Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 7:2 - Buku Lopatulika

2 Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo; ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Utsate malamulo anga, ndipo udzakhala ndi moyo. Usamale malangizo anga monga umachitira ndi maso ako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Utsate malamulo anga ndipo udzakhala ndi moyo; samala malangizo angawa monga uchitira ndi maso ako.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 7:2
16 Mawu Ofanana  

Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.


Ndisungeni monga kamwana ka m'diso, ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,


Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.


Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako.


Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Koma Yeremiya anati, Sadzakuperekani. Mveranitu mau a Yehova, amene ndinena ndi inu, chomwecho kudzakomera inu, ndipo moyo wanu udzakhalabe.


Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Anampeza m'dziko la mabwinja, m'chipululu cholira chopanda kanthu; anamzinga, anamlangiza, anamsunga ngati kamwana ka m'diso.


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa