Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:31 - Buku Lopatulika

31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:31
18 Mawu Ofanana  

Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.


ndipo munampeza mtima wake wokhulupirika pamaso panu, nimunapangana naye kumpatsa dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, ndi Aperizi, ndi Ayebusi, ndi Agirigasi, kulipereka kwa mbumba zake; ndipo mwakwaniritsa mau anu, popeza Inu ndinu wolungama.


Chifukwa chake mundimvere ine, eni nzeru inu, nkutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.


Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda.


Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.


Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.


Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.


Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.


Gwirani chikopa chotchinjiriza, ukani kundithandiza.


Onani, Mulungu, ndinu chikopa chathu; ndipo penyani pa nkhope ya Wodzozedwa wanu.


Adzakufungatira ndi nthenga zake, ndipo udzathawira kunsi kwa mapiko ake; choonadi chake ndicho chikopa chotchinjiriza.


Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.


Ndidziwa kuti zonse Mulungu azichita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kuchotsapo; Mulungu nazichita kuti anthu akaope pamaso pake.


Atatha masiku awa tsono, ine Nebukadinezara ndinakweza maso anga kumwamba, ndi nzeru zanga zinandibwerera; ndipo ndinalemekeza Wam'mwambamwamba, ndi kumyamika ndi kumchitira ulemu Iye wokhala chikhalire; pakuti kulamulira kwake ndiko kulamulira kosatha, ndi ufumu wake ku mibadwomibadwo;


Tsono ine Nebukadinezara ndiyamika, ndi kukuza, ndi kulemekeza Mfumu ya Kumwamba, pakuti ntchito zake zonse nzoona, ndi njira zake chiweruzo; ndi oyenda m'kudzikuza kwao, Iye akhoza kuwachepetsa.


Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.


Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.


Ndipo aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu Inu ya nthawi zosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa