Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 19:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Zonse adazilankhula Yehova tidzazichita. Ndipo Mose anabwera nao mau a anthu kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 19:8
9 Mawu Ofanana  

amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;


Ndipo anati kwa Mose, Mulankhule nafe ndinu, ndipo tidzamva; koma asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.


Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi maweruzo onse; ndipo anthu onse anavomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzachita.


Ndipo anatenga buku la Chipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.


Ndipo anthuwo anakhulupirira; ndipo pamene anamva kuti Yehova adawazonda ana a Israele, ndi kuti adaona mazunzo ao, anawerama, nalambira Mulungu.


Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Iaitu, koma tidzatumikira Yehova.


Ndipo anthu anati kwa Yoswa, Tidzamtumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera mau ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa