Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:39 - Buku Lopatulika

39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sangathe kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka, inde anagwa pansi pa mapazi anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Ndidaŵakantha, ndidaŵagwetsa pansi, kotero kuti sadadzukenso, ndidaŵapondereza ndi mapazi anga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:39
9 Mawu Ofanana  

Pakuti Inu munandimanga m'chuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; munandigonjetsera akundiukira.


Ndipo mfumu inalamula iwo, natuta miyala yaikuluikulu ya mtengo wapatali, kuika maziko ake a nyumbayo ndi miyala yosemasema.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza, ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Ndipo mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa kumapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.


Ndipo kunali, atatulutsira Yoswa mafumu awa, Yoswa anaitana aamuna onse a Israele, ndipo anati kwa akazembe a anthu a nkhondo amene anamuka naye, Yandikirani, pondani pa makosi a mafumu awa. Nayandikira iwo, naponda pa makosi ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa