Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 22:7 - Buku Lopatulika

7 M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali mu Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova, inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga; ndipo Iye anamva mau anga ali m'Kachisi wake, ndi kulira kwanga kunafika ku makutu ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga, ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:7
16 Mawu Ofanana  

Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao, ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.


Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.


Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.


M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva mu Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.


Ndipo Yehova anati, Ndapenyetsetsa mazunzo a anthu anga ali mu Ejipito, ndamvanso kulira kwao chifukwa cha akuwafulumiza; pakuti ndidziwa zowawitsa zao;


Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu; koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.


Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova; ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.


Koma Yehova ali mu Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.


Ndipo pokhala Iye m'chipsinjo mtima anapemphera kolimba koposa ndithu: ndi thukuta lake linakhala ngati madontho aakulu a mwazi alinkugwa pansi.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa