Tili ndi zambiri zoti nkunena pa zimenezi, koma nzovuta kufotokoza kwake, popeza kuti mwasanduka ouma mitu. Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:5

Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:10

ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1-2

Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse. Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika. Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi? Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka. Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa. Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza. Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa. Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse. Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso. Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere. Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:23-24

Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:17

Tsono inu okondedwa, popeza kuti mwazidziŵiratu zimenezi, chenjerani kuti zolakwa za anthu ochimwa zingakusokeretseni ndipo mungagwedezeke kenaka nkugwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13-14

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:16

Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:45

ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16-17

Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22-25

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:4

Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:18

Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:20-21

Iwe Timoteo, usunge bwino zimene adakusungitsa. Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, ndiponso maganizo otsutsana, amene anthu amanama kuti ndi nzeru zodziŵa zinthu. Anthu ena, chifukwa chovomereza nzeru zotere, adasokera nkutaya chikhulupiriro chao. Mulungu akukomere mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:1-3

Agalatiya opusa inu, adakulodzani ndani? Pamene tidakulalikirani Yesu Khristu, tidamuwonetsa poyera pamaso panu ngati wopachikidwa pa mtanda. Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m'buku la Malamulo.” Komatu nchodziŵikiratu kuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Paja Malembo akuti, “Munthu amene ali wolungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira, adzakhaladi ndi moyo.” Koma Malamulo akusiyana ndi chikhulupiriro, chifukwa Malembo akuti, “Munthu amene amachita zonse zolamulidwa ndi Malamulo, adzakhala ndi moyo pakutero.” Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.” Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza. Abale, ndikufotokozereni zimenezi pokupatsani chitsanzo cha zimene zimachitika tsiku ndi tsiku. Anthu aŵiri akapangana natsimikiza chimodzi, palibe munthu angaphwanye panganolo kapena kuwonjezapo mau. Tsono Mulungu adapatsa malonjezo ake kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sakunena kuti, “Ndi kwa mbeu zake” ai, ngati kuti akunena za anthu ambiri. Koma akunena kuti, “Ndi kwa mbeu yake”, popeza kuti akukamba za munthu mmodzi yekha. Ameneyu ndi Khristu. Chimene ndikunena ndi ichi: Mulungu adachita chipangano, nalonjeza kuchisunga. Malamulo a Mose, amene adadza patapita zaka 430, sangathe kuchiphwanya chipanganocho ndi kuwononga lonjezo la Mulungu lija. Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero. Nanga tsono cholinga cha Malamulo chinali chiyani? Mulungu adaonjezapo Malamulo kuti azindikiritse anthu machimo, mpaka mbeu ija ya Abrahamu, imene Mulungu adaaipatsa lonjezo lija, itabwera. Mulungu adapereka Malamulowo kudzera mwa angelo, ndiponso kudzera mwa munthu wochita ntchito ya mkhalapakati. Ndikufunseni chinthu chimodzi chokha: Kodi mudalandira Mzimu Woyera pakutsata Malamulo, kapena pakumva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino? Tsono tikati mkhalapakati, ndiye kuti pali anthu aŵiri. Koma Mulungu ali yekha. Kodi ndiye kuti Malamulo a Mose amatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Mpang'ono pomwe. Anthu akadalandira malamulo otha kuŵapatsa moyo, pamenepo bwenzi atasanduka olungama kudzera mwa malamulowo. Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza. Chisanafike chikhulupirirochi, tinali ngati akaidi m'manja mwa Malamulo, kudikira kuti chikhulupiriro chimene chidaati chifikecho, chiwululidwe. Motero Malamulowo anali ngati namkungwi wathu, mpaka atabwera Khristu, kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira. Popeza kuti tsopano chikhulupiriro chafika, namkungwiyo satilamuliranso. Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu. Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza. Kani ndinu opusa chotere? Kodi zimene Mzimu Woyera adayamba kuchita mwa inu, mukufuna kuzifikitsa pake penipeni tsopano ndi mphamvu zanuzanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:13

Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:67

Ndisanayambe kulangika ndinkasokera, koma tsopano ndimamvera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14-15

Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:13

Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:22

ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:20-21

Chifukwatu ngati anthu apulumuka ku zodetsa za dziko lino lapansi, pakudziŵa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu, pambuyo pake nkugwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zoipa zomwezo, potsiriza adzakhala oipa koposa m'mene analiri poyamba. Kukadakhala bwino kwa iwo akadakhala osadziŵa njira ya chilungamo, koposa kuileka atadziŵa lamulo loyera limene Mulungu adaŵapatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:1

Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:2-4

Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika. Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:48

Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:54

Malamulo anu asanduka nyimbo yanga kulikonse kumene ndimapita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:13-14

Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-13

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:14

Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:3-5

Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu. Munthu wotere ndi wodzitukumula ndi kunyada, sadziŵa kanthu. Mtima wake ngwodwala, wongofuna zotsutsanatsutsana ndi kukangana pa mau chabe. Zimenezi zimabweretsa kaduka, kusamvana, kusinjirirana, kuganizirana zoipa, kupsetsana mtima kosalekeza pakati pa anthu amene nzeru zao zidaonongekeratu ndipo sazindikiranso choona. Iwo amayesa kuti kupembedza Mulungu ndi njira yopatira chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:8-9

Kale simunkadziŵa Mulungu, nchifukwa chake munkatumikira zomwe sizili milungu konse. Koma tsopano mukumdziŵa Mulungu, makamaka ndinene kuti Mulungu ndiye akudziŵa inu. Nanga bwanji mukubwereranso ku miyambo yachabe ndi yopanda phindu ija? Bwanji mukufuna kukhalanso akapolo ake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:16

Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:25

Ndangoti thapsa m'fumbi. Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11-12

Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu. Samalani mayendedwe anu pakati pa akunja, kuti ngakhale azikusinjirirani kuti ndinu anthu ochita zoipa, komabe aziwona ntchito zanu zabwino. Apo adzalemekeza Mulungu pa tsiku limene Iye adzaŵayendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:5-6

Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula. Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:28

Koma munthu aziyamba wadziwona bwino asanadyeko mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:18-19

Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:14

Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:16

“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:41

Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:14-16

Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:22

Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:5

Koma kunena za ife, chifukwa cha kulandira Mzimu Woyera ndiponso pakukhulupirira, tikuyembekeza kuti Mulungu adzatiwona kuti ndife olungama pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:14

Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:16

Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5

Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11-12

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:2-3

Ndikufunseni chinthu chimodzi chokha: Kodi mudalandira Mzimu Woyera pakutsata Malamulo, kapena pakumva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino? Tsono tikati mkhalapakati, ndiye kuti pali anthu aŵiri. Koma Mulungu ali yekha. Kodi ndiye kuti Malamulo a Mose amatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Mpang'ono pomwe. Anthu akadalandira malamulo otha kuŵapatsa moyo, pamenepo bwenzi atasanduka olungama kudzera mwa malamulowo. Koma Malembo akunenetsa kuti zinthu zonse zili mu ulamuliro wa uchimo, kuti pakukhulupirira Yesu Khristu, anthu okhulupirira alandiredi zimene Mulungu adalonjeza. Chisanafike chikhulupirirochi, tinali ngati akaidi m'manja mwa Malamulo, kudikira kuti chikhulupiriro chimene chidaati chifikecho, chiwululidwe. Motero Malamulowo anali ngati namkungwi wathu, mpaka atabwera Khristu, kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira. Popeza kuti tsopano chikhulupiriro chafika, namkungwiyo satilamuliranso. Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu. Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu. Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza. Kani ndinu opusa chotere? Kodi zimene Mzimu Woyera adayamba kuchita mwa inu, mukufuna kuzifikitsa pake penipeni tsopano ndi mphamvu zanuzanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:1

Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:3-6

Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona. Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi. Munthu akamati amakhala mwa Mulungu, zochita zake zizilingana ndi zimene Yesu ankachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:8

Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:6-7

Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina. Koma palibe konse uthenga wabwino wina. Pali anthu ena amene akukusokonezani, ndipo akufuna kupotoza Uthenga Wabwino wonena za Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:32-33

“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba. Koma aliyense wondikana pamaso pa anthu kuti Ine sandidziŵa, Inenso ndidzamkana pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba kuti sindimdziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:27

Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:1-4

Mlandireni bwino munthu amene chikhulupiriro chake nchofooka, koma osati kuti mutsutsane naye pa maganizo ake. Tsono iwe, ukuweruziranji mbale wako? Kapena iwe winawe, ukunyozeranji mbale wako? Tonsefe tidzaima pamaso pa Mulungu kuti atiweruze. Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ” Motero aliyense mwa ife adzadzifotokozera yekha kwa Mulungu zimene adazichita. Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa. Pogwirizana ndi maganizo a Ambuye Yesu, ndikutsimikiza mosakayika konse kuti palibe chinthu chingadetse munthu pamaso pa Mulungu chifukwa wachikhudza. Koma ngati wina aganiza kuti chinthu nchomudetsa, kwa iyeyo chinthucho nchomudetsadi. Ngati ukhumudwitsa mbale wako pakudya chakudya cha mtundu wakutiwakuti, ndiye kuti sukuyendanso m'chikondi. Usamuwononge ndi chakudya chako munthu amene Khristu adamufera. Tsono musalole kuti anthu ena aziyese zoipa zinthu zimene inu mumaziwona kuti nzabwino. Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka. Aliyense wotumikira Khristu motere, amakondweretsa Mulungu, ndipo amakhala wovomerezeka kwa anthu. Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu. Wina amakhulupirira kuti palibe choletsa kudya chakudya chilichonse. Koma wina, amene chikhulupiriro chake nchofooka, amadya zamasamba zokha. Chakudya chisakuwonongetseni ntchito ya Mulungu. Zakudya zonse nzololedwa kuzidya, koma nkulakwa kudya chinthu chimene chingachimwitse anzathu. Nkwabwino kusadya nyama, kusamwa vinyo, ndiponso kusachita kanthu kalikonse kamene kangachimwitse mbale wako. Zimene iwe umakhulupirira pa zimenezi, zikhale pakati pa iweyo ndi Mulungu. Ngwodala amene mtima wake sumutsutsa pamene atsimikiza kuchita zakutizakuti. Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo. Amene amadya chilichonse, asanyoze mnzake amene amazisala. Amene amasala zinthu zina asaweruze mnzake amene amazidya, pakuti Mulungu wamulandira. Kodi iweyo ndiwe yani kuti uweruze wantchito wamwini kuti walakwa? Mbuye wake yekha ndiye aweruze ngati iye wakhoza kapena walephera pa ntchito yake. Ndipo adzakhoza, popeza kuti Ambuye angathe kumkhozetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:16

Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wachikondi, ndikufuna kukutamandani ndi kudalitsa dzina lanu loyera. Ndikubwera pamaso panu kukuthokozani chifukwa cha zonse, chifukwa ndinu wabwino ndipo chifundo chanu chimakhalapo nthawi zonse. Zikomo chifukwa cha moyo, chifukwa cha thanzi langa, chifukwa dzanja lanu lamphamvu landilimbitsa. Zikomo chifukwa cha kuleza mtima kwanu pa ine, ndipo tsiku lililonse mumandisonyeza chikondi chanu ngakhale sindiyenera. Ambuye, panopa ndikudzipereka pamaso panu, ndikuvomereza zofooka zanga. Ndikudziwa kuti ndili ndi zolakwa zambiri ndipo ndikufunika thandizo lanu kuti ndikule m'mbali zonse za moyo wanga. Ndikukupemphani kuti mudzitamandidwe mwa ine, ndipo kuti ndikhale chitsanzo chabwino kwa onse amene ali pafupi nane pankhani ya chikhulupiriro changa mwa Khristu. Ndikufuna kuyenda molimba mtima popanda manyazi, ndipo khalidwe langa likuwonetseni inu m'zonse zimene ndimachita ndi kunena. Ndikupatsani ulemerero wonse, ulemu ndi kutamandidwa kosatha, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa