Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -



62 Mau a Mulungu Pa Mphatso ya Kulankhula Malilime

62 Mau a Mulungu Pa Mphatso ya Kulankhula Malilime


1 Akorinto 12:10

Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:28

Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:27-31

Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa? Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti munthu amene Mzimu wa Mulungu amamtsogolera, sanganene kuti, “Yesu atembereredwe.” Ndiponso, munthu amene Mzimu Woyera samtsogolera, sanganene kuti, “Yesu ndi Ambuye.” Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira? Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:30

Kodi onse ali ndi mphatso ya kuchiritsa matenda? Kodi onse angathe kulankhula zilankhulo zosadziŵika? Kodi onse angathe kuzitanthauzira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:1

Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4

Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:1-5

Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo. Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine. Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo. Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira. Ngati ndipemphera m'chilankhulo chosadziŵika, mtima wanga ukupemphera inde, koma nzeru zanga sizipindulapo kanthu pamenepo. Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena. Ngakhale inu muthokoze Mulungu bwinobwino, koma munthu winayo sapindulapo konse. Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu. Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu. Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi. Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima. M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.” Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira. Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala? Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima, ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi. Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo. Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha. Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena. Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa. Koma Mulungu akaulula kanthu kwa munthu wina amene ali pomwepo, amene akulankhulayo akhale chete. Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa. Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo. Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu, akazi akhale chete m'misonkhano ya mpingo, pakuti iwo saloledwa kulankhula. Monga Malamulo a Mose anenera, akazi azikhala omvera. Ngati ali ndi mafunso, akafunse amuna ao kunyumba. Pajatu nchamanyazi kuti mkazi alankhule mu msonkhano wa mpingo. Monga nkuti mau a Mulungu adachokera kwa inu? Kaya kapena adafika kwa inu nokha? Ngati wina akuyesa kuti akulankhula mau ochokera kwa Mulungu, kapena kuti akuuzidwa mau ndi Mzimu Woyera, avomereze kuti zimene ndikukulemberanizi ndi lamulo lochokera kwa Ambuye. Ngati munthuyo savomereza zimenezi, Mulungunso samuvomereza iyeyo. Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo. Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka. Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:5

Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:13

Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:1-2

Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo. Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine. Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo. Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira. Ngati ndipemphera m'chilankhulo chosadziŵika, mtima wanga ukupemphera inde, koma nzeru zanga sizipindulapo kanthu pamenepo. Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena. Ngakhale inu muthokoze Mulungu bwinobwino, koma munthu winayo sapindulapo konse. Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu. Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu. Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:26

Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:13-14

Nchifukwa chake munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, apemphere kuti alandirenso mphatso ya kuchitanthauzira. Ngati ndipemphera m'chilankhulo chosadziŵika, mtima wanga ukupemphera inde, koma nzeru zanga sizipindulapo kanthu pamenepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:27-28

Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:15

Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:39

Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:16-17

Mukayamika Mulungu ndi mtima wanu wokha, nanga munthu amene ali nanu pamodzi, koma sadziŵa zamumtimazo, angavomereze bwanji kuti, “Amen!” pa pemphero lanu lothokoza Mulungu, pamene sakudziŵa zimene inuyo mukunena. Ngakhale inu muthokoze Mulungu bwinobwino, koma munthu winayo sapindulapo konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:18-19

Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu. Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17

Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:22

Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:11

Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:23-25

Tsono ngati mpingo wonse usonkhana pamodzi, ndipo onse ayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, nanga mukaloŵa anthu osadziŵa kapena osakhulupirira, kodi iwo sadzayesa kuti ndinu amisala? Koma ngati onse alankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo munthu wosakhulupirira kapena wosadziŵa aloŵa, adzatsutsidwa ndi zonse zimene akumva. Mau onsewo adzamuloŵa mu mtima, ndipo zobisika za mumtima mwake zidzaonekera poyera. Pamenepo iye adzadzigwetsa choŵerama pansi ndi kupembedza Mulungu, ndipo adzavomereza kuti Mulungu ali pakati panudi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:26-28

Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo. Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:29-33

