Munthu aliyense ali ndi udindo pa zochita zake. Mulungu sakukakamiza chifuniro chake pa ife ayi, nthawi zonse amatipatsa njira ziwiri: yabwino ndi yoipa, temberero kapena dalitso, moyo kapena imfa, ndipo ndife amene timasankha. Chilichonse chimene timachita pa moyo wathu, timachita ndi chifukwa, kaya zisankho zathu zikhale zabwino kapena zoipa.
Ufulu wosankha uwu ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo pa izi, Mulungu sali nawo mphamvu, chifukwa munthu aliyense amasankha chomwe akuona kuti ndi choyenera. Zina timazichita chifukwa cha chilakolako champhamvu, pamene zina timazichita popanda kudziwa kuti tikufunadi kuchita zimenezo.
Apa ndiye pali mfundo ya ufulu wosankha: kusankha mogwirizana ndi zomwe tikufuna. Ufulu wosankha umenewu umatibweretsera pa mikhalidwe iwiri yauzimu: "kupulumuka kapena kutayika" (Yohane 3:36). "Wokhulupirira Mwana ali nawo moyo wosatha; koma wosakhulupirira Mwana sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”
Ine ndasankhula njira yoti ndizikhala wokhulupirika, ndaika malangizo anu mumtima mwanga.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Ndidzapereka nsembe kwa Inu mwaufulu. Ndidzatamanda dzina lanu, Inu Chauta, popeza kuti ndinu abwino.
Ngatitu ndikugwira ntchitoyi mofuna ine ndekha, ndiye kuti ndilandirapo mphotho. Koma ngati ndiigwira mosafuna ine ndekha, ndiye kuti ntchitoyo ndi udindo umene Ambuye adandipatsa.
Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,
Pitani mukalirire milungu imene mwaisankhulayo. Ikupulumutseni milungu imeneyo pa nthaŵi ya kuzunzika kwanu.”
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Aliyense wofuna kuchita kufuna kwa Mulungu, adzadziŵa ngati zimene Ine ndimalankhula nzochokera kwa Mulungu kapena kwa Ine ndekha.
kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
Tsono mkaziyo adaona kuti mtengowo ndi wokongola, ndiponso kuti zipatso zake zingakhale zokoma kudya. Pompo adayamba kukhumbira kuti adyeko zipatsozo, adzakhale wanzeru. Motero adathyolako zipatso zina za mtengowo, naadya. Tsono zina adapatsako mwamuna wake, ndipo iyenso adadya.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere. Anthu oika mtima pa khalidwe lokonda zoipa, amadana ndi Mulungu. Anthu otere sagonjera Malamulo a Mulungu, ndipo kunena zoona, sangathedi kuŵagonjera. Ndipo anthu oika mtima pa khalidwe limenelo, sangathe kukondweretsa Mulungu.
“Tsono inu, opani Chauta ndipo mumtumikire moona ndi mokhulupirika. Chotsani milungu imene makolo anu ankaipembedza pambali pa mtsinje wa Yufurate ndi ku Ejipito, ndipo mutumikire Chauta. Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
Ndipo Chauta adamlamula munthuyo kuti, “Uzidya zipatso za mtengo uliwonse wam'mundawu, kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”
Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
Paja Chauta akuti, “Ofulidwa amene amalemekeza masiku a Sabata, amene amachita zokomera Ine, ndi kusunga chipangano changa mokhulupirika, Ineyo ndidzaŵapatsa dzina ndi mbiri yabwino pakati pa anthu anga, m'kati mwa fuko langa, koposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi. Ndidzaŵapatsa mbiri yabwino yosatha, yosaiŵalika.”
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza.
nonsenu ndidzakufetsani ku nkhondo. Nonsenu mudzaphedwadi, chifukwa simudayankhe m'mene ndidakuitanani, ndipo simudamve m'mene ndidalankhula, koma mudachita zoipa pamaso panga. Mudasankha kuchita zoipa m'malo mwa zabwino.”
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.
“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.
“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. Kapolo sakhala nao m'banja nthaŵi zonse, koma mwana. Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu.
Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Inde muzikhala ngati mfulu, koma ufulu wanuwo usakhale ngati chinthu chophimbira zoipa. Koma khalani ngati atumiki a Mulungu.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Lero ndikukupatsani zinthu ziŵiri kuti musankhepo, madalitso kapena matemberero. Madalitso kwa inu, mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, amene ndikukupatsani leroŵa. Koma matemberero kwa inu, mukapanda kumvera malamulo ameneŵa, nkusiya njira imene ndikukulamulani lero, kuti mutembenukire kwa milungu ina ndi kumaipembedza, milungu imene nkale lonse simudaipembedzepo.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Anyamata inu, muzikondwerera unyamata wanu. Mitima yanu izisangalala pa nthaŵi ya unyamata wanu. Inde muzitsata zimene mtima wanu ukufuna, ndiponso zimene maso anu akupenya. Koma mudziŵe kuti pa zonsezo Mulungu adzakuweruzani.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha.
Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata. Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti moyo umene ali nawo munthu si wake. Munthu sangathe kudzitsogolera yekha.
Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Popeza kuti mudadana ndi nzeru, ndipo simudasankhe kuwopa Chauta, kuti alandire mwambo wochita zinthu mwanzeru, akhale angwiro, achilungamo ndi osakondera. popeza kuti simudasamale malangizo anga, ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse, basitu tsono mudzadya zipatso zoyenera ntchito zanuzo, mudzakhuta zoipa zimene munkafuna kuŵachita ena.
koma chofunika nchimodzi chokha. Maria ndiye wasankhula chinthu chopambana, ndipo chimenechi palibe wina angamlande ai.”
Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya.
Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.