Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Yohane 1:7 - Buku Lopatulika

7 Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Paja pakuwoneka anthu ambiri onyenga pa dziko lapansi. Iwo savomereza kuti Yesu Khristu adadzakhaladi munthu. Munthu wosavomereza zimenezi ndi wonyenga, ndiponso woukira Khristu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndikunena zimenezi chifukwa anthu ambiri onyenga, amene savomereza kuti Yesu Khristu anabwera monga munthu, akuyenda mʼdziko lapansi. Munthu aliyense otere ndi wonyenga ndiponso wokana Khristu.

Onani mutuwo Koperani




2 Yohane 1:7
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


Izi ndakulemberani za iwo akusokeretsa inu.


Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.


Ndipo chisokeretsa iwo akukhala padziko ndi zizindikiro zimene anachipatsa mphamvu yakuzichita pamaso pa chilombo, ndi kunena kwa iwo akukhala padziko, kuti apange fano la chilombocho, chimene chinali nalo bala la lupanga ndi kukhalanso ndi moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa