Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 19:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Yesu adamuyankha kuti, “Bwanji ukundifunsa za chimene chili chabwino? Wabwino ndi Mmodzi yekha. Ngati ufuna kukaloŵa ku moyo, uzimvera Malamulo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 19:17
14 Mawu Ofanana  

ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.


Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu.


Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.


Pakuti Mose walemba kuti munthu amene achita chilungamo cha m'lamulo, adzakhala nacho ndi moyo.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.


Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa