Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 5:20 - Buku Lopatulika

20 Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti ngati kukhulupirika kwanu sikuposa kukhulupirika kwa aphunzitsi a Malamulo ndi kwa Afarisi, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 5:20
24 Mawu Ofanana  

Pomwepo anadziwitsa kuti sanawauze kupeza chotupitsa cha mikate, koma chiphunzitso cha Afarisi ndi Asaduki.


Ndipo amene adzalandira kamwana kamodzi kotereka chifukwa cha dzina langa, alandira Ine;


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.


Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Nkwa pafupi kuti ngamira ipyole diso la singano kuposa kuti mwini chuma alowe mu Ufumu wa Mulungu.


Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.


Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo.


Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.


Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri.


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


ndi kupezedwa mwa Iye, wosati wakukhala nacho chilungamo changa cha m'lamulo, koma chimene cha mwa chikhulupiriro cha Khristu, chilungamocho chochokera mwa Mulungu ndi chikhulupiriro;


Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa