Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 131:2 - Buku Lopatulika

2 Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 131:2
16 Mawu Ofanana  

Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu, pakuti ndidzamyamikanso chifukwa cha chipulumutso cha nkhope yake.


Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzamyamikanso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga, ndi Mulungu wanga.


Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.


Pakuti atero Ambuye, Yehova Woyera wa Israele, M'kubwera ndi m'kupuma inu mudzapulumutsidwa; m'kukhala chete ndi m'kukhulupirira mudzakhala mphamvu yanu; ndipo simunafune.


Nkokoma kuti munthu ayembekeze ndi kulindirira modekha chipulumutso cha Yehova.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Mudzakhala nao moyo wanu m'chipiriro.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa