M'mawu a Mulungu, timawerenga momwe Iye amatilimbikitsira kuthandiza osauka ndi kusamalira ofooka. Mtima wake umagunda chifukwa cha osowa, ndipo akutiuza kuti tichitepo kanthu powateteza!
Tili anthu a Mulungu, tiyenera kukumbukira kuti malemba ndi chisonyezero cha nzeru, chilango, ndi chikondi chosatha cha Mulungu, ndipo mmenemo Ambuye amalankhula nafe tonse kuti titonthoze ndikuthandiza osauka ndi osoŵa a dziko lino.
M’buku la Miyambo 3:27-28 (Buku Lopatulika) limati: “Usakana kuchitira zabwino munthu woyenera, pamene uli ndi mphamvu yochitira zimenezo. Usanene ndi mnzako, Pita, nubwerenso, ndipo mawa ndidzakupatsa, pamene uli nazo tsopano.” Kuyambira m’chipangano chakale mpaka chatsopano, tikuona chikhumbo cha Mulungu kuti ana ake achitire chifundo osauka ndi osoŵa.
Yesu anati osauka adzakhala nafe nthawi zonse, anatinso amene achitira chifundo osauka, odwala, ndi osoŵa, kwenikweni amatumikira Yesu mwiniwake (Mateyu 25:35-40) ndipo chifukwa chake, adzalandira mphotho.
Ndikukulangiza pano, kuti usakane kuchita zabwino, khalani chitoliro cha madalitso kwa onse omwe alibe chiyembekezo ndikusiya chizindikiro chosatha cha chikondi m'derali lomwe lawonongeka ndi chidani ndi kusayanjanitšana.
Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu.
Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa?
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe. Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka.
Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.
Yesu adayang'ana ophunzira ake, naŵauza kuti, “Ndinu odala, inu osaukanu, Ufumu wa Mulungu ndi wanu.
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.
Za munthu wotere paja Malembo akuti, “Wapereka mphatso zake moolowa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake nchamuyaya.”
Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?
Iye adati, “Amene ali ndi miinjiro iŵiri, apatseko mnzake amene alibe. Ndipo amene ali nacho chakudya, achitenso chimodzimodzi.”
Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.
Koma iwe ukamakonza phwando, uziitana amphaŵi, otsimphina, opunduka ndi akhungu.
Apo udzakhala wodala, chifukwa iwo alibe kanthu koti nkukubwezera. Mulungu ndiye adzakubwezera, pamene anthu olungama adzauka kwa akufa.”
“Kodi bwanji mafuta ameneŵa sadaŵagulitse ndalama mazana atatu kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?”
Ndipo ndikudziŵa kuti zimene amandilamula nzolinga ku moyo wosatha. Nchifukwa chake zimene ndimalankhula, ndimalankhula monga momwe Atate amandiwuzira.”
Adaatero osati chifukwa chodera nkhaŵa osaukawo, koma chifukwa anali mbala. Iye ankasunga thumba la ndalama, nkumabamo.
Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo.
Ndipo ngakhale nditagaŵira amphaŵi chuma changa chonse, kapena kupereka thupi langa kuti anthu alitenthe, koma ngati ndilibe chikondi, ndiye kuti changa palibe.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima.
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?
Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.
Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha.
“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.
Chuma cha munthu wolemera ndiye chitetezo chake, koma umphaŵi wa anthu osauka ndiye chiwonongeko chao.
Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza.
Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi.
Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge.
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.
Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,
kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.
Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.
Akhungu akupenya ndipo opunduka miyendo akuyenda; akhate akuchira ndipo agonthi akumva; akufa akuukitsidwa ndipo amphaŵi akumva Uthenga Wabwino.
Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Amene amalalatira mmphaŵi, amanyoza Mlengi wake. Amene amakondwerera tsoka la mnzake adzalangidwa.
Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”
Munthu akakupempha kanthu, uzimpatsa. Ndipo munthu akafuna kubwereka kanthu kwa iwe, usamkanize.”
Ndazindikira kuti zabwino zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe konse malire.
Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu.
Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.
Ukamaona anthu osauka akuzunzika m'dziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzao ndi kuŵalanda ufulu wao mwankhanza, usadabwe nazo zimenezo. Paja woyang'anira wokulapo ali naye wina wamkulu kwambiri amene amamuyang'anira. Ndipo palinso akuluakulu enanso oyang'anira iwowo.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse.
Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’
Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse.
Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake.
“Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda.
Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa.
Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’
Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri.
Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’
“Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga.
Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’
Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’
Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi.
Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’
Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”
Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.
Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
Pakati pa abale anu pakakhala wina wosauka m'midzi yanu, m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, musadzaume mtima, ndipo musadzaume manja.
Makamaka muzidzamchitira chifundo ndi kumkongoza monga momwe angafunire.
Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani.
Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira.
Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima.
Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye.
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi.
Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake.
Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza,
Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu.
dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.
Antchito okolola m'minda mwanu simudaŵalipire. Ndalama zamalipirozo zikulira mokutsutsani. Ndipo kufuula kwa okololawo kwamveka m'makutu a Chauta Mphambe.
“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri, musandimane zimenezo ndisanafe:
Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera,
kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka.
Chauta, mumamva zimene odzichepetsa amapempha. Mudzalimbitsa mitima yao, mudzaŵatchera khutu.
Potero mudzaŵateteza amasiye ndi opsinjidwa, kuti anthu amene ali a pansi pano, asadzathe kuwopsezanso.
Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.
Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo.
Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa.
Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu.
Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.
Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse.
Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake.
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.
Munthu wolemera amadziyesa wanzeru, koma munthu wosauka amene ali womvetsa zinthu, amamtulukira.
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba.
Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Kuyambira ubwana wanga mpaka kukula, ndakhala ndikupirira zilango zanu pozunzika mpaka pafupi kufa, tsopano ndatheratu.
“Ndidzadalitsa kwambiri mzinda wa Ziyoni poupatsa zosoŵa zake, anthu ake osauka, ndidzaŵapatsa chakudya chokwanira.
Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.
“Uziyanjana msanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo lamilandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende.
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m'kamwa mwanga, ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri.
Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.
Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.
Aŵiriwo akagwa, wina adzautsa mnzake. Koma tsoka amene ali yekha: akagwa, ndiye kuti zavuta, chifukwa palibe wina womuutsa.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Uziŵachitira ulemu azimai amasiye, amenetu ali amasiye enieni.
Koma ngati mai wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wao pa banja lao moopa Mulungu, kuti pakutero abwezere makolo ao zimene adalandira kwa iwo. Pakuti zimenezi Mulungu amakondwera nazo akamaziwona.
Mai amene ali wamasiye kwenikweni, wopanda wina aliyense womsamala, ameneyo waika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimthandiza.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake, ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa.
Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake.
Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.
Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.
Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
Koma anthu osoŵa adaŵatulutsa m'mavuto ao, adachulukitsa mabanja ao ngati magulu a nkhosa.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.
Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?
kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.
Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu.
Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera.
Ndidzasangalala ndi mtima wonse ndi kunena kuti. “Ndani angafanefane ndi Inu Chauta, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka kwa munthu wopambana pa mphamvu, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa kwa munthu wolanda zinthu zake?”
Paja Chauta amaimirira pafupi ndi munthu wosoŵa, amafuna kumpulumutsa kwa anthu ogamula kuti iyeyo aphedwe.
Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.
Paja Chauta amakondwera ndi anthu ake, amaŵalemekeza anthu odzichepetsa poŵagonjetsera adani ao.
Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.
Zitapita zaka zimenezo, padzakhalanso zaka zisanu ndi ziŵiri za njala, ndipo zaka zonse zija za dzinthu zidzaiŵalika mu Ejipito monse. Njalayo idzaononga dziko.
Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.
“Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.”
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha.
Ankakonda kutemberera, choncho matemberero amgwere. Sadakonde kudalitsa anthu ena, choncho madalitso akhale kutali ndi iye.
mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”
“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba.
“Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao.
Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.
Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.
Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.
M'tsala la munthu wosauka mumalola chakudya chambiri, koma anthu opanda chilungamo amalanda chakudyacho.
Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa.
Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale.
Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi.
Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.
Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.”
“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa.
Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi.
Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake.
Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.
Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu?
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Chauta adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili m'menemo. Amasunga malonjezo ake nthaŵi zonse.
Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.
Nkwabwino kukhala m'chilungamo ndi kusauka, kupambana kukhala nazo zokoma zambiri zimene munthu woipa ali nazo.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.
Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga.
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.
Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu.
Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”