Kunena za olankhula mau ochokera kwa Mulungu, aŵiri kapena atatu alankhule, ndipo ena onse aweruze zimene iwowo akunena. Koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amalankhula ndi anthu, ndipo amaŵathandiza, amaŵalimbitsa mtima ndi kuŵasangalatsa. Koma Mulungu akaulula kanthu kwa munthu wina amene ali pomwepo, amene akulankhulayo akhale chete. Nonsenu mungathe kulankhula mau ochokera kwa Mulungu malinga nkupatsana mpata, kuti onse aphunzire ndi kulimbikitsidwa. Anthu amene ali ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, adziŵe kuilamulira mphatsoyo. Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:39-40

Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo. Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4-6

Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira. Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao. Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso. Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankaŵamva akulankhula chilankhulo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:11

ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:46

Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:6

Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:10-13

Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini. Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere. Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:1-2

Tsono ine, abale, sindidathe kulankhula nanu monga momwe ndimalankhulira ndi anthu amene ali ndi Mzimu Woyera. Koma ndidaayenera kulankhula nanu ngati anthu odalira zapansipano, kapenanso ngati ana akhanda m'moyo wanu wachikhristu. Popeza kuti Mulungu adachita kundituma, ndidakhazika maziko monga mmsiri waluso, ndipo wina akumanga pa mazikowo. Koma aliyense azichenjera pomanga. Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu. Pa mazikoŵa munthu angathe kumangapo ndi golide, siliva, miyala yamtengowapali, mitengo, udzu kapena mapesi. Koma ntchito za munthu aliyense zidzaonekera poyera, pamene tsiku la chiweruzo lidzaziwonetsa. Pakuti tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito za munthu aliyense. Zimene munthu adamanga pamazikopo zikadzakhalapobe, mwiniwakeyo adzalandira mphotho. Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto. Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene. Tsono musadzinyenge. Ngati wina mwa inu adziyesa wanzeru, kunena za nzeru za masiku ano, ameneyo ayambe wakhala ngati wopusa, kuti asanduke wanzeru. Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.” Ndidakumwetsani mkaka, osakupatsani chakudya cholimba, chifukwa simukadatha kuchidya. Ngakhalenso tsopano simungathe kuchidya,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1

Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:7

Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:1

Muziyesetsa kukhala nacho chikondi, komanso muike mtima pa mphatso zimene Mzimu Woyera amapereka, makamaka mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:12

Ndidakutsimikizirani mopirira kwambiri kuti ndine mtumwi, pakuchita pakati panu zizindikiro, zozizwitsa ndi ntchito zina zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-12

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:19-21

Musayese kuletsa ntchito ya Mzimu Woyera. Inu nomwe mukudziŵa bwino kuti tsiku la Ambuye likadzafika ngati mbala yausiku. Musanyoze mau olalikidwa m'dzina la Mulungu, koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:4

Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:1

Inu okondedwa, musamakhulupirira maganizo aliwonse, koma muziŵayesa maganizowo kuti muwone ngati ndi ochokeradi kwa Mulungu. Paja aneneri ambiri onama awanda ponseponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:21

Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:11-12

Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo, anthu a chilankhulo chamtundu. Adaakuuzani kuti, “Malo opumulira ndi ano, otopa apumule, malo ousira ndi ano,” koma inu simudamvere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:20

Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:12

Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:26-27

Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:10

Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:20

Abale, musamaganiza zachibwana. Pa zoipa, khalani ngati ana osadziŵa, koma pa maganizo anu, mukhale okhwima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:24

Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:20

Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:31

Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:14-17

Pamene atumwi okhala ku Yerusalemu adamva kuti anthu a ku Samariya alandira mau a Mulungu, adatumako Petro ndi Yohane. Iwowo atafika, adayamba kupempherera okhulupirira aja kuti alandire Mzimu Woyera. Nthaŵiyo nkuti Mzimu Woyera asanafike pa wina aliyense mwa iwo. Onsewo anali atangobatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Tsono Petro ndi Yohane adaŵasanjika manja, ndipo adalandira Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 15:8-9

Ndipo Mulungu amene amadziŵa mitima ya anthu, adaŵachitira umboni pakuŵapatsa Mzimu Woyera, monga adapatsira ifeyo. Mulungu sadasiyanitse konse pakati pa ife ndi iwo, koma adayetsera mitima yao ndi chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa