Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:44 - Buku Lopatulika

44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwe adzanditumikira ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga; munandisunga ndikhale mutu wa amitundu; Anthu amene sindinawadziwa adzanditumikira ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 “Mudandipulumutsa kwa anthu anga ondiwukira. Mudandisunga kuti ndikhale wolamulira mitundu yonse. Choncho anthu osaŵadziŵa adayamba kunditumikira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:44
26 Mawu Ofanana  

Ndipo iye anakopa mitima ya anthu onse a Yuda, monga munthu mmodzi, natumiza iwo kwa mfumu, nati, Mubwere inu ndi anyamata anu onse.


Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.


Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.


Ndipo panali nkhondo nthawi yaitali pakati pa nyumba ya Saulo ndi nyumba ya Davide. Koma Davide analimba chilimbire, ndi nyumba ya Saulo inafooka chifokere.


Pomwepo mafuko onse a Israele anabwera kwa Davide ku Hebroni, nalankhula nati, Taonani, ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.


Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m'maiko ambiri.


Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu; mwandiika mutu wa amitundu; mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.


Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.


Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.


Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwe, ndi mtundu umene sunakudziwe udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele; pakuti Iye wakukometsa.


Pakuti mtundu ndi ufumu umene udzakana kukutumikira udzaonongeka; inde mitundu imeneyo idzasakazidwa ndithu.


Iwo amene sanafunse za Ine andifunafuna; ndi iwo amene sanandipwaire andipeza; ndinati, Taonani Ine, taonani Ine, kwa mtundu umene sunatchule dzina langa.


Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire; ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzaonongeka.


Ndipo ndidzadzibzalira iye m'nthaka, ndipo ndidzachitira chifundo Wosachitidwa-chifundo; ndipo ndidzati kwa Si-anthu-anga, Muli anthu anga; ndipo iwo adzati, Ndinu Mulungu wathu.


Ndiponso, Yesaya ati, Padzali muzu wa Yese, ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu; Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.


Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhale anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.


Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa