Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 15:10 - Buku Lopatulika

10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Iye ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ngati mutsata malamulo anga, mudzakhala m'chikondi changa, monga momwe Ine ndatsatira malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala m'chikondi chao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 15:10
28 Mawu Ofanana  

Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga.


Pakuti anaumirira Yehova osapatuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.


Ndipo Mose ndi Aroni anachita monga Yehova anawalamulira, momwemo anachita.


Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhale wopanduka ngakhale kubwerera m'mbuyo.


Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha. Ndili nayo mphamvu yakuutaya, ndi mphamvu ndili nayo yakuutenganso; lamulo ili ndinalandira kwa Atate wanga.


Pakuti sindinalankhule mwa Ine ndekha; koma Atate wondituma Ine, yemweyu anandipatsa Ine lamulo, limene ndikanene, ndi limene ndikalankhule.


Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.


Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndi kuti ndichita monga momwe Atate wandilamula. Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.


Ine ndalemekeza Inu padziko lapansi, m'mene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.


Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.


Ndipo wondituma Ine ali ndi Ine; sanandisiye Iye pa ndekha; chifukwa ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthawi zonse.


ndipo inu simunamdziwe Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.


Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.


Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.


Pakuti mkulu wa ansembe wotere anatiyenera ife, woyera mtima, wopanda choipa, wosadetsedwa, wosiyana ndi ochimwa, wakukhala wopitirira miyamba;


Pakuti pakadakhala bwino kwa iwo akadakhala osazindikira njira ya chilungamo, ndi poizindikira, kubwerera kutaya lamulo lopatulika lopatsidwa kwa iwo.


Ndipo umo tizindikira kuti tamzindikira Iye, ngati tisunga malamulo ake.


koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;


iye wakunena kuti akhala mwa Iye, ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.


Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa