Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:16 - Buku Lopatulika

16 Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Chauta adakhuluma mokalipa, pamene adatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:16
12 Mawu Ofanana  

M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao.


ndi kuti, Ufike mpaka apa, osapitirirapo; apa adzaletseka mafunde ako odzikuza?


Ndipo anadzudzula Nyanja Yofiira, ndipo inaphwa: Potero anawayendetsa mozama ngati m'chipululu.


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Tamverani, mapiri inu, chitsutsano cha Yehova, ndi inu maziko olimba a dziko lapansi; pakuti Yehova ali nacho chitsutsano ndi anthu ake, ndipo adzatsutsana ndi Israele.


Adzudzula nyanja, naiphwetsa, naumitsa mitsinje yonse; Basani ndi Karimele afota, ndi duwa la ku Lebanoni linyala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa