Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho. Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi. Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.
Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.
“Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano. Mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu, Mulungu adatipatsa Mzimu Woyerayo moolowa manja. Adachita zimenezi, kuti mwa kukoma mtima kwake tisanduke olungama pamaso pake, ndipo tikalandire moyo wosatha umene tikuuyembekeza.
Machimo anu adakulekanitsani ndi Mulungu wanu, ndipo Iye wakufulatirani chifukwa cha machimo anuwo. Choncho saamva zimene inu mumanena.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.
Nthaŵi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziŵe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziŵa, Ndidzaŵakhululukira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta.
Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu.
“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Ngati ndife osakhulupirika, Iye amakhalabe wokhulupirika, pakuti sangathe kudzitsutsa.”
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Momwemonso inuyo mudziwone ochita ngati kufa nkulekana ndi uchimo, koma okhala ndi moyo wotumikira Mulungu, mogwirizana ndi Khristu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Inu amene mumakhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu, ndakulemberani zimenezi kuti mudziŵe kuti muli ndi moyo wosatha.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira. Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.