Masalimo 131 - Buku LopatulikaKudzichepetsa kwa Davide pakupemphera Nyimbo yokwerera; ya Davide. 1 Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa. 2 Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa. 3 Israele, uyembekezere Yehova, kuyambira tsopano kufikira kosatha. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi