Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi.
Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.
Yehova akhalira wabwino omlindirira, ndi moyo womfunafuna. Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.
Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse. Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.
Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.
Ndi mtendere ndidzagona pansi, pomwepo ndidzagona tulo; chifukwa Inu, Yehova, mundikhalitsa ine, ndikhale bwino.
Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.
Ndipo Iye anati, Tuluka, nuime paphiri lino pamaso pa Yehova. Ndipo taonani, Yehova anapitapo, ndi mphepo yaikulu ndi yamphamvu inang'amba mapiri, niphwanya matanthwe pamaso pa Yehova; koma Yehova sanakhale m'mphepomo. Itapita mphepoyo kunali chivomezi; komanso Yehova sanali m'chivomezicho. Chitaleka chivomezi panali moto; koma Yehova sanali m'motomo. Utaleka moto panali bata la kamphepo kayaziyazi.
Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake. Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali m'tseri, ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe.
Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.
Pakuti inu mudzatuluka ndi kukondwa, ndi kutsogozedwa ndi mtendere; mapiri ndi zitunda, zidzaimba zolimba pamaso panu, ndi mitengo yonse ya m'thengo idzaomba m'manja mwao.
pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
Mundidziwitse njira zanu, Yehova; Mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m'choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.
Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Otsata zachiwembu andiyandikira; akhala kutali ndi chilamulo chanu. Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha. Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukane nazo mboni zanu. Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu. Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu.
Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.
Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka padziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.
pakuti Mulungu sali Mulungu wa chisokonezo koma wa mtendere; monga mwa Mipingo yonse ya oyera mtima.
Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Asanduliza namondwe akhale bata, kotero kuti mafunde ake atonthole. nawasokolotsa kumaiko, kuchokera kum'mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kunyanja. Pamenepo akondwera, popeza pagwa bata; ndipo Iye awatsogolera kudooko afunako.
Pakuti Iye ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti onse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati,
Ndipo Ambuye wa mtendere yekha atipatse ife mtendere nthawi zonse, monsemo. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu. Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?
Inu ndinu mobisalira mwanga; m'nsautso mudzandisunga; mudzandizinga ndi nyimbo za chipulumutso.
Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake; koma asabwererenso kuchita zopusa.
Wodala munthu amene mumlanga, Yehova; ndi kumphunzitsa m'chilamulo chanu; kuti mumpumitse masiku oipa; kufikira atakumbira woipa mbuna.
Ndipo ndinati, Ha, wina akadandipatsa mapiko onga a njiwa! Mwenzi nditauluka, ndi kukhaliratu.
Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, Limbani, musaope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.
Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake. Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.
Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Pakuti Yehova watonthoza mtima wa Ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja; ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edeni, ndi malo ake ouma ngati munda wa Yehova; kukondwa ndi kusangalala kudzapezedwa m'menemo, mayamikiro, ndi mau a nyimbo yokoma.
Mutonthoze, mutonthoze mtima wa anthu anga, ati Mulungu wanu. Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye. Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa. Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo? Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lake, ndi kumphunzitsa Iye? Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya chiweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha? Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono. Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza. Amitundu onse ali chabe pamaso pa Iye; awayesa ngati chinthu chachabe, ndi chopanda pake. Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi chithunzithunzi chotani? Fano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golide analikuta ndi golide, naliyengera maunyolo asiliva. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.
Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu. Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
Kodi mpheta ziwiri sizigulidwa kakobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu: Filipo, ndi Bartolomeo; Tomasi, ndi Mateyu wamsonkho yo; Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa. Chifukwa chake musamaopa; inu mupambana mpheta zambiri.
Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Pamene ndinati, Literereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza. Pondichulukira zolingalira zanga m'kati mwanga, zotonthoza zanu zikondweretsa moyo wanga.
Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.
Ndipo Yehova, Iye ndiye amene akutsogolera; Iye adzakhala ndi iwe, Iye sadzakusowa kapena kukusiya; usamachita mantha, usamatenga nkhawa.
Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.
Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima mu Yerusalemu.
Imbani inu, m'mwamba, nukondwere iwe dziko lapansi, imbani inu mapiri, pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, nadzachitira chifundo ovutidwa ake.
ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
Usaope, Yakobo, nyongolotsi iwe, ndi anthu inu a Israele; ndidzakuthangata iwe, ati Yehova, ndiye Mombolo wako, Woyera wa Israele.
Popeza tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro, tikhala ndi mtendere ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu;
Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu aike moyo wao ndi kuchita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;
Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.
Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka.
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.
ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Kunena za Mulungu, njira yake ili yangwiro; mau a Yehova anayesedwa; Iye ndiye chikopa kwa onse akukhulupirira Iye.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
Mulungu ndiye wangwiro m'njira zake; mau a Yehova ngoyengeka; ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.
Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.
Inde m'njira ya maweruziro anu, Yehova, ife talindira Inu; moyo wathu ukhumba dzina lanu, ndi chikumbukiro chanu. Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali padziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.
Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
Ndipo chimene chilichonse mukafunse m'dzina langa, ndidzachichita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzachita.
Yehova anaonekera kwa ine kale, ndi kuti, Inde, ndakukonda iwe ndi chikondi chosatha; chifukwa chake ndakukoka iwe ndi kukukomera mtima.
amene tili naye chokhazikika mtima ndi chiyandiko cholimbika, mwa chikhulupiriro cha pa Iye.
Musakumbukire zidapitazo, ngakhale kulingalira zinthu zakale. Taonani, Ine ndidzachita chinthu chatsopano; tsopano chidzaoneka; kodi simudzachidziwa? Ndidzakonzadi njira m'chipululu, ndi mitsinje m'zidalala.
Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.
koma monga kulembedwa, Zimene diso silinazione, ndi khutu silinazimve, nisizinalowe mu mtima wa munthu, zimene zilizonse Mulungu anakonzereratu iwo akumkonda Iye.
Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Chigwa chilichonse chidzadzazidwa, ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zidzachepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala; ndipo ulemerero wa Yehova udzavumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena chomwecho.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:
Mudzandidziwitsa njira ya moyo, pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
ndipo makutu ako adzamva mau kumbuyo kwa iwe akuti, Njira ndi iyi, yendani inu m'menemo: potembenukira inu kulamanja, ndi potembenukira kulamanzere.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Ngati mukhala mwa Ine, ndi mau anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.
Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.
Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.
Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?
Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi. Umo tidzazindikira kuti tili ochokera m'choonadi, ndipo tidzakhazikitsa mtima wathu pamaso pake,
Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika. Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi.