Mateyu 5:19 - Buku Lopatulika19 Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. Onani mutuwo |