Ndipo Mulungu ananena mau onse amenewa, nati, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iliyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena nyama zako, kapena mlendo amene ali m'mudzi mwako; chifukwa m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe. Usaphe. Usachite chigololo. Usabe. Usamnamizire mnzako. Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.
ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse. Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu;
Ndipo Yesu anati kwa iye, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiwiri lolingana nalo ndili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini. Pomwepo anatumizanso akapolo ena, nanena, Uzani oitanidwawo, Onani, ndakonza phwando langa; ng'ombe zanga, ndi zonona ndinazipha, ndi zinthu zonse zapsa: idzani kuukwati. Pa malamulo awa awiri mpokolowekapo chilamulo chonse ndi aneneri.
Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.
Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.
Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?
Buku ili la chilamulo lisachoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kuchita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzachita mwanzeru.
Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo.
Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.
Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita; Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu. Ndipo ndidzasandutsa mizinda yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma. Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako. Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi mizinda yanu idzakhala bwinja. Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake. Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo. Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola. Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu. Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani. Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo. ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.
Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?
Ndipo munthu amene asunga malamulo ake akhala mwa Iye, ndi Iye mwa munthuyo. Ndipo m'menemo tizindikira kuti akhala mwa ife, kuchokera mwa Mzimu amene anatipatsa ife.
Chifukwa chake muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga chilangizo chake, ndi malemba ake, ndi maweruzo ake, ndi malamulo ake, masiku onse.
Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe.
Taonani, ndilikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero; dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.
Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli ophunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.
nusunge chilangizo cha Yehova Mulungu wako, kuyenda m'njira zake, kusunga malemba ndi malamulo ndi maweruzo ndi umboni wake, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose, kuti ukachite mwa nzeru m'zonse ukachitazo, ndi kumene konse ukatembenukirako;
ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha;
Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.
Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.
Ha? Mwenzi akadakhala nao mtima wotere wakundiopa Ine, ndi kusunga malamulo anga masiku onse, kuti chiwakomere iwo ndi ana ao nthawi zonse!
Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba.
Muzisunga malemba ake, ndi malamulo ake, amene ndikuuzani lero lino, kuti chikukomereni inu ndi ana anu akukutsatani, ndi kuti masiku anu achuluke padziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu kosatha.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokhapokha pokhala ine ndilipo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani ntchito yake ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira; pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.
ndipo anati, Ngati udzamveratu mau a Yehova, Mulungu wako, ndi kuchita zoona pamaso pake, ndi kutchera khutu pa malamulo ake, ndi kusunga malemba ake onse, za nthenda zonse ndinaziika pa Aejipito sindidzaziika pa iwe nnena imodzi; pakuti Ine Yehova ndine wakuchiritsa iwe.
Mverani atsogoleri anu, nimuwagonjere; pakuti alindirira moyo wanu, monga akuwerengera; kuti akachite ndi chimwemwe, osati mwachisoni: pakuti ichi sichikupindulitsani inu.
pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama.
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a padziko lapansi; Ndipo anthu onse a padziko lapansi adzaona kuti akutchulani dzina la Yehova; nadzakuopani. Ndipo Yehova adzakuchulukitsirani zokoma, m'zipatso za thupi lanu, ndi m'zipatso za zoweta zanu, ndi m'zipatso za nthaka yanu, m'dziko limene Yehova analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani ilo. Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita; osapatukira mau ali onse ndikuuzani lero, kulamanja, kapena kulamanzere, kutsata milungu ina kuitumikira. Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani. Mudzakhala otembereredwa m'mzinda, ndi otembereredwa pabwalo. Lidzakhala lotembereredwa dengu lanu ndi choumbiramo mkate wanu. Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu. Mudzakhala otembereredwa polowa inu, ndi otembereredwa potuluka inu. ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu;
Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.
Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu; ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.
Anthu onse amvere maulamuliro a akulu; pakuti palibe ulamuliro wina koma wochokera kwa Mulungu; ndipo iwo amene alipo aikidwa ndi Mulungu.
popeza ndikuuzani lero kukonda Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake, ndi kusunga malamulo ake ndi malemba ake ndi maweruzo ake, kuti mukakhale ndi moyo ndi kuchuluka, ndi kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni m'dziko limene mulowako kulilandira.
monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;
Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
ndipo chimene chilichonse tipempha, tilandira kwa Iye, chifukwa tisunga malamulo ake, ndipo tichita zomkondweretsa pamaso pake.
Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.
ndi kuwachitira chifundo anthu zikwizikwi a iwo amene akondana ndi Ine, nasunga malamulo anga.
Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.
nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.
Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadze kupasula, koma kukwaniritsa. Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse. Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba.
Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.
Ndipo tsopano, ngati mudzamvera mau anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa cha padera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa;
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza. Komatu m'chilamulo cha Yehova muli chikondwerero chake; ndipo m'chilamulo chake amalingirira usana ndi usiku.
dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino; koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu ina imene simunaidziwa.
Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.
Ndipo ukadzayenda m'njira zanga kusunga malemba anga ndi malamulo anga, monga atate wako Davide anayendamo, Ine ndidzachulukitsa masiku ako.
Muzisunga mwachangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zake, ndi malemba ake, amene anakulamulirani.
Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.
Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.
Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.
Ndipo iye anayankha nati, Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu yako yonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mnansi wako monga iwe mwini.
Chotero chilamulo chili choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Mukana kusunga zouza zanga ndi malamulo anga kufikira liti?
Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;
Musamaonjeza pa mau amene ndikuuzani, kapena kuchotsapo, kuti musunge malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani.
Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake. Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi. Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa. Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva. ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe. Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.
Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.
kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.
Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.
Pakuti mau amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo; Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.
Potero muzisamalira kuchita monga Yehova Mulungu wanu anakulamulirani; musamapatuka kulamanzere kapena kulamanja. Muziyenda m'njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani, kuti mukakhale ndi moyo, ndi kuti chikukomereni, ndi kuti masiku anu achuluke m'dziko limene mudzakhala nalo lanulanu.
Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwe; chifukwa inakhazikika pathanthwepo. Ndipo yense akamva mau anga amenewa, ndi kusawachita, adzafanizidwa ndi munthu wopusa, yemwe anamanga nyumba yake pamchenga; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.
Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino:
Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.
Ndipo Samuele anati, Kodi Yehova akondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zophera, monga ndi kumvera mau a Yehova? Taonani, kumvera ndiko kokoma koposa nsembe, kutchera khutu koposa mafuta a nkhosa zamphongo. Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.
Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine, ngodala akusunga njira zanga. Imvani mwambo, mukhale anzeru osaukana.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kuchita malamulo ake ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero lino.
Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.
Zimenenso mudaziphunzira, ndi kuzilandira, ndi kuzimva, ndi kuziona mwa ine, zomwezo chitani; ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi ndi inu.
Koma samalirani bwino kuti muchite chilangizo ndi chilamulo zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulirani, kukonda Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zake zonse ndi kusunga malamulo ake, ndi kumuumirira Iye, ndi kumtumikira Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa mu unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.
Munthu aliyense wakudza kwa Ine, ndi kumva mau anga, ndi kuwachita, ndidzakusonyezani amene afanana naye. Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunathe kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino. Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.
kuti usunge lamulolo, lopanda banga, lopanda chilema, kufikira maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu;
Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang'ono, ndi mlendo wokhala m'midzi mwanu, kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mau onse a chilamulo ichi; ndi kuti ana ao osadziwa amve, naphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu kudziko kumene muolokera Yordani kulilandira likhale lanulanu.
Ndipo tsopano, pamaso pa Aisraele onse, khamu la Yehova, ndi m'makutu a Mulungu wathu, sungani, nimufunefune malamulo onse a Yehova Mulungu wanu, kuti mukhale nalo lanulanu dziko lokoma ili, ndi kulisiyira ana anu pambuyo panu cholowa chao kosalekeza.
Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.
Ndipo Iye anayankha, nati kwa iwo, Inunso mulumphiranji lamulo la Mulungu chifukwa cha miyambo yanu? Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nao opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israele. Ndipo Yesu anaitana ophunzira ake, nati, Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira. Ndipo ophunzira ananena kwa Iye, Tiione kuti mikate yotere m'chipululu yakukhutitsa unyinji wotere wa anthu? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Muli nayo mikate ingati? Ndipo iwo anati, Isanu ndi iwiri, ndi tinsomba pang'ono. Ndipo Iye analamulira anthuwo akhale pansi onse; natenga mikateyo isanu ndi iwiri ndi nsombazo; nayamika Mulungu, nanyema, napatsa kwa ophunzira, ndi ophunzira kwa anthu. Ndipo onsewa anadya, nakhuta: ndipo anatola makombo otsala madengu asanu ndi awiri odzala. Ndipo anadyawo anali amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana. Ndipo m'mene Iye anauza makamuwo amuke, analowa m'ngalawa, nafika m'malire a Magadani. Pakuti Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo, Wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Aliyense amene anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mau a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.
amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;
Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.
Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine.
ngati mudzamvera mau a Yehova Mulungu wanu, kuwasunga malamulo ake ndi malemba ake olembedwa m'buku la chilamulo ichi; ngati mudzabwerera kudza kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse.
Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;
ndi kuchitira chifundo anthu zikwi, a iwo amene akondana ndi Ine nasunga malamulo anga.
Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.