Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:49 - Buku Lopatulika

49 Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

49 Amene anditulutsa kwa adani anga; inde mundikweza ine pamwamba pa iwo akundiukira; mundipulumutsa kwa munthu wachiwawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

49 Ndinu amene mudandipulumutsa kwa adani anga. Mudandikweza pamwamba pa ondiwukira, mudandilanditsa kwa anthu ankhanza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

49 amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:49
11 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.


Ndipo Davide anazindikira kuti Yehova anamkhazikitsa mfumu ya Israele, ndi kuti anakulitsa ufumu wake chifukwa cha anthu ake Israele.


Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa;


Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.


Andipulumutsa kwa adani anga. Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine, mundikwatula kwa munthu wachiwawa.


Mwa Inu tidzakankhira pansi otsutsana nafe, m'dzina lanu tidzapondereza akutiukira ife.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa.


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa