2 Samueli 22 - Buku LopatulikaNyimbo yoyamikira Yehova ya Davide ( Mas. 18 ) 1 Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo. 2 Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi. 3 Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa. 4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga. 5 Pakuti mafunde a imfa anandizinga, mitsinje ya zopanda pake inandiopsa ine. 6 Zingwe za kumanda zinandizingira; misampha ya imfa inandifikira ine. 7 M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake. 8 Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira. Maziko a dziko la kumwamba anasunthika. Nagwedezeka, chifukwa Iye anakwiya. 9 M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao. 10 Anaweramitsa miyambanso, natsika; ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake. 11 Ndipo Iye anaberekeka pa kerubi nauluka; inde anaoneka pa mapiko a mphepo. 12 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye, kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga. 13 Cheza cha pamaso pake makala a moto anayaka. 14 Yehova anagunda kumwamba; ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ake. 15 Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza; mphezi, nawaopsa. 16 Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake. 17 Iye anatumiza kuchokera kumwamba nanditenga; Iye ananditulutsa m'madzi aakulu. 18 Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu. 19 Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga. 20 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu; Iye anandipulumutsa, chifukwa akondwera ndi ine. 21 Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho. 22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga. 23 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga; ndipo za malemba ake, sindinawapatukire. 24 Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye, ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga. 25 Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwanga pamaso pake. 26 Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo, ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro. 27 Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza. 28 Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse. 29 Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga. 30 Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu; ndi Mulungu wanga ndilumphira linga. 31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye. 32 Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu? 33 Mulungu ndiye linga langa lamphamvu; ndipo Iye ayendetsa angwiro mu njira yake. 34 Iye asandutsa mapazi ake akunga mapazi a mbawala; nandiika pa misanje yanga. 35 Iye aphunzitsa manja anga nkhondo; kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa. 36 Ndiponso munandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu; ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa. 37 Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, ndi mapazi anga sanaterereke. 38 Ndinapirikitsa adani anga, ndi kuwaononga; ndiponso sindinabwerere mpaka nditawatha. 39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga. 40 Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira. 41 Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo, kuti ndiwalikhe akudana ndi ine. 42 Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa; ngakhale kwa Yehova, koma Iye sanawayankhe. 43 Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati fumbi la padziko, ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala. 44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine. 45 Alendo adzandigonjera ine, pakumva za ine, adzandimvera pomwepo. 46 Alendo adzafota, nadzabwera ndi kunthunthumira otuluka mokwiririka mwao. 47 Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa; 48 inde Mulungu wakundibwezera chilango ine, ndi kundigonjetsera anthu a mitundu. 49 Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa. 50 Chifukwa chake ndidzakuongani Yehova, pakati pa amitundu, ndipo ndidzaimba zolemekeza dzina lanu. 51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi