Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


149 Mau a Mulungu Okhudza Kufunika kwa Malamulo

149 Mau a Mulungu Okhudza Kufunika kwa Malamulo


Eksodo 20:1-17

Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati, Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. “Usaphe.” “Usachite chigololo.” “Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.” “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:15

“Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17-18

“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:5-6

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:10-11

Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 10:12-13

Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:10

Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:7-8

Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:3

Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:6

Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-40

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:34

Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu, ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:1

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndipo nthaŵi zonse muzimvera malamulo ndi malangizo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 22:31

“Tsono muzimvera malamulo anga ndi kuŵatsata. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34

Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:2

Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:2

Musaonjezerepo kanthu kena pa zimene ndakulamulani, ndipo musachotsepo kanthu. Muzimvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:25

Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:1

Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:19

Kuumbala si kanthu ai, kusaumbala si kanthunso. Kanthu nkutsata malamulo a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:32-33

Inu Aisraele, musamale ndithu kuchita zimene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, osapatukira ku dzanja lamanja kapena lamanzere. Muziyenda m'njira imene Chauta, Mulungu wanu, wakulamulani, kuti zinthu zidzakuyendereni bwino, ndipo mudzapitirire kukhala ndi moyo m'dziko limene mukakhalemolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 2:3

Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:22

Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:24

Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:4

atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti, “Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi, usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Yohane 1:6

Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:93

Sindidzaiŵala konse malangizo anu, pakuti mwandipatsa nawo moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:6

Tsono inu, muzichita monga momwe Chauta akulamulirani. Muziyenda m'njira zake ndipo muzimuwopa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:13

Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:1

Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:26

Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:21

“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:20-22

Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:16

Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:3-4

Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:172

Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 1:8

Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:16

Munthu womvera malamulo amadzisungira moyo, koma munthu wonyoza malangizo a Mulungu adzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 26:3-4

“Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi, Ndidzaononga akachisi anu opembedzerako mafano ku mapiri ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo lubani, ndipo ndidzaponya mitembo yanu pa mafano opanda moyo, ndipo ndidzadana nanu. Ndidzasandutsa mizinda yanu kuti ikhale mabwinja, ndidzasandutsanso malo anu achipembedzo kuti akhale opanda anthu, ndipo sindidzalolanso kumva fungo lokoma la zopereka zanu. Ndidzaononga dziko lanu kotero kuti adani anu amene adzakhale m'menemo adzadabwa. Ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndipo ndidzakupirikitsani, lupanga lili pambuyo. Dziko lanu lidzasanduka chipululu, ndipo mizinda yanu idzasanduka mabwinja. “Pa nyengo imeneyo nthaka idzakondwerera zaka zoipumitsa nthaŵi yonse pamene m'dzikomo mulibe anthu, inu muli m'dziko la adani anu. Pamenepo nthaka idzapuma ndi kukondwerera zaka zopumazo. Nthaŵi zonse pamene dzikolo lilibe anthu, nthaka idzapuma, kupuma kwake kumene sidapumepo pa zaka zonse pamene inu munkakhalamo. Ndipo ngakhale ena amene mudzatsalenu, ndidzaika mtima wa mantha mwa inu pamene muli m'dziko la adani anu. Mtswatswa wa tsamba louluka udzakuthaŵitsani. Mudzathaŵa monga m'mene munthu amathaŵira lupanga, ndipo mudzagwa pansi popanda okuthamangitsani. Mudzaphunthwitsana monga ngati mukuthaŵa nkhondo, ngakhale palibe amene akukupirikitsani. Ndipo simudzakhala ndi mphamvu zoti mulimbane ndi adani anu. Mudzatha, kuchita kuti psiti, pakati pa mitundu ya anthu, ndipo dziko la adani anu lidzakudyani. Ngakhale ena amene mudzatsalenu, nanunso mudzazunzika m'dziko la adani anu chifukwa cha machimo anu, ndipo mudzazunzikanso chifukwa cha machimo a makolo anu. ndidzakupatsani mvula pa nyengo yake, ndipo nthaka idzakubalirani zokolola zochuluka, ndipo mitengo yam'minda idzakubalirani zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:29

Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:47-48

Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu amene ndimaŵakonda. Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda, ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:31-32

Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:24

Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-2

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:39-40

Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai. koma nonsenu amene mudakangamira Chauta, Mulungu wanu, muli ndi moyo lero lino. Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 7:2

Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:10

“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:12

Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:35

Munditsogolere kuti ndimvere malamulo anu, chifukwa ndimakondwera nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:17

Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:19-20

Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo, Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:2-3

Chodziŵira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake. Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha. Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano. Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:97

Ndimakonda malamulo anu kwambiri, ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 24:7

Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:10

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:28

Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:45

ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:2-3

“Ine ndine Chauta Mulungu wako, amene ndidakutulutsa mu ukapolo ku dziko la Ejipito. Apo Mose adaŵayankha kuti, “Musaope, Mulungu wafika kuti akuyeseni, kuti muzimuwopa m'mitima mwanu, ndiponso kuti musachimwe.” Koma anthu ankaima kutali, Mose yekha ndiye adayandikira mtambo wamdima m'mene munali Mulungu. Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba. Musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide, kuti muziipembedzera kumodzi ndi Ine. Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani. Mukadzandimangira guwa lamiyala, miyala yake musadzaseme, chifukwa mukadzaisema ndi chitsulo chosemera, mudzaipitsa guwalo. Popita ku guwa langa, musadzaponde pa makwerero, kuti maliseche anu angaonekere.’ ” “Usakhale ndi milungu ina, koma Ine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:17

Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 27:10

Tsono mumvereni, ndipo musunge malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani leroŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:9

Pajatu malamulo amene amati, “Usachite chigololo, usaphe, usabe, usasirire”, ndiponso malamulo ena onse, amaundidwa mkota m'lamulo ili lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:61

Nchifukwa chake inu Aisraele, mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Mulungu wathu, ndipo mumvere bwino mau ake, ndi kutsata malamulo ake monga lero lino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:60

Ndimafulumira, sindizengereza kutsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:4

Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:4-5

Muzichita zimene ndikukulamulani, ndi kutsata malamulo anga ndi kuŵamvera. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu. Nchifukwa chake muchite zimene ndikukulamulani ndipo muzimvera malamulo anga, motero mudzakhala ndi moyo. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 19:5

Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:31

Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:16

“Uzilemekeza atate ako ndi amai ako, monga momwe Chauta, Mulungu wako, adakulamulira, kuti pakutero masiku a moyo wako achuluke ndipo kuti zinthu zikuyendere bwino m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:77

Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo, pakuti malamulo anu amandikondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:19

Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:1-2

Tsono aŵa ndi malamulo, malangizo ndi zina zoyenera kuzitsata, zimene Chauta, Mulungu wanu, adandilamula kuti ndikuphunzitseni. Muzikatsata zonsezi m'dziko limene mudzaloŵa ndi kukhalamolo, Chauta, Mulungu wathu, adalonjeza makolo anu aja Abrahamu, Isaki ndi Yakobe kuti adzakupatsani inu dziko limene lili ndi mizinda ikuluikulu ndi yachuma, imene inu simudaimange. Nyumba zake zidzakhala zodzaza ndi zinthu zabwino zimene inuyo simudaikemo. Zitsime zidzakhala zokumbiratu ndipo padzakhala minda yamphesa ndi yaolivi imene simudalime ndinu. Chauta akadzakuloŵetsani m'dziko limeneli, ndipo mukadzakhala ndi chakudya chambiri, musadzaiŵale Chauta amene adakutulutsani ku Ejipito, dziko laukapolo. Muziwopa Chauta, Mulungu wanu. Muzipembedza Iye yekha, ndipo mukamalumbira, muzitchula dzina lake lokha. Musamapembedza milungu ina, milungu imene amaipembedza anthu okhala mozunguliramu, popeza kuti mukatero, mkwiyo wa Chauta udzakuyakirani ngati moto, ndipo udzakuwonongani kwathunthu, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, amene amakhala pakati panu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Musamupute Chauta, Mulungu wanu, monga mudachitira ku Masa kuja. Musamale kuti musunge malamulo onse amene Iye akupatsani. Muzichita zokhazo zimene Chauta akuti ndi zolungama ndi zabwino, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Mudzalandira dziko labwinolo limene Chauta adalonjeza molumbira kuti adzapatsa makolo anu. Adani anu mudzaŵapirikitsa, monga Chauta adalonjezera. nthaŵi zonse pamene muli moyo, inu ndi zidzukulu zanu. Muzikaopa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muzikamvera malamulo ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsaniŵa, kuti pakutero mukakhale moyo nthaŵi yaitali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:13

Wonyoza malangizo amadziwononga, koma wosamala lamulo amalandira mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:17

Koma nkwapafupi kuti thambo ndi dziko lapansi zithe, kupambana kuti kalemba kakang'ono ka pa Malamulo kathe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:22

Muzimvera mokhulupirika zonse zimene ndakuuzanizi. Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, muzichita zonse zimene akulamulani, ndipo mukhale okhulupirika kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:18

Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:14

Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene ndikulamulani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 31:18

Chauta atatsiriza kulankhula ndi Mose pa phiri la Sinai lija, adampatsa Moseyo miyala iŵiri yaumboni, imene Mulungu mwini anali atalembapo kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21

“Si munthu aliyense womangonditi ‘Ambuye, Ambuye’ amene adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba ai. Koma adzaloŵe ndi wochita zimene Atate anga akumwamba afuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:28

Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:1-5

Mwana wanga, uvomere mau anga, ndi kusunga bwino malamulo anga. Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza. Nzeruyo idzakupulumutsa ku mayendedwe oipa, idzakuteteza kwa amtherakuŵiri, amene amasiya njira zolungama, namayenda m'njira zamdima. Iwoŵa amakondwa pochita zoipa, amasangalala ndi ntchito zosalungama. Anthu ameneŵa njira zao nzokhotakhota, makhalidwe ao ngonyenga. Udzapulumuka kwa mkazi wadama, kwa mkazi wachiwerewere wolankhula mau oshashalika, amene amasiya mwamuna wake wapaumbeta, kuiŵala chipangano chochita ndi Mulungu wake. Pakuti nyumba yake imatsenderekera ku imfa, njira zake zimamufikitsa kwa anthu akufa. Opita kwa iye, palibe ndi mmodzi yemwe wobwerako, sazipezanso njira zopita ku moyo. Uzitchera khutu ku nzeru, uziikapo mtima pa kumvetsa zinthu. Ndiye iwe, uzitsata njira za anthu abwino, uziyenda m'njira za anthu ochita chilungamo. Paja anthu olungama ndiwo adzakhale m'dziko, anthu okhulupirika ndiwo adzakhazikike m'menemo. Koma anthu oipa Mulungu adzaŵachotsa pa dziko, anthu onyenga adzaŵatulutsa m'dzikomo. Ndikutitu upemphe mtima wozindikira zinthu, ndi kupemba kuti ukhale womvetsa zinthu. Uziifunafuna nzeruyo ngati siliva, ndi kumaiwunguza ngati chuma chobisika. Ukatero, udzamvetsa za kuwopa Chauta, udzapeza nzeru za kudziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:21

Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 13:4

Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 19:8

Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:50

Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:142

Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:23

Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:4-5

atatewo adandiphunzitsa ndi mau akuti, “Ugwiritse mumtima mwako zimene ndikukuuzazi, usunge malamulo anga, kuti ukhale ndi moyo. Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:46-47

adati: Mukumbukire bwino malamulo onse amene ndakupatsani leroŵa. Muuze ana anu kuti azimvera mosamala mau onse a malamuloŵa. Mauŵa sikuti ndi mau achabe. Mau ameneŵa ndiwo moyo wanu. Muŵamvere, ndipo mudzakhalitsa m'dziko mukukakhalamolo uko kutsidya kwa Yordani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:168

Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:23

Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:33

Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu, ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:1

Chauta adauzanso Mose kuti, “Sema ina miyala ngati iŵiri yakale ija, kuti ndilembepo mau omwe anali pa miyala yoyamba udaphwanya ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:8

Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:1-2

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira. Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:153-154

Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:13

Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:4-5

“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko. Usagwadire fano lililonse kapena kumalipembedza, chifukwa Ine Chauta, Mulungu wako, ndine Mulungu wosalola kupikisana nane, ndipo ndimalanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:10-12

Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo. Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse. Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:13

Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:51

Ndithu ndikunenetsa kuti munthu akamvera mau anga, sadzafa konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:9

Chauta adzakusandutsani anthu opatulikira Iye monga adalonjezera, malinga mukachita zonse zimene akukulamulani ndi kuyenda m'njira yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:27

Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:27-28

Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:10

Koma ndimachitira chifundo chosasinthika anthu zikwi zambirimbiri amene amandikonda namasunga malamulo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 11:19-20

Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu. Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu aŵiri ameneŵa ndiwo amene amapangana zoipa nkumalangiza anthu zoipa mumzinda muno. Motero adzatsata malamulo anga, adzasunga ndi kumvera malangizo anga. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:59-60

Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu. Tsono anthu sadzandichititsa manyazi, ndikatsata malamulo anu onse. Ndimafulumira, sindizengereza kutsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:13-14

“Usaphe.” “Usachite chigololo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:11

Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:3

Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:16

“Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:5

Koma munthu akamasunga mau a Mulungu, pamenepo chikondi cha Mulungu chafikadi pake penipeni mwa iyeyo. Chotitsimikizitsa kuti tili mwa Iye, ndi chimenechi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:153

Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:6-8

Mukaŵasunge ndi kuŵatsata, ndipo chimenechi chidzaonetsa anthu a mitundu ina kuti ndinu anthu anzeru ndi omvetsa zinthu bwino. Akadzamva malamulo onseŵa, iwowo adzati, “Mtundu umenewu ndi waukulu, wanzeru ndi womvetsa zinthu bwino.” Palibe mtundu wina uliwonse, kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi Mulungu wokhala pafupi nawo, monga m'mene Mulungu wathu amakhalira ndi ife. Nthaŵi zonse tikamuitana, amatiyankha. Palibe mtundu wina uliwonse kaya ndi waukulu chotani, umene uli ndi malamulo ndi malangizo achilungamo onga aŵa amene ndakupatsani leroŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:14

Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 31:33

Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:19

lemekeza atate ako ndi amai ako, ndiponso konda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:17

Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:46

“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:63

Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-4

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu. Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe. Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wokongola ngati mkanda wam'khosi. Tsono udzayenda pa njira yako mosaopa, phazi lako silidzaphunthwa konse. Ukamakhala pansi, sudzachita mantha, ukamagona, udzakhala ndi tulo tabwino. Usamaopa zoopsa zobwera modzidzimutsa, usamachita mantha ndi tsoka lodzagwera anthu oipa. Chauta ndiye adzakhale chikhulupiriro chako, adzasunga phazi lako kuti lingakodwe. Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino. Usamkonzekere chiwembu mnzako, amene amakhala nawe pafupi mokudalira. Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:7

“Usatchule pachabe dzina la Chauta, Mulungu wako, chifukwa Mulunguyo sadzamleka aliyense wotchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:32

Musamale bwino kuti muchite zonse zimene ndakulamulani. Musaonjezepo kapena kuchotsapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:22

Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:24

Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:111-112

Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:8-9

Amangeni pamikono panu, ndiponso muŵaike pa mphumi pakati pa maso anu. Alembeni pa mphuthu za zitseko za nyumba zanu ndi pa zipata zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:32-36

“Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga. Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga. Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa. Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta. Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo. Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:58-59

Muzimvera mau onse a malamulo aŵa a m'buku muno, ndipo dzina ili lodabwitsa ndi lochititsa mantha la Chauta, Mulungu wanu, muzilitamanda. Mukapanda kutero, inuyo ndi zidzukulu zanu, Chauta adzakugwetserani masautso apadera, mavuto aakulu okhalitsa ndiponso nthenda zoopsa zosamva mankhwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:23

“Munthu wosavomerezana ndi Ine, ndiye kuti ngwotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ndiye kuti ameneyo ngwomwaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:151-152

Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:12

Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:15-16

Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:25

Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 29:9

Mau onse a chipangano ichi muŵamvere mokhulupirika, kuti choncho mudzakhoze pa zonse zimene mudzachite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:6

Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:4

Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:15-16

“Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa