Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Marko 6:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Yesu adaŵauza kuti, “Tiyeni tipite kwatokha kumalo kosapitapita anthu, kuti mukapumule pang'ono.” Adaatero chifukwa anthu anali piringupiringu, mwakuti iwo sankatha kupeza ndi mpata wodyera womwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 6:31
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Yesu pakumva, anachokera kumeneko m'ngalawa, kunka kumalo achipululu pa yekha; ndipo makamu, pamene anamva, anamtsata Iye mumtunda kuchokera m'midzi.


Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.


Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya.


Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya,


Zitapita izi anachoka Yesu kunka kutsidya lija la nyanja ya Galileya, ndiyo ya Tiberiasi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa