2 Samueli 22:22 - Buku Lopatulika22 Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Ine ndidatsata njira za Chauta sindidachite zoipa ndi kumsiya Mulungu wanga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga. Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.