Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:9 - Buku Lopatulika

9 M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 M'mphuno mwake munatuluka utsi, ndi moto wotuluka m'kamwa mwake unaononga; makala anayaka nao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:9
17 Mawu Ofanana  

Cheza cha pamaso pake makala a moto anayaka.


Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka, maziko a dziko anaonekera poyera, ndi mtonzo wa Yehova, ndi mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwake.


Atayika ndi mpweya wa Mulungu, nathedwa ndi mpumo wa mkwiyo wake.


Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi, nafukuka maziko a dziko lapansi, mwa kudzudzula kwanu, Yehova, mwa mpumo wa mpweya wa m'mphuno mwanu.


Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.


Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.


Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati moto wonyeketsa pamwamba paphiri, pamaso pa ana a Israele.


Taonani, dzina la Yehova lichokera kutali, mkwiyo wake uyaka, malawi ake ndi aakulu; milomo yake ili yodzala ndi ukali, ndi lilime lake lili ngati moto wonyambita;


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Ndipo ndidzawapititsa iwo pamodzi ndi adani ako kudziko limene sudziwa iwe; pakuti moto wayaka m'mkwiyo wanga, umene udzatentha inu.


Chifukwa chake Yehova Mulungu wa makamu atero, Chifukwa munena mau awa, taona, ndidzayesa mau anga akhale m'kamwa mwako ngati moto, anthu awa ndidzayesa nkhuni, ndipo udzawatha iwo.


Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake.


Pakuti wayaka moto mu mkwiyo wanga, utentha kumanda kunsi ukutha dziko lapansi ndi zipatso zake, nuyatsa maziko a mapiri.


Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa