Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:18 - Buku Lopatulika

18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:18
82 Mawu Ofanana  

Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:


Achirikizika kunthawi za nthawi, achitika m'choonadi ndi chilunjiko.


Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha.


Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.


Ndine amene ndilimbitsa mau a mtumiki wanga, kuchita uphungu wa amithenga anga; ndi kunena za Yerusalemu, Adzakhalamo anthu; ndi za mizinda ya Yuda; Idzamangidwa; ndipo ndidzautsa malo abwinja ake.


Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.


Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.


Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.


Ndipo aliyense amene adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.


Indetu ndinena kwa inu, Sanauke wakubadwa mwa mkazi munthu wamkulu woposa Yohane Mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu Ufumu wa Kumwamba amkulira iye.


Pakuti indetu ndinena kwa inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziona, koma sanazione; ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimve.


Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa Munthu atadza mu ufumu wake.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga padziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula padziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.


nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.


Ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, Indetu ndinena kwa inu, kuti munthu mwini chuma adzalowa movutika mu Ufumu wa Kumwamba.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti inu amene munanditsata Ine, m'kubadwanso, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iwiri, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Ndani wa awiriwo anachita chifuniro cha atate wake? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.


Indetu ndinena kwa inu, Zinthu zonse izi zidzafika pa mbadwo uwu wamakono.


Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.


Indetu, ndinena kwa inu, kuti adzamkhazika iye woyang'anira zinthu zake zonse.


Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziwani.


Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandichitira ichi Ine.


Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundichitira ichi Ine.


Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko.


Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.


Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeze chikhulupiriro chotere.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Palibe munthu anasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena amai, kapena atate, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwinowo,


Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho.


Ndipo anaitana ophunzira ake, nati kwa iwo, Ndithu ndinena ndi inu, Mkazi wamasiye amene waumphawi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo:


Indetu ndinena ndi inu, Mbadwo uno sudzapita kufikira zinthu izi zonse zitachitika.


Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.


Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.


Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.


Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.


Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;


Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.


Ndipo anausitsa moyo m'mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!


Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.


Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m'dzina langa chifukwa muli ake a Khristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.


kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.


Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.


Onani nyumba yanu isiyidwa kwa inu yabwinja; ndipo ndinena kwa inu kuti, Simudzandiona Ine, kufikira mudzati, Wolemekezeka Iye amene akudza m'dzina la Ambuye.


Kuti thambo ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali.


Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.


Koma anati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Palibe munthu wasiya nyumba, kapena mkazi, kapena abale, kapena akum'bala, kapena ana, chifukwa cha Ufumu wa Mulungu,


Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine mu Paradaiso.


Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.


Ndipo ananena naye, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mudzaona thambo lotseguka, ndi angelo a Mulungu akwera natsikira pa Mwana wa Munthu.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wosalowa m'khola la nkhosa pakhomo, koma akwerera kwina, iyeyu ndiye wakuba ndi wolanda.


Chifukwa chake Yesu ananenanso nao, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ine ndine khomo la nkhosa.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati mbeu ya tirigu siigwa m'nthaka, nifa, ikhala pa yokha iyo; koma ngati ifa, ibala chipatso chambiri.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake; kapena mtumwi sali wamkulu ndi womtuma iye.


Yesu anayankha, Moyo wako kodi udzautaya chifukwa cha Ine? Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Asanalire tambala udzandikana Ine katatu.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, ntchito zimene ndichita Ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi; chifukwa ndipita Ine kwa Atate.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni inu, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.


Ndipo tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m'dzina langa.


Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, pamene unali mnyamata unadzimangira wekha m'chuuno, ndipo unayenda kumene unafuna; koma pamene udzakalamba udzatulutsa manja ako, ndipo adzakumanga wina, nadzakunyamula kumene sufuna.


Indetu, indetu, ndinena kwa iwe, Tilankhula chimene tichidziwa, ndipo tichita umboni za chimene tachiona; ndipo umboni wathu simuulandira.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Pamenepo Yesu anayankha nati kwa iwo, Indetu, indetu ndinena kwa inu, sangathe Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.


Yesu anayankha iwo nati, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Mundifuna Ine, si chifukwa munaona zizindikiro, koma chifukwa munadya mkate, nimunakhuta.


Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Si Mose amene anakupatsani inu mkate wa Kumwamba; koma Atate wanga akupatsani inu mkate woona wa Kumwamba.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wokhulupirira ali nao moyo wosatha.


Chifukwa chake Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha.


Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa tchimolo.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Munthu akasunga mau anga, sadzaona imfa nthawi yonse.


Yesu anati kwa iwo, Indetu, indetu, ndinena kwa inu, asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndilipo.


koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa