Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:51 - Buku Lopatulika

51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 Iye apatsa mfumu yake chipulumutso chachikulu; naonetsera chifundo wodzozedwa wake, kwa Davide ndi mbeu yake ku nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 Mulungu amathandiza mfumu yake kuti izipambana nthaŵi ndi nthaŵi. Amaonetsa chikondi chake chosasinthika kwa wodzozedwa wake, ndiye kuti kwa Davide ndi kwa zidzukulu zake mpaka muyaya.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.”

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:51
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi.


Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa: Atero Davide mwana wa Yese, atero munthu wokwezedwa, ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo, ndi mwini nyimbo yokoma ya Israele.


Ndipo nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi ku nthawi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika ku nthawi zonse.


Ndiye amene apatsa mafumu chipulumutso: Amene alanditsa Davide mtumiki wake kulupanga loipa.


Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.


Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!


Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.


Mulungu adziwika m'zinyumba zake ngati msanje.


Ndapeza Davide mtumiki wanga; ndamdzoza mafuta anga oyera.


Koma chikhulupiriko changa ndi chifundo changa zidzakhala naye; ndipo nyanga yake idzakwezeka m'dzina langa.


Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.


Ndidzakhalitsanso mbeu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m'mwamba.


Mbeu yake idzakhala kunthawi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuwa pamaso panga.


Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.


koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene Ndidzawaukitsira.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa