Dziko lauzimu lilipoli, ndipo mmenemo timayenera kuchita nkhondo ndi pemphero komanso ndi mawu a Mulungu. Nkhondo zazikulu zimamenyedwa m’dziko lauzimu limeneli. M’dziko lauzimuli ndi kumene mphamvu zodabwitsa za Mulungu zimaonekera. Si kumene timangomenyana ndi mizimu yoipa yokha ayi, komanso kumene umapezera zodabwitsa ndi chipambano m’moyo wako.
Pakuti nkhondo yathu si yolimbana ndi anthu, koma ndi olamulira, ndi akuluakulu, ndi mafumu a dziko la mdima lino, ndi makamu a mizimu yoipa m’malo akumwamba. (Aefeso 6:12) Apa Mulungu akutiuza za dziko lauzimu limeneli, kumene ukhoza kupambana pokhapokha wodzazidwa ndi mphamvu zake.
Ngakhale kuti timakhala m’dzikoli, sitimenya nkhondo monga mmene dziko limamenyera. Zida zathu za nkhondo si za dziko lino, koma zili ndi mphamvu ya Mulungu yogumula mipanda. (2 Akorinto 10:3-4)
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Ndimasamba m'manja kuwonetsa kuti sindidachimwe, ndimakupembedzani pa guwa lanu lansembe, Inu Chauta.
Ndimaimba molimbika nyimbo yothokozera, ndimalalika ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Pajatu chilichonse chimene Mulungu adalenga nchabwino, palibe chilichonse choti munthu asale, akamachilandira moyamika Mulungu,
pakuti chimayeretsedwa ndi mau a Mulungu ndi mapemphero aja.
Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo, ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.
Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati, “Chauta ndi wabwino, chikondi chake pa Israele nchamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa.
Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye.
Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.
Khalani okondwa nthaŵi zonse.
Muzipemphera kosalekeza.
Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya.
Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.”
Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo,
omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina,
sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo.
Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.”
Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani ndi kuwononga chakudya chonse,
Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake, Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo.
Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza, khosi lake lidavekedwa unyolo,
mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi. Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe.
Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
Nthaŵi zonse ndimayamika Mulungu wanga chifukwa cha inu, popeza kuti adakukomerani mtima mwa Khristu Yesu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse.
Apereke nsembe zothokozera, ndi kulalika ntchito za Chauta, poimba nyimbo zachimwemwe.
Mitengo yam'nkhalango idzaimbira Chauta mokondwa, pamene adzabwera kudzalamulira dziko lapansi.
Thokozani Chauta, pakuti ngwabwino, chikondi chake chosasinthika nchamuyaya.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu.
Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo.
Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Inde ankamudziŵa Mulungu, koma m'malo mwa kumtamanda kapena kumthokoza, maganizo ao adasanduka opanda pake, ndipo m'mitima yao yopusa mudadzaza mdima.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani.
Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu,
kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Koma Inu Mulungu mudzaŵaponya adani anga m'dzenje lozama lachiwonongeko. Anthu okhetsa magazi ndi onyenga sadzafika ngakhale theka la masiku ao. Koma ine ndidzadalira Inu.
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
“Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga.
Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.
Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa.
Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.
Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.