Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:20 - Buku Lopatulika

20 Iye ananditulutsanso ku malo aakulu; Iye anandipulumutsa, chifukwa akondwera ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Iye ananditulutsanso ku malo akulu; Iye anandipulumutsa, chifukwa akondwera ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:20
16 Mawu Ofanana  

Ndipo anachoka kumeneko nakumba chitsime china; koma sanakangane nacho chimenecho; ndipo anatcha dzina lake Rehoboti; ndipo anati, Chifukwa kuti tsopano Yehova anatipatsa ife malo, ndipo tidzabalana m'dziko muno.


Koma Iye akatero kuti, Sindikondwera nawe konse; onani, ndine pano, andichitire chimene chimkomera.


Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga, ndi mapazi anga sanaterereke.


Ndipo Yabezi anaitana kwa Mulungu wa Israele, ndi kuti, Mundidalitse ndithu, ndi kukulitsa malire anga; ndi dzanja lanu likhale ndi ine, nimundisunge, kuti choipa chisandivute. Ndipo Mulungu anafikitsa chopempha iye.


M'mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova; anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Popeza Yehova akondwera nao anthu ake; adzakometsa ofatsa ndi chipulumutso.


Adadzitengera kwa Yehova; kuti adzampulumutsa, amlanditse tsopano popeza akondwera naye.


Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.


Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto.


Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


Amakhulupirira Mulungu; Iye ampulumutse tsopano, ngati amfuna; pakuti anati, Ine ndine Mwana wa Mulungu.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa