Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Yohane 1:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo chikondi ndi ichi, kuti tiyende monga mwa malamulo ake. Ili ndi lamulolo, monga mudalimva kuyambira pachiyambi, kuti mukayende momwemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Chikondi chimene ndikunenachi nchakuti tikhale omvera malamulo a Mulungu. Lamulo limene ndikukulemberanilo, monga mudamva kuyambira pa chiyambi, ndi lakuti moyo wanu uzikhala wachikondi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo chikondi ndiye kuyenda momvera malamulo ake. Lamulo lake ndi lakuti mukhale moyo wachikondi monga munamva kuyambira pachiyambi.

Onani mutuwo Koperani




2 Yohane 1:6
14 Mawu Ofanana  

Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga.


Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo Ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsa ndekha kwa iye.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m'chikondi changa; monga Ine ndasunga malamulo a Atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi chake.


Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulani inu.


Muziyenda kutsata Yehova Mulungu wanu, ndi kumuopa, ndi kusunga malamulo ake, ndi kumvera mau ake, ndi kumtumikira Iye, ndi kummamatira.


Koma inu, chimene munachimva kuyambira pachiyambi chikhale mwa inu. Ngati chikhala mwa inu chimene mudachimva kuyambira pachiyambi, inunso mudzakhalabe mwa Mwana, ndi mwa Atate.


koma iye amene akasunga mau ake, mwa iyeyu zedi chikondi cha Mulungu chathedwa. M'menemo tizindikira kuti tili mwa Iye;


Okondedwa, sindikulemberani lamulo latsopano, komatu lamulo lakale limene munali nalo kuyambira pa chiyambi; lamulo lakalelo ndilo mau amene mudawamva.


ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.


Pakuti ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake: ndipo malamulo ake sali olemetsa.


Ndipo tsopano ndikupemphani, mkazi womveka inu, wosati monga kukulemberani lamulo latsopano, koma lomwelo tinali nalo kuyambira pachiyambi, kuti tikondane wina ndi mnzake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa